Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 3

‘Ndidzakusonkhanitsani Pamodzi’​—Mulungu Analonjeza Kuti Adzabwezeretsa Kulambira Koyera

‘Ndidzakusonkhanitsani Pamodzi’​—Mulungu Analonjeza Kuti Adzabwezeretsa Kulambira Koyera

EZEKIELI 20:41

MFUNDO YAIKULU: Maulosi a Ezekieli anasonyeza kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa

Mpatuko unachititsa kuti zinthu zisokonekere mu Isiraeli ndipo anthu sankagwirizananso. Zonsezi zinkachitika chifukwa choti Aisiraeli anadetsa kulambira koyera komanso ananyoza dzina la Mulungu. Pa nthawi ya mavutoyi, Yehova anauza Ezekieli kuti anene maulosi osiyanasiyana amene anawapatsa chiyembekezo. Yehova anagwiritsa ntchito mawu ochititsa chidwi komanso masomphenya ochititsa mantha kuti alimbikitse Aisiraeli amene anali ku ukapolo komanso anthu onse amene ankafunitsitsa kuti kulambira koyera kubwezeretsedwe.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 8

“Ndidzazipatsa Mʼbusa Mmodzi”

Mulungu anauzira Ezekieli kuti alosere zokhudza Mesiya, Wolamulira wam’tsogolo komanso M’busa wa anthu a Yehova, amene adzabwezeretse kulambira koyera mpaka kalekale.

MUTU 9

“Ndidzawapatsa Mtima Umodzi”

Kodi maulosi amene anaperekedwa kwa Ayuda okhulupirika amene anali ku ukapolo ku Babulo akutikhudza masiku ano?

MUTU 10

“Mudzakhala Amoyo”

Ezekieli anaona masomphenya a mafupa ouma amane anakhalanso ndi moyo. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

MUTU 11

“Ine Ndakuika Kuti Ukhale Mlonda”

Kodi mlondayu ankayenera kulengeza uthenga wotani? Kodi ankayenera kupereka chenjezo lotani?

MUTU 12

“Ndidzawachititsa Kuti Akhale Mtundu Umodzi”

Yehova analonjeza kuti adzagwirizanitsa anthu ake.

MUTU 13

‘Ufotokoze za Kachisiyu’

Kodi kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya ankatanthauza chiyani?

MUTU 14

“Ili ndi Lamulo Lokhudza Kachisi”

Kodi ndi mfundo zofunika ziti zimene Ayuda a m’nthawi ya Ezekieli anaphunzira m’masomphenya amene Ezekieli anaona? Kodi masomphenyawa akutanthauza chiyani masiku ano?