Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Inu Abale Athu Okonda Yehova:

Anthu amene anapezeka pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Dzina la Mulungu” mu 1971 anasangalala kulandira mabuku atsopano angapo. Buku Lapachaka la 1972 linafotokoza kuti “palibe amene ankayembekezera kuti alandira mabuku amenewa.” Ponena za limodzi mwa mabuku atsopanowo, m’bale wina anati: “Sitinakhalepo ndi buku losangalatsa chonchi limene likutithandiza kuoneratu zinthu zam’tsogolo.” Kodi m’baleyu ankanena buku liti? Ankanena buku la Chingelezi lakuti “Anthu a Mitundu Inawo Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova”​—Adzadziwa Bwanji? Koma n’chifukwa chiyani anthu anasangalala ndi buku limeneli? Chifukwa chakuti linafotokoza mfundo zatsopano zokhudza maulosi opezeka m’buku la Ezekieli, amene akunena zimene zidzachitikire anthu onse m’tsogolo.

Kungochokera pamene bukuli linatulutsidwa, chiwerengero cha anthu a Mulungu chawonjezeka mofulumira kwambiri kuchoka pa anthu 1.5 miliyoni kufika pa anthu oposa 8 miliyoni. (Yes. 60:22) Atumiki a Yehova onsewa amalankhula zilankhulo zoposa 900. (Zek. 8:23) Ambiri mwa anthu amenewa analibe mwayi wophunzira buku limene likufotokoza mwatsatanetsatane maulosi ouziridwa amene mneneri Ezekieli analemba.

Komanso kungochokera m’chaka cha 1971, takhala tikumvetsa bwino mfundo zambiri za choonadi cha m’Baibulo chifukwa chakuti kuwala kwakhala kukuwonjezereka. (Miy. 4:18) Mwachitsanzo, m’chaka cha 1985 tinayamba kumvetsa bwino chifukwa chake a “nkhosa zina” amaonedwa kuti ndi olungama komanso kuti ndi anzake a Mulungu. (Yoh. 10:16; Aroma 5:18; Yak. 2:23) Kenako mu 1995 tinamvetsa koyamba kuti kuweruza komaliza kuti winawake ndi “nkhosa” kapena “mbuzi” kudzachitika m’tsogolo pa “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21; 25:31, 32) Kusintha konseku kunakhudza kwambiri mmene timamvera maulosi a m’buku la Ezekieli.

“Iwe mwana wa munthu, uonetsetse, umvetsere mwatcheru ndipo uchite chidwi ndi zonse zimene ndikuonetse, chifukwa ndakubweretsa kuno kuti udzachite zimenezi.”​—EZEKIELI 40:4

M’zaka zaposachedwapa kuwala kwakhala kukuwonjezerekabe. Taganizirani zimene tikuphunzira m’mafanizo a Yesu. Panopa tikumvetsa bwino kwambiri tanthauzo la mafanizo amenewa. Ena mwa mafanizo amenewa akufotokoza zinthu zimene zichitike pa chisautso chachikulu chimene chiyambe posachedwapa. Mofanana ndi zimenezi, tamvetsanso bwino maulosi ena amene akupezeka m’buku la Ezekieli. Ena mwa maulosi amenewa ndi okhudza Gogi wa ku Magogi (chaputala 38 ndi 39), ntchito ya munthu amene ali ndi kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera (chaputala 9) komanso okhudza chigwa chimene chinali ndi mafupa ouma ndiponso tanthauzo la kuphatikizidwa kwa ndodo ziwiri (chaputala 37). Kumvetsa bwino zinthu zonsezi kwachititsa kuti tisinthe zimene zinalembedwa zaka zambiri m’mbuyomu m’buku lakuti “Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova.”

Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri a Yehova akhala akufunsa kuti, “Kodi buku limene lingafotokoze bwino mfundo zatsopano za maulosi a m’buku la Ezekieli lidzatuluka liti?” Buku lake ndi limene mukuwerengali, lakuti Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera. Mukamawerenga mitu 22 ya m’bukuli komanso kuganizira mozama zithunzi zake zokongola, muona kuti polemba bukuli tinayesetsa kufufuza mosamala. Tinaganizira mozama komanso kupemphera kuti timvetse chifukwa chake Yehova watipatsa buku lochititsa chidwi la Ezekieli. Tinaganizira mozama mafunso ngati akuti: Kodi m’buku la Ezekieli muli maphunziro otani amene anathandiza anthu a m’nthawi ya Ezekieli komanso amene angatithandize ifeyo masiku ano? Kodi ndi maulosi ati amene akunena za zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo? Kodi tiziganiza kuti zinthu zosiyanasiyana zotchulidwa m’maulosi a Ezekieli zikuimira zinthu zinazake? Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kumvetsa bwino kwambiri buku la m’Baibuloli, lomwe tonse timasangalala kuliwerenga.

Mukamawerenga buku la Ezekieli, kuyambira kumayambiriro mpaka kumapeto, muphunzira za mbali yakumwamba ya gulu la Yehova yomwe ndi yochititsa chidwi. Sitikukayikira kuti mumachitanso chidwi kuti Yehova wakhazikitsa mfundo zapamwamba zoti atumiki ake akumwamba ndi apadziko lapansi, amene akufuna kumamulambira m’njira yovomerezeka, azitsatira. Buku la Kulambira Koyera likuthandizani kuti muziyamikira kwambiri zimene Yehova wachitira kale anthu ake komanso zimene awachitire posachedwapa. Muona kuti bukuli likufotokoza mfundo zikuluzikulu ziwiri mobwerezabwereza. Mfundo yoyamba ndi yakuti, ngati tikufuna kusangalatsa Yehova tikuyenera kudziwa komanso kuvomereza kuti iye ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Yachiwiri ndi yakuti, tiyenera kulambira Yehova m’njira imene amavomereza komanso kuti zochita zathu zizigwirizana ndi mfundo zake zamakhalidwe abwino, zomwe ndi zapamwamba.

Tikufunitsitsa kuti bukuli likuthandizeni kuti muzilambira Yehova m’njira imene imalemekeza dzina lake lalikulu ndi loyera. Komanso likulimbikitseni kuti muziyembekezera nthawi imene anthu amitundu yonse adzadziwe kuti iye ndi Yehova.​—Ezek. 36:23; 38:23.

Tikupempha Atate wathu wachikondi Yehova kuti akudalitseni chifukwa cha khama lanu poyesetsa kumvetsa buku limene anauzira mneneri Ezekieli kuti alembe.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova