Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 15

“Ndidzathetsa Uhule Wako”

“Ndidzathetsa Uhule Wako”

EZEKIELI 16:41

MFUNDO YAIKULU: Zimene tikuphunzira zokhudza mahule amene anafotokozedwa m’buku la Ezekieli komanso la Chivumbulutso

1, 2. Kodi ndi hule lotani limene tikhoza kunyansidwa nalo kwambiri?

 ZIMAKHALA zomvetsa chisoni tikaona munthu atayamba uhule. Timadzifunsa kuti, N’chiyani chinapangitsa kuti ayambe khalidwe loipa limeneli? Kodi anayamba uhule chifukwa chakuti ali wamng’ono ankazunzidwa komanso kuchitidwa nkhanza ndi anthu am’banja lake? Kodi umphawi wadzaoneni ndi umene unapangitsa kuti akhale kapolo wa khalidwe loipali? Kapena kodi ankathawa nkhanza za m’banja? Nkhani zomvetsa chisoni ngati zimenezi zimachitika kawirikawiri m’dziko loipali. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yesu Khristu anachitira chifundo mahule ena. Iye ananena motsimikiza kuti anthu amene akanalapa n’kusintha moyo wawo akanatha kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wabwino.​—Mat. 21:28-32; Luka 7:36-50.

2 Koma tiyeni tiganizire mtundu wina wa uhule. Yerekezerani za mkazi amene wasankha dala kuti akhale hule. Iye sakuona kuti khalidweli ndi loipa koma akuona kuti ndi losangalatsa. Iye akungofuna kupeza ndalama komanso kutchuka. Koma bwanji ngati mkaziyo anali ndi mwamuna wabwino komanso wokhulupirika koma anamusiya mwadala n’kukayamba uhule? Mkazi wotereyu tikhoza kunyansidwa naye komanso kunyansidwa ndi khalidwe lake loipalo. Mmene tikumvera tikaganizira za mkaziyu ndi chifukwa chachikulu chimene chimapangitsa Yehova mobwerezabwereza kugwiritsa ntchito mawu akuti hule pofuna kusonyeza mmene amamvera ndi zipembedzo zabodza.

3. Kodi tikambirana nkhani zotani m’mutuwu?

3 M’buku la Ezekieli muli nkhani ziwiri zimene zagwiritsa ntchito chitsanzo cha hule pofotokoza kusakhulupirika kwa anthu a Mulungu ku Isiraeli ndi ku Yuda. (Ezekieli chaputala 16 ndi 23) Koma tisanakambirane nkhani zimenezi mwatsatanetsatane, tiyeni tikambirane za hule lina lophiphiritsa. Hule limeneli linayamba uhule kale kwambiri Ezekieli asanakhaleko komanso Aisiraeli asanakhaleko ndipo akupitirizabe khalidwe limeneli. Huleli linatchulidwa m’buku la Chivumbulutso lomwe ndi lomalizira m’Baibulo.

“Mayi wa Mahule”

4, 5. Kodi “Babulo Wamkulu” ndi ndani, nanga tikudziwa bwanji zimenezi? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 M’masomphenya amene Yesu anaonetsa mtumwi Yohane chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, panaoneka chinthu china chodabwitsa. Chinthu chimenechi chikutchedwa “hule lalikulu” kapena kuti “Babulo Wamkulu, mayi wa mahule.” (Chiv. 17:1, 5) Kwa zaka zambiri, atsogoleri azipembedzo komanso akatswiri a Baibulo, sankadziwa kuti huleli ndi ndani. Anthu osiyanasiyana amatanthauzira hule limeneli mosiyanasiyananso. Ena amanena kuti akuimira Babulo, ena amati akuimira Roma, pomwe ena amati akuimira Tchalitchi cha Katolika. Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehovafe tamvetsa zimene kwenikweni “hule lalikulu” limeneli limaimira. Tikudziwa kuti limaimira zipembedzo zonse zabodza. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

5 Hule limeneli lili ndi mlandu chifukwa limachita chiwerewere ndi “mafumu a dziko lapansi” kapena kuti andale. Choncho n’zoonekeratu kuti huleli silikuimira andale. Kuwonjezera pamenepo buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti “amalonda apadziko lapansi,” adzalira Babulo Wamkulu akadzawonongedwa. Choncho Babulo Wamkulu sakuimira amalonda. Ndiye kodi Babuloyu ndi ndani? Huleli lili ndi mlandu chifukwa limachita “zamizimu,” kulambira mafano komanso kuchita zachinyengo. Kodi zimenezi si zimenenso zipembedzo za m’dzikoli zimachita? Onani kuti huleli likufotokozedwa kuti lakwera kapena kuti lili ndi mphamvu pa olamulira andale a m’dzikoli. Hule limeneli limazunzanso atumiki okhulupirika a Yehova Mulungu. (Chiv. 17:2, 3; 18:11, 23, 24) Kodi zimenezi sizikugwirizana ndendende ndi zimene zipembedzo zabodza zakhala zikuchita kuyambira kalekale mpaka pano?

Mumzinda wa Babele umene pambuyo pake unkatchulidwa kuti Babulo munali mabungwe, ziphunzitso komanso zochitika zosiyanasiyana zokhudzana ndi kulambira kwabodza. (Onani ndime 6)

6. N’chifukwa chiyani timanena kuti Babulo Wamkulu “ndi mayi wa mahule”?

6 Koma kodi n’chifukwa chiyani Babulo Wamkulu samangotchedwa hule lalikulu, koma amatchedwanso kuti “mayi wa mahule”? M’chipembedzo chabodzachi muli mbali zosiyanasiyana. Muli mipingo komanso magulu osawerengeka. Kungoyambira pamene zilankhulo zinasokonezedwa ku Babele wakale kapena kuti ku Babulo, ziphunzitso zabodza zafalikira padziko lonse ndipo zimenezi zachititsa kuti payambike mipingo yambiri. Mpake kuti dzina lakuti “Babulo Wamkulu” linachokera ku mzinda wa Babulo komwe zipembedzo zabodza zinayambira. (Gen. 11:1-9) Choncho tinganene kuti zipembedzo zonsezi ndi “ana” a gulu limodzi lomwe ndi hule lalikulu. Kawirikawiri Satana amagwiritsira ntchito zipembedzo zimenezi kuti azikopa anthu kuti azichita zamizimu, azilambira mafano komanso kuti azichita miyambo imene silemekeza Mulungu. N’zosadabwitsa kuti anthu a Mulungu amachenjezedwa kuti azipewa zipembedzo zabodzazi zomwe zikupezeka padziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake.”​—Werengani Chivumbulutso 18:4, 5.

7. N’chifukwa chiyani timamvera chenjezo lakuti tituluke m’Babulo Wamkulu?

7 Kodi inuyo mwamvera chenjezo limeneli? Kumbukirani kuti ndi Yehova yemweyo amene analenga anthu kuti azitha kuzindikira “zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Munthu angakwaniritse zosowa zimenezi pokhapokha ngati akulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Atumiki a Yehova amayesetsa kupewa chilichonse chogwirizana ndi kulambira kwabodza. Koma Satana Mdyerekezi ali ndi cholinga chosiyana ndi chimenechi. Iye amakonda kukopa anthu a Mulungu kuti azichita nawo zinthu zokhudza kulambira kwabodza. Ndipo nthawi zambiri zimamuyendera. Pofika mu nthawi ya Ezekieli, anthu a Mulungu anali atagwera mumsampha umenewu kambirimbiri. Tingachite bwino kukambirana zimene zinawachitikirazi chifukwa zingatithandize kudziwa zimene Yehova amafuna, chilungamo chake ndiponso chifundo chake.

“Unakhala Hule”

8-10. Kodi ndi chinthu chofunika chiti pa kulambira koyera chimene chimatithandiza kuti tizimvetsa mmene Yehova amamvera pa nkhani ya kulambira kwabodza? Perekani chitsanzo.

8 M’buku la Ezekieli Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzo cha hule, pofuna kusonyeza mmene kusakhulupirika kwa anthu ake kunamukhudzira. Ezekieli anauziridwa kuti alembe nkhani ziwiri zomveka bwino zosonyeza mmene Yehova ankakhudzidwira ndi kusakhulupirika komanso makhalidwe oipa a anthu ake. Koma n’chifukwa chiyani anawayerekezera ndi mahule?

9 Kuti tipeze yankho lake, tikufunika kukumbukira chinthu chofunika kwambiri pa kulambira koyera chimene tinakambirana m’Mutu 5 wa buku lino. M’Chilamulo chimene anapereka kwa Aisiraeli Yehova ananena kuti: “Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine. [kapena kuti, “motsutsana ndi ine,” mawu am’munsi.]. . . . Ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha.” (Eks. 20:3, 5) Patapita nthawi, anabwerezanso mfundo ya choonadi imeneyi ponena kuti: “Musagwadire mulungu wina, chifukwa Yehova amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha. Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.” (Eks. 34:14) Apatu Yehova anafotokoza mfundo yofunika momveka bwino kwambiri. Mfundo yake ndi yakuti, sitingalambire Yehova movomerezeka pokhapokha ngati tikulambira iye yekha basi.

10 Tingayerekezere zimenezi ndi ukwati. Munthu amene ali pa banja amayembekezera kuti mkazi kapena mwamuna wake azikonda iye yekha basi. Ngati munthu mmodzi m’banjamo atayamba kukondana kapena kukopana ndi munthu wina, n’zomveka winayo kuchita nsanje komanso kuona kuti mnzakeyo ndi wosakhulupirika. (Werengani Aheberi 13:4.) Mofanana ndi zimenezi, pa nkhani yakulambira, Yehova amaona kuti anthu ake amene anadzipereka kwa iye, achita zinthu zosakhulupirika ngati atamusiya n’kuyamba kulambira milungu yabodza. Iye anasonyeza mwamphamvu mmene amamvera pa nkhani imeneyi mu Ezekieli chaputala 16.

11. Kodi Yehova anafotokoza chiyani zokhudza Yerusalemu ndi mmene anayambira?

11 M’chaputala 16 cha buku la Ezekieli muli mawu amene Yehova analankhula kwa nthawi yaitali m’buku lonseli. Mawu amenewa ndi amodzi mwa maulosi aatali kwambiri m’Malemba a Chiheberi. Yehova akufotokoza za mzinda wa Yerusalemu umene ukuimira anthu osakhulupirika afuko la Yuda. Akufotokoza nkhani yomvetsa chisoni ndi yochititsa mantha yokhudza zimene zinachitika mkazi wophiphiritsayu atangobadwa kumene komanso mmene anayambira khalidwe loipali. Atangobadwa anatayidwa ndipo panalibe womuthandiza kapena womusamalira. Makolo ake anali a Kanani am’dzikolo ndipo ankalambira milungu yabodza. Kwa nthawi yaitali, Yerusalemu ankalamuliridwa ndi a Yebusi omwe anali a Kanani, mpaka pamene Davide anagonjetsa mzindawo. Yehova anamvera chisoni mwana wotayidwayo ndipo anamutenga n’kumusambisa komanso kumupatsa zinthu zina zofunika. Patapita nthawi anakhala ngati mkazi wake. Ndipotu Aisiraeli amene pambuyo pake ankakhala mumzindawo anali atachita pangano ndi Yehova. Iwo anachita pangano limeneli mwakufuna kwawo m’nthawi ya Mose. (Eks. 24:7, 8) Mzinda wa Yerusalemu utakhala likulu la dzikolo, Yehova anadalitsa mzindawo n’kuukongoletsa mofanana ndi mmene mwamuna wolemera komanso wamphamvu angachitire ndi mkazi wake wokondedwa amene wamuveka zinthu zokongola.​—Ezek. 16:1-14.

Solomo analola kuti akazi ake omwe anali amitundu ina, amukakamize kulambira mafano zomwe zinaipitsa mzinda wa Yerusalemu (Onani ndime 12)

12. Kodi kulambira mafano kunayamba bwanji mu Yerusalemu?

12 Taonani zimene kenako zinachitika. Yehova ananena kuti: “Unayamba kudalira kukongola kwako ndipo unakhala hule chifukwa cha kutchuka kwako. Unayamba kuchita uhule mosadziletsa ndi munthu aliyense wodutsa mʼnjira ndipo unapereka kukongola kwako kwa anthu odutsawo.” (Ezek. 16:15) M’masiku a Solomo, Yehova anadalitsa kwambiri komanso kulemeretsa anthu ake moti mzinda wa Yerusalemu unali wokongola kwambiri ndipo unatchuka kwambiri pa nthawiyo. (1 Maf. 10:23, 27) Koma pang’ono ndi pang’ono anthu a mu Yerusalemu anakhala osakhulupirika ndipo anayamba kulambira mafano. Pofuna kusangalatsa akazi ake ambirimbiri a mitundu ina, Solomo anayamba kulambira milungu yabodza ndipo zimenezi zinadetsa Yerusalemu. (1 Maf. 11:1-8) Ndipo mafumu ena omwe anabwera pambuyo pake anachita zoipa kuposa pamenepa. Anadetsa dziko lonse polimbikitsa kulambira mafano. Kodi Yehova anamva bwanji chifukwa cha zochita zauhule komanso zosakhulupirika zimenezi? Iye anati: ‘Zinthu zimenezi siziyenera kuchitika ndipo zisadzachitikenso.’ (Ezek. 16:16) Koma anthu ake opandukawo anapitiriza kuchita zoipa.

Aisiraeli ena ankapereka nsembe ana awo kwa milungu yabodza ngati Moleki

13. Kodi anthu a Mulungu ku Yerusalemu anali ndi mlandu waukulu wochita zoipa zamtundu wanji?

13 Tangoganizani mmene Yehova zinkamupwetekera komanso mmene zinkamunyansira pamene ankafotokoza zinthu zoipa zimene anthu ake osankhidwa ankachita. Iye anati: “Unatenga ana ako aamuna ndi aakazi amene unandiberekera nʼkuwapereka nsembe kwa mafano. Kodi zochita zako zauhulezo sizinakukwanire? Unapha ana anga ndipo unawapereka nsembe powaponya pamoto.” (Ezek. 16:20, 21) Zinthu zonyansa zimene anthu a ku Yerusalemu ankachita, zikusonyezeratu kuti Satana ndi woipa kwambiri. Iye amasangalala kwambiri kusocheretsa anthu a Yehova kuti azichita zinthu zomupandukira. Koma Yehova amaona chilichonse. Mulungu angathetse zinthu zoipa zonse zimene Satana akuyambitsa ndipo adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.​—Werengani Yobu 34:24.

14. Pa chitsanzo chimene Yehova anapereka, kodi azichemwali ake awiri a Yerusalemu anali ndani ndipo ndi ndani amene anali woipa kwambiri pa atatuwa?

14 Koma Yerusalemu sananyansidwe ngakhale pang’ono ndi zinthu zoipa zimene ankachita. Anapitiriza kuchita uhule. Yehova ananena kuti iye ankachita khalidwe loipali mopanda manyazi kuposa mahule ena chifukwa iye ndi amene ankalipira anthu kuti achite nawo za uhulezo. (Ezek. 16:34) Mulungu ananena kuti Yerusalemu anali ngati ‘mayi ake’ kutanthauza mitundu ina imene pa nthawi ina inkalamulira dzikolo. (Ezek. 16:44, 45) Mchemwali wake wamkulu wa Yerusalemu anali Samariya amene ankachita kwambiri za uhule kuposa mng’ono wakeyu. Mulungu anatchulanso mchemwali wake wachiwiri dzina lake Sodomu. Apa Sodomu akumugwiritsa ntchito mophiphiritsa chifukwa panali patadutsa nthawi yaitali kuchokera pamene anawonongedwa chifukwa cha kusamvera komanso chifukwa cha makhalidwe oipa amene ankachitika kumeneko. Mfundo ya Yehova pamenepa inali yoti Yerusalemu anachita zinthu zoipa kwambiri kuposa azichemwali ake awiriwo, Samariya komanso Sodomu. (Ezek. 16:46-50) Anthu a Mulungu ananyalanyaza machenjezo amene ankapatsidwa mobwerezabwereza ndipo anapitiriza kupandukira Mulungu.

15. Pamene Yehova anapereka chilango pa Yerusalemu, kodi cholinga chake chinali chotani, nanga anapereka uthenga wotani wopatsa chiyembekezo?

15 Kodi Yehova akanachita chiyani? Iye anachenjeza Yerusalemu kuti: “Ine ndikusonkhanitsa pamodzi zibwenzi zako zonse zimene unkazisangalatsa” komanso kuti “Ndidzakupereka mʼmanja mwa anthu okuukira.” Anthu amene kale ankagwirizana ndi anthu a Mulunguwo adzawaukira n’kuwawononga ndipo adzawalanda zinthu zawo zamtengo wapatali zimene zinkachititsa kuti azioneka okongola. Iye anati: “Iwo adzakugenda ndi miyala ndipo adzakupha ndi malupanga awo.” N’chifukwa chiyani Yehova anapereka chilango chimenechi? Sikuti ankafuna kuwonongeratu anthu akewo. M’malomwake anafotokoza cholinga chake kuti: “Ndidzathetsa uhule wako.” Mulungu anawonjezera kuti: “Mkwiyo wanga ndidzauthetsera pa iwe moti sindidzakukwiyiranso. Ndidzangokhala osachita kalikonse ndipo sindidzakhalanso wokwiya.” Monga momwe tafotokozera m’Mutu 9 wa bukuli, cholinga chachikulu cha Yehova chinali kubwezeretsa anthu ake pambuyo pa ukapolo. Chifukwa chiyani? Iye anati: “Ine ndidzakumbukira pangano limene ndinapangana nawe uli wakhanda.” (Ezek. 16:37-42, 60) Mosiyana ndi anthu akewo, Yehova anasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwambiri.​—Werengani Chivumbulutso 15:4.

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani sitimanenanso kuti Ohola ndi Oholiba akuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu? (Onani bokosi lakuti “Atsikana Apachibale Omwe Anali Mahule.”) (b) Kodi tikuphunzira chiyani mu Ezekieli chaputala 16 ndi 23?

16 Mawu aatali komanso amphamvu amene Yehova analankhula omwe akupezeka mu Ezekieli chaputala 16, akutiphunzitsa mfundo zake zapamwamba kwambiri kuti iye ndi wachilungamo komanso wachifundo chachikulu. Zimenezi ndi zimene tikuzipezanso mu Ezekieli chaputala 23. Akhristu oona masiku ano amamvetsa uthenga wa Yehova wosapita m’mbali wokhudza uhule wa uzimu umene anthu akewo ankachita. Sitingafune kukwiyitsa Yehova ngati mmene Yuda ndi Yerusalemu anachitira. Choncho tiyenera kupeweratu kulambira mafano kwa mtundu uliwonse. Zimenezi zikuphatikizapo dyera komanso kukonda kwambiri chuma, komwe kuli ngati kulambira mafano. (Mat. 6:24; Akol. 3:5) Tiziyamikira kuti mwa chifundo chake Yehova wabwezeretsa kulambira koyera m’masiku otsiriza ano komanso kuti sadzalolanso kuti kulambira kumeneku kudetsedwe. Iye anachita pangano ndi Isiraeli wauzimu limene “lidzakhalepo mpaka kalekale,” pangano limene silidzaphwanyidwa chifukwa cha kusakhulupirika kapena uhule. (Ezek. 16:60) Choncho tiziyamikira kuti masiku ano tili ndi mwayi wokhala m’gulu la anthu a Yehova omwe ndi oyera.

17 Kodi zimene Yehova ananena zokhudza mahule ofotokozedwa m’buku la Ezekieli, zikutiphunzitsa chiyani zokhudza “hule lalikulu,” lomwe ndi Babulo Wamkulu? Tiyeni tione.

‘Sadzapezekanso’

18, 19. Kodi mahule awiri omwe atchulidwa m’buku la Ezekieli akufanana bwanji ndi hule lomwe latchulidwa m’buku la Chivumbulutso?

18 Yehova samasintha. (Yak. 1:17) Yehova sanasinthe mmene amaonera zipembedzo zabodza kapena kuti Babulo Wamkulu, kwa nthawi yonse imene zakhalapo. Choncho sitimadabwa tikaona kuti chiweruzo chimene chinaperekedwa kwa mahule otchulidwa m’buku la Ezekieli ndi chofanana ndi chiweruzo chimene chidzaperekedwe kwa “hule lalikulu” lotchulidwa m’buku la Chivumbulutso.

19 Mwachitsanzo, mungaone kuti chilango chimene mahule otchulidwa mu ulosi wa Ezekieli analandira sichinachokere kwa Yehova mwachindunji koma chinachokera kwa mitundu imene anthu a Mulungu osakhulupirika ankachita nayo chigololo chauzimu. Mofanana ndi zimenezi, zipembedzo zabodza zonse pamodzi zikuimbidwa mlandu wochita chigololo ndi “mafumu a dziko lapansi.” Koma kodi ndi ndani adzapereke chilango kwa huleli? Timawerenga m’Baibulo kuti maufumu andalewa ‘adzadana ndi hulelo. Adzatenga zinthu zake zonse nʼkulisiya lamaliseche ndipo adzadya minofu yake nʼkulipsereza ndi moto.’ N’chifukwa chiyani mafumu a dziko lapansi adzachite zinthu zodabwitsa ngati zimenezi? Adzachita zimenezi chifukwa Mulungu ‘adzaika pulani mʼmitima yawo kuti achite mogwirizana ndi maganizo ake.’​—Chiv. 17:1-3, 15-17.

20. N’chiyani chikusonyeza kuti chiweruzo chimene Babulo adzalandire chidzakhala chomaliza?

20 Choncho Yehova adzagwiritsa ntchito mafumu a dzikoli kuti apereke chiweruzo kwa zipembedzo zonse zabodza kuphatikizapo zipembedzo zonse zimene zimati ndi za Chikhristu. Chiweruzo chimenechi chidzakhala chomaliza, kutanthauza kuti zipembedzo zabodza sizidzakhululukidwa ndipo sizidzakhalanso ndi mwayi uliwonse woti zisinthe njira zake. Buku la Chivumbulutso limanena kuti Babulo ‘sadzapezekanso.’ (Chiv. 18:21) Angelo a Mulungu adzasangalala ndi kuwonongedwa kwake ndipo adzanena kuti: “Tamandani Ya! Utsi umene ukufuka chifukwa cha kuwotchedwa kwake udzafuka mpaka kalekale.” (Chiv. 19:3) Chiweruzo chimenechi chidzakhala chamuyaya, moti palibe chipembedzo chilichonse chabodza chimene chidzabwerenso n’kuyamba kuipitsa kulambira koyera. Babulo akadzalandira chiweruzo chamoto komanso kuwonongedwa, mophiphiritsa adzakhala ngati akutulutsa utsi umene udzafuke mpaka kalekale.

Mayiko omwe akhala akuyendera maganizo a Babulo Wamkulu adzamuukira n’kumuwononga (Onani ndime 19, 20)

21. Kodi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kudzakhala chiyambi cha chiyani, nanga kodi nthawi imeneyo idzatha bwanji?

21 Mafumu adzikoli akadzaukira Babulo Wamkulu, adzakhala akupereka chiweruzo cha Mulungu ndipo akadzachita zimenezi adzakhala akukwaniritsa mbali yaikulu ya cholinga cha Yehova. Chimenechi chidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu ndipo idzakhala nthawi imene padzikoli padzakhala mavuto amene sanachitikepo chiyambire. (Mat. 24:21) Chisautso chachikulu chidzafika pachimake pa nkhondo ya Aramagedo, yomwe ndi nkhondo ya Yehova yothetsa dziko loipali. (Chiv. 16:14, 16) Mogwirizana ndi zimene mitu yakutsogolo ya buku lino ikufotokoza, buku la Ezekieli likufotokoza zambiri za mmene chisautso chimenechi chidzakhalire. Koma pofika pano kodi ndi mfundo ziti zimene taziphunzira mu Ezekieli chaputala 16 ndi 23 zomwe tikufuna kuzikumbukira komanso kuzigwiritsira ntchito?

Maboma a dzikoli adzaukira Babulo Wamkulu popereka chilango chochokera kwa Mulungu (Onani ndime 21)

22, 23. Kodi kukambirana zokhudza mahule ofotokozedwa m’buku la Ezekieli komanso hule lofotokozedwa mu Chivumbulutso kungakhudze bwanji utumiki wathu wopatulika?

22 Satana amafuna kusokoneza anthu amene amalambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Palibe chimene chimamusangalatsa kwambiri kuposa kupeza mwayi wotipatutsa pa kulambira koyera komanso kutichititsa kuti tizichita makhalidwe ofanana ndi a mahule amene afotokozedwa m’buku la Ezekieli. Choncho tizikumbukira kuti Yehova safuna kuti tizipikisana naye komanso kuchita zinthu zosonyeza kusakhulupirika pa nkhani ya kulambira. (Num. 25:11) Timayesetsa kuti tizipewa chilichonse chokhudza kulambira kwa bodza, timapewa kukhudza “chinthu chilichonse chodetsedwa” m’maso mwa Mulungu. (Yes. 52:11) Zifukwa zimenezi ndi zimene zimatipangitsa kuti tizipewa kulowerera m’mikangano ya ndale komanso zidani zimene zimagawanitsa dzikoli. (Yoh. 15:19) Timaona kuti kukonda dziko lako ndi mbali ya chipembedzo chabodza imene Satana amalimbikitsa ndipo timapeweratu kuchita zimenezi.

23 Tikufunika tizikumbukira kuti tili ndi mwayi waukulu wolambira Yehova m’kachisi wake wauzimu, yemwe ndi woyera komanso wosaipitsidwa. Posonyeza kuti timayamikira njira imeneyi yakulambira, tikuyenera kuyesetsa kuti tisachite china chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chabodza komanso zochita zake za uhule.