Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 9

“Ndidzawapatsa Mtima Umodzi”

“Ndidzawapatsa Mtima Umodzi”

EZEKIELI 11:19

MFUNDO YAIKULU: Mmene ulosi wa Ezekieli wafotokozera nkhani yokhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera

1-3. Kodi Ababulo ankachita chiyani ponyoza anthu amene ankalambira Yehova, nanga n’chifukwa chiyani?

 YEREKEZERANI kuti ndinu Myuda wokhulupirika ndipo mukukhala mumzinda wa Babulo. Anthu amtundu wanu akhala ali ku ukapolo kwa zaka 50 kapena kuposa. Mogwirizana ndi zimene mumachita nthawi zonse, pa tsiku la Sabata mukupita kukakumana ndi okhulupirira anzanu kuti mukalambire Yehova. Pamene mukudutsa m’misewu ya mumzindawo, mukuona akachisi komanso malo olambirira osawerengeka. Ndipo mukuona anthu ambirimbiri akupita kumeneko n’kumakapereka nsembe kwa milungu yawo ngati Maduki komanso kuiimbira nyimbo.

2 Mutachoka pagulu la anthuwo mukukumana ndi kagulu kochepa ka anzanu amene mumalambira nawo Yehova. a Kenako mukufika pamalo opanda phokoso mwina pafupi ndi ngalande za mumzindawo kuti mupemphere, muimbe nyimbo komanso kuwerenga Mawu a Mulungu limodzi ndi anzanu. Pamene mukupemphera mukumva kaphokoso ka ngalawa zimene azimangirira m’mbali mwa ngalandeyo. Mtima wanu ukukhala m’malo chifukwa mukuona kuti amenewo ndi malo abata. Mukungolakalaka kuti anthu amumzindawo asakupezeni n’kusokoneza msonkhanowo ngati mmene amachitira nthawi zambiri. Koma n’chifukwa chiyani anthuwa amachita zimenezi?

3 Kuyambira kale, Ababulo akhala akupambana pankhondo ndipo anthu amumzindawo amaona kuti milungu yawo yabodza ndi imene imawathandiza. Ababulowo amaona kuti kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu, ndi umboni wakuti mulungu wawo Maduki ndi wamphamvu kuposa Yehova. Chifukwa cha zimenezi akunyoza Mulungu wanu komanso anthu ake. Nthawi zina amanena monyoza kuti: “Tiimbireni nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.” (Sal. 137:3) Nyimbo zambiri zopezeka m’buku la Masalimo zimanena mmene Ziyoni anagonjetsera adani a Yehova. Mwina Ababulo ankakonda kunyoza nyimbo zimenezi. Koma nyimbo zina za m’buku la Masalimo zimanena za Ababulo. Mwachitsanzo Salimo lina limanena kuti: “Yerusalemu amusandutsa bwinja. . . . Anthu otizungulira akutiseka komanso kutikuwiza.”​—Sal. 79:1, 3, 4.

4, 5. Kodi ulosi wa Ezekieli unapereka chiyembekezo chotani, nanga tikambirana chiyani m’mutuwu? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Palinso Ayuda ena opanduka amene akukunyozani chifukwa chakuti mumakhulupirira Yehova komanso aneneri ake. Ngakhale akukunyozani choncho, inuyo ndi banja lanu mumalimbikitsidwa chifukwa cha kulambira koyera. Mumasangalala mukasonkhana pamodzi ndi anzanu n’kumapemphera komanso kuimba nyimbo. Mumasangalalanso mukamawerenga Mawu a Mulungu. (Sal. 94:19; Aroma 15:4) Tayerekezani kuti patsiku limeneli munthu wina amene mumalambira naye limodzi wabweretsa chinthu china chapadera pamsonkhanowu. Wabweretsa mpukutu umene uli ndi ulosi wa Ezekieli. Mukusangalala kumva lonjezo la Yehova lakuti adzabwezeretsa anthu ake kudziko lakwawo. Pamene ulosiwo ukuwerengedwa mukusangalala mumtima ndipo mukuyembekezera kuti tsiku lina, inu ndi banja lanu mudzabwerera kwanu n’kukathandiza nawo pantchito yobwezeretsa kulambira koona.

5 M’buku la Ezekieli muli maulosi ambiri okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koona. Tiyeni tikambirane nkhani yopatsa chiyembekezo imeneyi. Kodi malonjezo amenewa anakwaniritsidwa bwanji kwa anthu omwe anali ku ukapolowo? Kodi maulosi amenewa akutikhudza bwanji masiku ano? Nthawi zina tizikambirana mmene maulosiwa adzakwaniritsidwire m’tsogolo.

“Iwo Adzapita ku Ukapolo, Kudziko Lina”

6. Kodi Mulungu ankachita chiyani pochenjeza mobwerezabwereza anthu amene ankamupandukira?

6 Kudzera mwa Ezekieli, Yehova anauza anthu ake momveka bwino chilango chimene adzawapatse chifukwa cha kupanduka kwawo. Yehova ananena kuti: “Iwo adzapita ku ukapolo, kudziko lina.” (Ezek. 12:11) Monga mmene tinaonera m’Mutu 6 wa bukuli, Ezekieli anachita zinthu zina zosonyeza mmene Mulungu adzaperekere chilangocho. Koma Ezekieli sanali munthu woyamba kupereka chenjezo ngati limeneli kwa Aisiraeli. Nthawi ya Mose zaka pafupifupi 1000 nthawi ya Ezekieli isanafike, Yehova anachenjeza anthu ake kuti akapitiriza kupanduka, adani adzawatenga n’kupita nawo ku ukapolo. (Deut. 28:36, 37) Aneneri ena ngati Yesaya ndi Yeremiya anali ataperekanso chenjezo ngati limeneli.—Yes. 39:5-7; Yer. 20:3-6.

7. Kodi Mulungu analanga anthu ake m’njira ziti?

7 Koma chomvetsa chisoni n’chakuti anthu ambiri sanamvere machenjezo amenewa. Ndipo zimenezi zinam’pweteka kwambiri Yehova mumtima. Zimene abusa oipa ankachita zinapangitsa kuti anthu apandukire Yehova, ayambe kulambira mafano, azichita zinthu zosakhulupirika komanso kuti azichita zachinyengo. Choncho anawalola kuti avutike ndi njala zomwe zinali zochititsa manyazi chifukwa dziko lawolo linali “loyenda mkaka ndi uchi.” (Ezek. 20:6, 7) Ndiye mogwirizana ndi zimene analosera, Yehova analola kuti anthu ake opandukawo atengedwe kupita ku ukapolo. Mavuto anafika pachimake mu 607 B.C.E., pamene Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake. Anthu ambirimbiri amene anapulumuka anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Kumeneko iwo ankanyozedwa komanso kutsutsidwa monga mmene tafotokozera kumayambiriro kwa mutu uno.

8, 9. Kodi Mulungu anachenjeza mpingo wa Chikhristu m’njira ziti pa nkhani ya mpatuko?

8 Kodi zimene zinachitikira Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo zinachitikiranso mpingo wa Chikhristu? Inde zinauchitikiradi. Mofanana ndi Ayuda a m’nthawi yakale, nawonso otsatira a Khristu anachenjezedwa zinthu zisanafike poipa. Kumayambiriro kwa utumiki wake, Yesu anati: “Chenjerani ndi aneneri abodza amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwa mitima yawo ali ngati mimbulu yolusa.” (Mat. 7:15) Patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo anauziridwa kuti alembe chenjezo lofanana ndi limeneli. Iye analemba kuti: “Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.”​—Mac. 20:29, 30.

9 Akhristu anaphunzitsidwa mmene angazindikirire komanso kupewa anthu oopsa amenewa. Akulu a Chikhristu analangizidwa kuti azichotsa ampatuko mumpingo. (1 Tim. 1:19; 2 Tim. 2:16-19; 2 Pet. 2:1-3; 2 Yoh. 10) Komabe mofanana ndi mmene zinalili ndi Aisiraeli komanso Ayuda akale, pang’ono ndi pang’ono Akhristu anasiya kumvera machenjezo achikondi amene ankapatsidwa. Pofika kumapeto kwa nthawi ya atumwi, mpatuko unali utamera mizu mumpingo. Yohane, yemwe anali mtumwi womaliza ndipo anali adakali ndi moyo kumapeto kwa nthawi ya atumwi, ananena kuti mumpingo munadzadza zachinyengo ndipo mpatuko unali utafalikira. Yohane anali mtumwi yekhayo amene anatsala yemwe ankachititsa kuti khalidwe loipali lisafalikire. (2 Ates. 2:6-8; 1 Yoh. 2:18) Kodi chinachitika n’chiyani Yohane atamwalira?

10, 11. Kodi fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole lakhala likukwaniritsidwa bwanji kuyambira m’zaka za m’ma 100 C.E.?

10 Yohane atamwalira, fanizo la Yesu lokhudza tirigu ndi namsongole linayamba kukwaniritsidwa. (Werengani Mateyu 13:24-30.) Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, Satana anafesa “namsongole” kapena kuti Akhristu abodza mumpingo ndipo zinthu zinayamba kuipa mofulumira. Yehova ayenera kuti anamva chisoni kwambiri kuona mpingo umene Mwana wake anauyambitsa, ukuipitsidwa ndi kulambira mafano, maholide, miyambo yachikunja komanso ziphunzitso zabodza zimene anazitenga kwa akatswiri anzeru za anthu amene sankaopa Mulungu komanso zipembedzo za Satana. Kodi Yehova anachita chiyani? Mofanana ndi zimene anachita ndi Aisiraeli osakhulupirika, iye analola kuti anthu ake atengedwe kupita ku ukapolo. Kuyambira m’zaka za m’ma 100 C.E., zinali zovuta kupeza Akhristu omwe anali ngati tirigu chifukwa chakuti Akhristu achinyengo anali atachuluka. Apa tingati mpingo woona wa Chikhristu unali ngati uli ku ukapolo ku Babulo Wamkulu yemwe amaimira zipembedzo zonse zonyenga, koma Akhristu achinyengowo ankangotsatira zochita za zipembedzo zabodzazo. Akhristu abodzawo atachuluka, matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu anayambika.

11 Pa nthawi yonse imene matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu anali amphamvu, panali Akhristu ena oona amene Yesu anawayerekezera ndi “tirigu” mufanizo lake lija. Mofanana ndi Ayuda amene anali ku ukapolo amene akufotokozedwa pa Ezekieli 6:9, Akhristu amenewa anakumbukira Mulungu woona. Molimba mtima ena ankatsutsa ziphunzitso zabodza za matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Iwo ankanyozedwa komanso kuzunzidwa. Kodi Yehova akanasiya anthu akewo kuti apitirize kukhala mumdima wauzimuwo mpaka kalekale? Ayi. Monga mmene zinalili ndi Aisiraeli akale, Yehova anasonyeza mkwiyo wake pamlingo woyenera komanso kwa nthawi yoyenera. (Yer. 46:28) Kuwonjezera pamenepo Yehova sanasiye anthu ake opanda chiyembekezo. Tiyeni tikambiranenso za Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo wakale ndipo tione mmene Yehova anawathandizira kuti akhale ndi chiyembekezo chakuti ukapolo wawo udzatha.

Kwa zaka zambiri Akhristu oona akhala akuzunzidwa ndi Babulo Wamkulu (Onani ndime 10, 11)

“Mkwiyo Wanga Udzatha”

12, 13. N’chifukwa chiyani patapita nthawi Yehova anasiya kukwiyira anthu ake omwe anali ku ukapolo m’nthawi ya Ezekieli?

12 Yehova anauza anthu ake mosapita m’mbali kuti adzawasonyeza mkwiyo wake koma anawatsimikiziranso kuti sadzawasonyeza mkwiyo wake wolungamawo mpaka kalekale. Mwachitsanzo taonani mawu awa: “Mkwiyo wanga udzatha komanso ukali wanga pa iwo udzachepa ndipo ndidzakhutira. Ndikadzamaliza kuwasonyeza ukali wanga, iwo adzadziwa kuti ine Yehova ndalankhula chifukwa ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha basi.” (Ezek. 5:13) N’chifukwa chiyani mkwiyo wa Yehova udzachepe?

13 Pakati pa anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo panalinso Ayuda okhulupirika amene anatengedwa limodzi ndi Ayuda osakhulupirikawo. Kuwonjezera pamenepo kudzera mwa Ezekieli, Mulungu analosera kuti ena mwa anthu ake adzalapa ali ku ukapolo komweko. Iye analosera kuti Ayuda olapawo adzakumbukira zinthu zochititsa manyazi zimene anachita popandukira Mulungu wawo ndipo adzachonderera Yehova kuti awakhululukire ndi kuwakomera mtima. (Ezek. 6:8-10; 12:16) Pa gulu la anthu okhulupirikawa panalinso Ezekieli, Danieli ndi anzake atatu. Ndipotu Danieli anakhala ndi moyo nthawi yaitali moti analipo panthawi imene ukapolo unkayamba komanso pamene unkatha. Pemphero lake lochokera pansi pamtima lolapa machimo amene Aisiraeli anachita likupezeka m’buku la Danieli chaputala 9. Sitikukayikira kuti mmene Danieli ankamvera, ndi mmenenso ankamvera anthu masauzande ambiri amene anali ku ukapolo. Iwo ankafunitsitsa kuti Yehova awakhululukire komanso ayambirenso kuwadalitsa. Choncho zinali zosangalatsa kwambiri kumva Ezekieli akufotokoza maulosi ouziridwa akuti Ayudawo adzamasulidwa ndipo adzabwezeretsa kulambira koyera.

14. N’chifukwa chiyani Yehova anathandiza anthu ake kuti abwerere kudziko lawo?

14 Koma panali chinthu china chofunika kwambiri pankhani ya kumasulidwa kwa anthu a Yehova kuti abwererenso kwawo. Sikuti ukapolowo unatha chifukwa chakuti Ayudawo anali oyenera kumasulidwa, koma chifukwa chakuti nthawi ya Yehova yoti ayeretse dzina lake pakati pa anthu amitundu ina inali itakwana. (Ezek. 36:22) Nthawi inali itakwana yoti Ababulo adziwe kuti milungu yawo monga Maduki sinali yofanana ngakhale pang’ono ndi Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Tiyeni tikambirane malonjezo 5 amene Yehova anauzira Ezekieli kuti auze Ayuda anzake amene anali nawo kuukapolo. Choyamba tiyeni tikambirane chimene lonjezo lililonse linkatanthauza kwa Ayuda okhulupirikawo. Kenako tiona njira yaikulu imene malonjezo amenewo anakwaniritsidwira.

15. Kodi Ayuda amene anabwerera kwawo anasintha zinthu ziti pa nkhani ya kulambira?

15 LONJEZO LOYAMBA. Palibe adzalambire mafano kapena zinthu zonyansa zogwirizana ndi chipembedzo chabodza. (Werengani Ezekieli 11:18; 12:24.) Monga mmene tinaonera m’Mutu 5 wa buku lino, Yerusalemu komanso kachisi wake anali ataipitsidwa ndi zochita za chipembedzo chabodza ngati kulambira mafano. Izi zikusonyeza kuti anthuwo ankachita zinthu zoipa ndipo anali atatalikirana ndi Yehova. Kudzera mwa Ezekieli, Yehova anali ataneneratu kuti Ayuda amene adzapite ku ukapolo azidzayembekezera nthawi imene adzayambirenso kulambira koyera komanso kosaipitsidwa. Madalitso onse amene adzabwere chifukwa cha kubwezeretsa kumeneku, adzadalira pa mfundo yofunika iyi: kubwezeretsedwa kwa dongosolo la Mulungu lokhudza kulambira koyera.

16. Kodi Yehova analonjeza chiyani zokhudza dziko la anthu ake?

16 LONJEZO LACHIWIRI. Adzabwerera kudziko lakwawo. Yehova anauza anthu omwe anali ku ukapolo kuti: “Ndidzakupatsani dziko la Isiraeli.” (Ezek. 11:17) Lonjezo limeneli linali lapadera kwambiri chifukwa Ababulo omwe ankazunza anthu a Mulungu, sanawapatse chiyembekezo chilichonse chakuti adzabwerera kudziko lakwawo limene ankalikonda kwambiri. (Yes. 14:4, 17) Kuwonjezera pamenepo, Ayuda amene adzabwerere kwawowo akadzapitiriza kukhala okhulupirika, dziko lawo lidzakhala lachonde komanso lobereka zipatso zimene zidzawathandize kuti akhale ndi chakudya komanso ntchito yopindulitsa. Kunyozeka komanso kuvutika chifukwa cha zikanakhala mbiri yakale.​—Werengani Ezekieli 36:30.

17. Kodi chinachitika n’chiyani pa nkhani yopereka nsembe kwa Yehova?

17 LONJEZO LACHITATU. Adzayambiranso kupereka nsembe paguwa la Yehova. Monga mmene taonera m’Mutu 2 wa buku lino mogwirizana ndi Chilamulo, kupereka nsembe inali m’mbali yofunika pakulambira koyera. Ngati Ayuda amene anabwerera kwawowo akanakhalabe omvera n’kumalambira Yehova yekha, nsembe zawo zikanakhala zovomerezeka kwa Yehova. Zimenezi zikanathandiza kuti machimo a anthuwo aphimbidwe komanso kuti akhale pafupi ndi Mulungu. Yehova analonjeza kuti: “Nyumba yonse ya Isiraeli idzanditumikira mʼphiri langa loyera, phiri lalitali lamʼdziko la Isiraeli, akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Kumeneko ndidzasangalala nanu ndipo ndidzafuna kuti mundibweretsere zopereka zanu komanso nsembe zanu zabwino kwambiri za zinthu zanu zonse zopatulika.” (Ezek. 20:40) Kulambira koyera kudzabwezeretsedwadi ndipo zimenezi zidzabweretsa madalitso kwa anthu a Mulungu.

18. Kodi Yehova akanaweta bwanji anthu ake?

18 LONJEZO LA 4. Abusa oipa adzachotsedwa. Chifukwa chachikulu chimene anthu a Mulungu ankachitira zoipa chinali chakuti ankatengera makhalidwe oipa a anthu amene ankawatsogolera. Yehova analonjeza kuti adzasintha zimenezi. Ponena za Abusa oipawo Yehova analonjeza kuti: “Ndiwaletsa kuti asamadyetse nkhosa zanga.  . . Ndidzalanditsa nkhosa zanga mʼkamwa mwawo.” Mosiyana ndi abusa oipawo, Yehova anatsimikizira anthu ake okhulupirika kuti: “Ndidzasamalira nkhosa zanga.” (Ezek. 34:10, 12) Kodi akanachita bwanji zimenezi? Akanagwiritsa ntchito amuna okhulupirika kuti akhale abusa.

19. Kodi Yehova analonjeza chiyani zokhudza mgwirizano?

19 LONJEZO LA 5. Anthu olambira Yehova adzakhala ogwirizana. Tangoganizani mmene zinthu zinalili. Zinalitu zokhumudwitsa kwa anthu amene ankalambira Mulungu mokhulupirika kuona kuti anthu a Mulungu sakugwirizana pa nthawi imene anali asanatengedwe kupita ku ukapolo. Anthuwo anayamba kutengera zochita za aneneri abodza komanso abusa oipa ndipo anafika poukira aneneri okhulupirika omwe ankaimira Yehova. Anthuwo anapanga magulu amene ankatsutsana. Chinthu chimodzi chosangalatsa chokhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koona ndi lonjezo ili limene Yehova anapereka kudzera mwa Ezekieli kuti: “Ndidzawapatsa mtima umodzi ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa iwo.” (Ezek. 11:19) Ngati Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu akanakhalabe ogwirizana ndi Yehova Mulungu komanso Ayuda anzawo palibe mdani amene akanatha kuwagonjetsa. Monga mtundu Ayudawo akanatha kuyambiranso kuchita zinthu zobweretsa ulemerero kwa Yehova m’malo mochita zinthu zimene zikanachititsa kuti Yehova anyozedwe komanso asalemekezedwe.

20, 21. Kodi malonjezo a Mulungu anakwaniritsidwa bwanji kwa Ayuda amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo?

20 Kodi malonjezo 5 amenewa anakwaniritsidwa kwa Ayuda amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo? Tingachite bwino kukumbukira mawu a mtumiki wakale wokhulupirika Yoswa amene ananena kuti: “Palibe mawu ngakhale amodzi pa malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena, omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.” (Yos. 23:14) Monga mmene Yehova anakwaniritsira malonjezo ake m’nthawi ya Yoswa, anachitanso chimodzimodzi pa nthawi imene Ayuda amene anali ku ukapolo anabwerera kudziko lakwawo.

21 Ayuda anasiya kuchita zinthu zina zimene zinkawachititsa kuti atalikirane ndi Yehova, monga kulambira mafano komanso kuchita zinthu zina zonyansa zokhudzana ndi chipembedzo chabodza. Ngakhale kuti zinkaoneka zosatheka, Ayudawo anayambiranso kukhala m’dziko lawo, ankalima ndipo ankakhala moyo wosangalala. Chimodzi mwa zinthu zimene anayambirira kuchita ndi kubwezeretsa guwa lansembe ku Yerusalemu komanso kupereka nsembe zovomerezeka paguwalo. (Ezara 3:2-6) Yehova anawadalitsa powapatsa abusa abwino auzimu monga Ezara, amene anali wansembe wokhulupirika komanso wokopera Malemba, bwanamkubwa Nehemiya ndi Zerubabele, Mkulu Wansembe Yoswa komanso aneneri olimba mtima monga Hagai, Zekariya ndi Malaki. Pa nthawi yonse imene anthuwa ankamvera komanso kutsatira malangizo a Yehova, ankakhala ogwirizana kwambiri kuposa kale lonse.​—Yes. 61:1-4; werengani Yeremiya 3:15.

22. Kodi tikudziwa bwanji kuti kukwaniritsidwa koyamba kwa maulosi okhudza kubwezeretsa kunali chithunzi chabe cha zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo?

22 N’zosachita kufunsa kuti anthu analimbikitsidwa kwambiri ataona kukwaniritsidwa kwa mbali yoyamba ya malonjezo a Yehova okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera. Koma kukwaniritsidwa kwa malonjezo amenewa kunkaimira chinthu china chapadera kwambiri. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Kukwaniritsidwa kwa malonjezo amenewa kunkadalira zimene Ayuda akanachita. Yehova akanakwaniritsa malonjezo amenewa pokhapokha ngati anthuwo akanapitiriza kukhala omvera. Patapita nthawi, Ayudawo anasiyanso kukhala omvera ndipo anapanduka. Mogwirizana ndi zimene Yoswa ananena, nthawi zonse zimene Yehova wanena zimachitika. Choncho malonjezowo anali oti adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu komanso yokhalitsa. Tiyeni tione mmene zimenezi zinachitikira.

“Ndidzasangalala” Nanu

23, 24. Kodi “nthawi ya kubwezeretsa zinthu zonse” inayamba liti, nanga inayamba bwanji?

23 Monga anthu amene timaphunzira Baibulo, timadziwa kuti masiku otsiriza a dziko loipali anayamba mu 1914. Koma zimenezi sizipangitsa kuti atumiki a Yehova azikhala achisoni. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse” yomwe ndi nyengo yochititsa chidwi inayambika mu 1914. (Mac. 3:21) Tikudziwa bwanji zimenezi? Kodi chinachitika n’chiyani kumwamba mu 1914? Yesu Khristu yemwe ndi Mesiya anaikidwa kukhala Mfumu. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene zinachitikazo kunali kubwezeretsa zinthu? Musaiwale kuti Yehova analonjeza Mfumu Davide kuti banja lake lidzakhala lachifumu mpaka kalekale. (1 Mbiri 17:11-14) Ufumu umenewo unasokonezeka pang’ono mu 607 B.C.E. pamene Ababulo anawononga Yerusalemu, n’kuthetsa ulamuliro wa mafumu am’banja la Davide.

24 Monga “Mwana wa munthu,” Yesu anali mbadwa ya Davide ndipo anali woyenerera mwalamulo kukhala pampando wachifumu wa Davide. (Mat. 1:1; 16:13-16; Luka 1:32, 33) Mu 1914 Yehova ataika Yesu pampando wachifumu kumwamba, “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse” inayamba. Tsopano njira inatseguka yoti Yehova agwiritse ntchito Mfumu yagwiro imeneyi popitiriza ntchito yobwezeretsa zinthu.

25, 26. (a) Kodi ukapolo wa ku Babulo Wamkulu unatha liti, nanga tikudziwa bwanji zimenezo? (Onaninso bokosi lakuti “N’chifukwa Chiyani Tikuti Chinali Chaka cha 1919?”) (b) Kodi n’chiyani chimene chinayamba kukwaniritsidwa mu 1919?

25 Chimodzi mwa zinthu zoyambirira zimene Khristu anachita atangokhala Mfumu, chinali choti iye ndi Atate ake anayendera anthu a Mulungu kuti aone dongosolo la kulambira koyera padziko lapansi. (Mal. 3:1-5) Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena mufanizo lake la tirigu ndi namsongole, kwa nthawi yaitali zinali zosatheka kusiyanitsa tirigu ndi namsongole kapena kuti Akhristu enieni odzozedwa ndi Akhristu abodza. b Koma mu 1914 nthawi yokolola inafika ndipo zinali zosavuta kuwasiyanitsa. Kwa zaka zambiri chaka cha 1914 chisanafike, Ophunzira Baibulo okhulupirika ankadzudzula zinthu zolakwika zimene matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu ankachita ndipo anayamba kusiya kuchita zinthu zimene matchalitchi amenewa ankachita. Nthawi ya Yehova yoti amalizitse kuwabwezeretsa inali itakwana. Choncho kumayambiriro kwa chaka cha 1919, patangodutsa zaka zochepa ‘nyengo yokolola’ itayambika, anthu a Mulungu anali atamasukiratu ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. (Mat. 13:30) Apatu ukapolo wa anthu a Mulungu unatheratu.

26 Maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera anayamba kukwaniritsidwa m’njira yaikulu kuposa njira ina iliyonse imene anthu a Mulungu akale anaona. Tsopano tiyeni tione mmene malonjezo 5 amene takambirana kale aja anakwaniritsidwira m’njira yaikulu.

27. Kodi Mulungu anayeretsa bwanji anthu ake kuti asamalambirenso mafano?

27 LONJEZO LOYAMBA. Kutha kwa kulambira mafano komanso miyambo ina yonyansa yachipembedzo. Kumapeto kwa zaka za m’ma 1800 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, Akhristu okhulupirika anayamba kusonkhana pamodzi ndipo anayamba kusiya kutsatira miyambo ya chipembedzo chabodza. Anasiya kukhulupirira chiphunzitso cha utatu, anasiya kukhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa komanso anasiya kukhulupirira kuti kuli moto wa helo. Anasiya kukhulupirira zonsezi chifukwa sizigwirizana ndi zimene malemba amanena komanso ndi zochokera kuchipembedzo chabodza. Iwo anayamba kuona kuti kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira ndi kulambira mafano. Pang’ono ndi pang’ono anthu a Mulungu anayambanso kuona kuti kugwiritsa ntchito mtanda polambira ndi mtundu wakulambira mafano.​—Ezek. 14:6.

28. Kodi anthu a Mulungu anabwezeretsedwa bwanji kudziko lawo?

28 LONJEZO LACHIWIRI. Anthu a Mulungu anayambiranso kulambira koyera. Atachoka m’Babulo Wamkulu, Akhristu okhulupirika anayambiranso kulambira Mulungu woona ngati mmene ankachitira poyamba. Yehova akuwadalitsa, akulandira chakudya chauzimu chochuluka chimene chimalimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova ndipo sasowa chilichonse. (Werengani Ezekieli 34:13, 14.) Tiphunzira zambiri pamfundo imeneyi m’Mutu 19 wa buku lino. Tiona kuti Yehova wadalitsa anthu ake ndi chakudya chauzimu chochuluka chopatsa thanzi chimene chimalimbitsa ubwenzi wawo ndi iye.​—Ezek. 11:17.

29. Kodi mu 1919 munachitika zotani zimene zinalimbikitsa ntchito yolalikira?

29 LONJEZO LACHITATU. Anayambiranso kupereka nsembe zomwe ankapereka ngati mphatso paguwa la Yehova. M’nthawi ya atumwi, Akhristu sanauzidwe kuti azipereka nsembe zanyama koma kuti azipereka mphatso zamtengo wapatali, zomwe ndi mawu otamanda Yehova komanso kulalikira kwa ena zokhudza Yehovayo. (Aheb. 13:15) Pa nthawi yonse imene Akhristu anali ku ukapolo ku Babulo Wamkulu, panalibe dongosolo lililonse lowathandiza kuti azilambira Mulungu komanso kulalikira. Koma pamene ukapolowo unkatha, anthu a Mulungu anali atayamba kale kupereka nsembe zotamanda Mulungu zimenezi. Anthu a Mulunguwo ankatanganidwa ndi ntchito yolalikira komanso ankasangalala kutamanda Mulungu pamisonkhano yawo. Kuyambira mu 1919 “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” ankalimbikitsa kwambiri ntchito yolalikira ndipo anakonza zoti izichitika mwadongosolo kwambiri. (Mat. 24:45-47) Choncho paguwa lansembe la Yehova pankabwera nsembe zambiri za anthu otamanda dzina loyera la Yehova amene ankachulukirachulukira.

30. Kodi Yesu anachita chiyani kuti anthu ake akhale ndi abusa abwino?

30 LONJEZO LA 4. Kuchotsa abusa oipa. Khristu anapulumutsa anthu a Mulungu kwa abusa achinyengo komanso odzikonda a m’matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Mumpingo wa Chikhristu abusa amene ankachita zinthu ngati abusa abodza amenewo, anachotsedwa pa maudindo awo. (Ezek. 20:38) Monga m’busa wabwino, Yesu anaonetsetsa kuti nkhosa zake zikusamaliridwa mwachikondi. Mu 1919 iye anasankha kapolo wokhulupirika komanso wanzeru. Kagulu kakang’ono kameneko ka Akhristu odzozedwa okhulupirika, kankatsogolera pa ntchito yopereka chakudya chauzimu. Choncho anthu a Mulungu ankasamaliridwa bwino. Patapita nthawi, akulu anaphunzitsidwa kuti azithandiza kusamalira “nkhosa za Mulungu.” (1 Pet. 5:1, 2) Mawu ouziridwa opezeka pa Ezekieli 34:15, 16 kawirikawiri akhala akugwiritsidwa ntchito pokumbutsa abusa a Chikhristu mfundo zimene Yehova komanso Yesu Khristu amafuna kuti abusawa azitsatira.

31. Kodi Yehova anakwaniritsa bwanji ulosi wa pa Ezekieli 11:19?

31 LONJEZO LA 5. Mgwirizano wa anthu olambira Yehova. Kwa zaka zambiri, kwayambika zipembedzo zambiri kuchokera m’matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu, kuphatikizapo timagulu timene timangokhalira kukangana. Mosiyana ndi zimenezi, Yehova wachita zinthu zodabwitsa ndi anthu ake amene ayambiranso kumulambira m’njira imene amavomereza. Zimene Mulungu analonjeza kudzera mwa Ezekieli zakuti “ndidzawapatsa mtima umodzi,” zakhala zikukwaniritsidwa mochititsa chidwi. (Ezek. 11:19) Padziko lonse lapansi pali anthu mamiliyoni ambiri amene amatsatira Khristu ndipo anthu amenewa ndi ochokera m’zipembedzo, m’mitundu, m’zikhalidwe zosiyanasiyana komanso amapeza zinthu mosiyanasiyana. Koma anthu onsewa amaphunzitsidwa mfundo za choonadi zofanana ndipo amagwira ntchito yofanana mogwirizana kwambiri. Usiku womaliza wa moyo wake padziko lapansi, Yesu anapemphera kuchokera pansi pamtima kuti otsatira ake akhale ogwirizana. (Werengani Yohane 17:11, 20-23.) Masiku ano Yehova wayankha pemphero limeneli m’njira yaikulu kwambiri.

32. Kodi mukumva bwanji mukaganizira za ulosi wokhudza kubwezeretsa? (Onaninso bokosi lakuti “Maulosi Okhudza Ukapolo ndi Kubwezeretsa.”)

32 Kodi simukusangalala kuti mukukhala m’nthawi yapadera kwambiri imene kulambira koyera kwabwezeretsedwa? Timaona kukwaniritsidwa kwa maulosi a Ezekieli m’mbali zonse za kulambira kwathu masiku ano. Sitikukayikira kuti panopa Yehova akusangalala ndi anthu ake mogwirizana ndi zimene ananeneratu kudzera mwa Ezekieli kuti “ndidzasangalala” nanu. (Ezek. 20:41) Anthu a Mulungu amenewa ndi ogwirizana ndipo akudyetsedwa bwino komanso akupereka nsembe zotamanda Yehova padziko lonse lapansi. Kodi simukusangalala kukhala m’gulu la anthu amenewa, omwe anamasulidwa atakhala mu kapolo wauzimu kwa zaka zambiri? Koma maulosi ena a Ezekieli okhudza kubwezeretsa akwaniritsidwa m’njira yaikulu kutsogoloku.

“Ngati Munda wa Edeni”

33-35. (a) Kodi ulosi wa pa Ezekieli 36:35 unatanthauza chiyani kwa Ayuda amene anali ku ukapolo? (b) Kodi ulosi umenewu ukutanthauza chiyani kwa anthu a Mulungu masiku ano? (Onaninso bokosi lakuti “Nthawi Yobwezeretsa Zinthu Zonse.”)

33 Monga mmene taonera, “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse” inayamba ndi kubwezeretsedwa kwa mzere wa mafumu am’banja la Davide pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu mu 1914. (Ezek. 37:24) Kenako Yehova anapatsa Khristu mphamvu kuti abwezeretse kulambira koyera pakati pa anthu ake amene anakhala mu ukapolo wauzimu kwa zaka zambiri. Koma kodi ntchito yobwezeretsa imene Khristu anagwira inathera pomwepo? Ayi ndithu. Ntchito imeneyi idzapitirirabe mochititsa chidwi m’tsogolo ndipo maulosi a Ezekieli akufotokoza mwatsatanetsatane mmene ntchito imeneyi idzachitikire.

34 Mwachitsanzo, taganizirani mawu ouziridwa otsatirawa: “Anthu adzanena kuti: ‘Dziko limene linali bwinja tsopano lakhala ngati munda wa Edeni.’” (Ezek. 36:35) Kodi lonjezo limeneli linkatanthauza chiyani kwa Ezekieli komanso Ayuda anzake omwe anali ku ukapolo? N’zosachita kufunsa kuti iwo sankayembekezera kuti dziko lawo lingasinthe n’kukhala munda wokongola kapena Paradaiso amene Yehova anadzala m’munda wa Edeni. (Gen. 2:8) Koma iwo anamvetsa kuti Yehova akuwatsimikizira kuti dziko lawo lobwezeretsedwa lidzakhalanso lokongola ndiponso lobala zipatso.

35 Kodi lonjezo limeneli likutanthauza chiyani kwa ife masiku ano? Sitikuyembekezera kuti dziko loipali lingasinthe panopa n’kukhala Paradaiso pamene Satana Mdyerekezi akulilamulira. Koma tikudziwa kuti mawu amenewa akukwaniritsidwa mwauzimu masiku ano. Monga atumiki a Yehova, tili m’paradaiso wauzimu amene anabwezeretsedwa kapena kuti malo amene timaona kuti kutumikira Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu ndipo timamutumikira mwakhama. Kulambira kumeneku kukupitirizabe kukhala koyera mowonjezerekawonjezereka. Koma kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa bwanji m’tsogolo?

36, 37. Kodi ndi malonjezo ati amene adzakwaniritsidwe m’Paradaiso kutsogoloku?

36 Nkhondo yaikulu ya Aramagedo ikadzatha, Yesu adzaonjezera ntchito yobwezeretsa kuti iphatikize dziko lapansi lenilenili. Mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000, Yesu adzatsogolera anthu kuti asinthe dzikoli kukhala munda wa Edeni kapena kuti Paradaiso ngati mmene Yehova ankafunira. (Luka 23:43) Pa nthawi imeneyo anthu onse adzakhala ogwirizana ndipo azidzasamalira dziko lapansili. Kwina kulikonse sikudzakhalanso zinthu zoopsa kapena zochititsa mantha. Taganizirani mmene zidzakhalire lonjezo ili likadzakwaniritsidwa lakuti: “Ine ndidzachita pangano lamtendere ndi nkhosazo. Ndipo ndidzachotsa zilombo zolusa mʼdzikomo nʼcholinga choti nkhosazo zizidzakhala mʼchipululu zili zotetezeka ndipo zizidzagona munkhalango.”​—Ezek. 34:25.

37 Kodi mukutha kuona zimenezi m’maganizo mwanu? Popanda kuopa chilichonse muzidzatha kupita kulikonse padziko lapansili. Palibe chilombo chilichonse chimene chidzakuvulazeni. Palibe choopsa chilichonse chimene chidzasokoneze mtendere wanu. Muzidzatha kuyenda nokhanokha munkhalango yowilira kwambiri n’kumasangalala ndi kukongola kwake. Muzidzatha kugona bwinobwino nkhalangomo muli otetezeka ndipo muzidzadzuka mutapuma popanda chilichonse chokuvulazani.

Taganizirani nthawi imene “mudzagone munkhalango” popanda kuopa chilichonse (Onani ndime 36, 37)

38. Kodi mukumva bwanji mukaganizira za kukwaniritsidwa kwa lonjezo lomwe lili pa Ezekieli 28:26?

38 Tidzaonanso kukwaniritsidwa kwa lonjezo lakuti: “Adzakhala mʼdzikolo motetezeka ndipo adzamanga nyumba komanso kulima minda ya mpesa. Iwo azidzakhala motetezeka ndikadzapereka chiweruzo kwa onse owazungulira amene amawanyoza. Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo.” (Ezek. 28:26) Adani onse a Yehova akadzawonongedwa, tidzasangalala ndi mtendere komanso chitetezo padziko lonse. Pamene tizidzasamalira dziko lapansi, tidzatha kudzisamalira tokha komanso anthu amene timawakonda, tidzamanga nyumba zabwino n’kumakhalamo komanso tidzadzala minda yampesa.

39. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti maulosi amene Ezekieli analemba okhudza Paradaiso adzakwaniritsidwa?

39 Kodi malonjezo amenewa akungomveka ngati maloto chabe kwa inu? Ngati ndi choncho, kumbukirani zimene mwaona kale pa nthawi ino ya “kubwezeretsa zinthu zonse.” Ngakhale kuti Satana akutsutsa kwambiri, Yesu wapatsidwa mphamvu kuti abwezeretse kulambira koyera munthawi yovuta ino. Umenewutu ndi umboni wamphamvu wakuti malonjezo onse amene Yehova ananena kudzera mwa Ezekieli adzakwaniritsidwa.

a Ayuda ambiri amene anali ku ukapolo ankakhala m’midzi imene inali kutali ndi mzinda wa Babulo. Mwachitsanzo, Ezekieli ankakhala limodzi ndi Ayuda amene ankakhala pafupi ndi mtsinje wa Kebara. (Ezek. 3:15) Koma panalinso Ayuda ena ochepa amene ankakhala mumzinda. Pa gulu la anthu amenewa panali “amʼbanja lachifumu komanso anthu olemekezeka.”​—Dan. 1:3, 6; 2 Maf. 24:15.

b Mwachitsanzo, sitinganene motsimikiza kuti ndi anthu ati amene ankatsutsana ndi zimene matchalitchi omwe amati ndi a Chikhristu ankaphunzitsa m’zaka za m’ma 1500 amene analidi Akhristu odzozedwa.