Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 11

“Ine Ndakuika Kuti Ukhale Mlonda”

“Ine Ndakuika Kuti Ukhale Mlonda”

EZEKIELI 33:7

MFUNDO YAIKULU: Yehova anasankha mlonda ndipo anamuuza ntchito imene akuyenera kugwira

1. Fotokozani zimene aneneri a Yehova omwe akhala akugwira ntchito ngati mlonda akhala akuchita komanso zimene zinachitika pambuyo pake.

 MLONDA waima pamwamba pa mpanda wa Yerusalemu ndipo akutchinga maso ake pamene dzuwa likulowa. Iye akuyang’ana kutali. Mwadzidzidzi, akutenga lipenga lake n’kuika pakamwa, kenako akukokera mpweya m’mapapo ndi kuliza lipenga lochenjeza, chifukwa asilikali a Babulo akubwera. Koma nthawi inali itatha kuti anthu ozengereza okhala mumzindawo achitepo kanthu atamva kulira kwa lipenga lochenjezalo. Kwa zaka zambiri, alonda osankhidwa ndi Yehova kapena kuti aneneri akhala akuchenjeza anthu a Yehova kuti tsiku limeneli lidzafika koma anthuwo sanafune kumvera. Tsopano asilikali a Babulo azungulira mzindawo. Atazungulira mpandawo kwa miyezi yambiri, asilikaliwo anagumula mpanda wa mzindawo, anagwetsa kachisi komanso anapha ndi kugwira anthu osakhulupirika okhala mumzinda wa Yerusalemu amene ankalambira mafano.

2, 3. (a) Kodi anthu akukumana ndi zinthu zotani masiku ano? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Masiku ano, asilikali a Yehova akupita kukapereka chiweruzo kwa anthu osakhulupirika amene akukhala padziko lapansi. (Chiv. 17:12-14) Chiweruzocho chidzakhala pachimake pa chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo. (Mat. 24:21) Koma anthu ambiri adakali ndi mwayi, woti amvere chenjezo limene likuperekedwa ndi anthu amene anasankhidwa ndi Yehova, kuti agwire ntchito ya mlonda.

3 Kodi n’chiyani chimene chinachititsa kuti Yehova asankhe alonda? Kodi mlonda amalengeza uthenga wotani? Kodi ndi ndani amene akhala akugwira ntchito ya mlonda, nanga ifeyo udindo wathu ndi wotani? Tiyeni tikambirane mayankho amafunso amenewa.

“Ukuyenera Kuwachenjeza”

4. N’chifukwa chiyani Yehova anasankha alonda? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Werengani Ezekieli 33:7. Kale alonda enieni ankaima pamwamba pa mpanda wa mzinda kuti ateteze anthu okhala mumzindawo. Umenewu unali umboni wakuti wolamulira wa mzindawo akufuna kuti anthu ake akhale otetezeka. Ngakhale kuti phokoso la lipenga la mlondayo likanatha kudzutsa anthu amumzindawo, phokoso lomwelo likanathanso kupulumutsa moyo wa anthu amene akanamvera chenjezolo. Mofanana ndi zimenezi, sikuti Yehova anasankha alonda kuti aziopseza Aisiraeli ndi uthenga wachiweruzo koma chifukwa chakuti ankakonda anthu ake ndipo ankafuna kuwateteza.

5, 6. Kodi ndi njira imodzi iti imene Yehova amasonyezera chilungamo chake?

5 Pamene Yehova anasankha Ezekieli kuti akhale mlonda anasonyeza makhalidwe ake amene amatilimbikitsa. Tiyeni tikambirane awiri a makhalidwe amenewa.

6 Chilungamo: Chilungamo cha Yehova chimaonekera akamachita zinthu mosakondera ndi aliyense wa ife payekhapayekha. Mwachitsanzo, ngakhale kuti gulu lalikulu linamva komanso kukana uthenga wa Ezekieli, Yehova sankaona kuti Aisiraeli onse ndi opanduka koma ankafuna kuona zimene aliyense payekha angachite akamva uthengawo. Mobwerezabwereza amasonyeza kuti akulankhula ndi “munthu woipa” komanso “munthu amene amachita zinthu zabwino.” Choncho Yehova amapereka chiweruzo potengera zimene munthu aliyense wachita atamva uthenga wake.​—Ezek. 33:8, 18-20.

7. Kodi Yehova amaganizira zinthu ziti akamaweruza anthu?

7 Chilungamo cha Yehova chimaonekeranso bwino tikaona mmene amaweruzira anthu. Anthu samaweruzidwa potengera zimene anachita m’mbuyo koma amaweruzidwa potengera zimene achita ndi chenjezo limene apatsidwa. Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ndikauza munthu woipa kuti: ‘Udzafa ndithu,’ ndiyeno iyeyo nʼkusiya machimo akewo, nʼkuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, . . . munthuyo adzapitiriza kukhala ndi moyo.” Kenako Yehova anawonjezera mfundo yochititsa chidwi yakuti: “Sadzapatsidwa chilango chifukwa cha machimo amene anachitawo.” (Ezek. 33:14-16) Komabe anthu amene anachita zolungama m’mbuyomu sangayembekezere kuti salandira chilango, ngati panopa atasiya kumvera Mulungu. Yehova ananena kuti ngati munthu wayamba “kukhulupirira kuti zinthu zolungama zimene anachita mʼmbuyo zidzamupulumutsa nʼkuchita zinthu zoipa, zinthu zonse zolungama zimene anachita zija sizidzakumbukiridwa. Iye adzafa chifukwa cha zinthu zoipa zimene wachita.”​—Ezek. 33:13.

8. Kodi machenjezo amene amapezeka m’maulosi amatiphunzitsa zotani zokhudza chilungamo cha Yehova?

8 Umboni wina wakuti Yehova ndi wachilungamo ndi wakuti amapereka chenjezo asanapereke chilango. Mwachitsanzo, Ezekieli anayamba ntchito yake kutatsala zaka pafupifupi 6 kuti asilikali a Babulo awononge Yerusalemu. Koma Ezekieli sanali woyamba kuchenjeza anthu a Mulungu kuti adzaweruzidwa chifukwa cha zochita zawo. Tikutero chifukwa zaka 100 Yerusalemu asanawonongedwe, Yehova anatumiza mneneri Hoseya, Yesaya, Mika, Odedi ndi Yeremiya kuti agwire ntchito ngati alonda. Yehova anauza Yeremiya kuti akakumbutse Aisiraeli kuti: “Ine ndinaika alonda amene ankanena kuti: ‘Mverani kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa!’” (Yer. 6:17) Yehova kapena alondawo sakanaimbidwa mlandu chifukwa cha anthu amene anaphedwa pamene Ababulo anapereka chiweruzo cha Yehova.

9. Kodi Yehova anasonyeza bwanji chikondi chokhulupirika?

9 Chikondi: Yehova anasonyeza chikondi chokhulupirika pamene anatumiza alonda kuti akachenjeze anthu olungama komanso anthu oipa omwe anamukhumudwitsa ndi kuipitsa mbiri yake. Tangoganizani, Aisiraeli ankadziwika kuti ndi anthu a Yehova koma mobwerezabwereza anamusiya n’kuyamba kulambira milungu yabodza. Yehova anasonyeza mmene zinamupwetekera poyerekezera mtunduwo ndi mkazi wachigololo. (Ezek. 16:32) Ngakhale zinali choncho, Yehova sanawataye mofulumira. Iye ankafuna kuti anthuwo abwererenso kwa iye osati kuwabwezera zoipa. Iye choyamba ankapereka mwayi kwa anthuwo kuti asinthe asanawapatse chilango. Chifukwa chiyani? Iye anauza Ezekieli kuti: “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma ndimafuna kuti munthu woipa asinthe zochita zake nʼkupitiriza kukhala ndi moyo.” (Ezek. 33:11) Umu ndi mmene Yehova ankamvera m’mbuyomo ndipo ndi mmenenso akumvera panopa.​—Mal. 3:6.

10, 11. Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ake?

10 Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene Yehova anachitira zinthu ndi Aisiraeli mwachilungamo komanso mwachikondi? Chinthu chimodzi chimene tikuphunzira ndi chakuti tisamaone anthu amene tikuwalalikira monga gulu koma tiziona munthu aliyense payekha. Tingalakwitse kwambiri ngati titaweruziratu munthu kuti ndi wosayenera kumva uthenga wathu chifukwa cha zimene ankachita m’mbuyo, chikhalidwe chake, mtundu wake, chuma chimene ali nacho kapena chilankhulo chake. Yehova anaphunzitsa mtumwi Petulo mfundo imene ikugwirabe ntchito mpaka pano yakuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Mac. 10:34, 35.

Kodi timaona anthu ngati mmene Yehova amawaonera? (Onani ndime 10)

11 Mfundo ina yofunika imene tikuphunzirapo ndi yakuti, tikuyenera kumadzifufuza nthawi ndi nthawi chifukwa zinthu zachilungamo zimene tinkachita m’mbuyomo, sizingapangitse kuti tisalandire chilango panopa, ngati tikuchita zoipa. Tizikumbukira kuti nafenso timalakwitsa zinthu ngati mmene zilili ndi anthu amene timawalalikira. Malangizo amene mtumwi Paulo anapereka kumpingo wa Korinto akugwiranso ntchito kwa ifeyo. Iye anati: “Amene akuganiza kuti waima bwinobwino asamale kuti asagwe. Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene anthu ena amakumana nawo.” (1 Akor. 10:12, 13) Tisakhale ngati munthu amene ‘amakhulupirira kuti zinthu zolungama zimene anachita mʼmbuyo zidzamupulumutsa’ n’kumaganiza kuti akhoza kumachita zinthu zoipa koma osalandira chilango, chifukwa chakuti amachitanso zinthu zabwino. (Ezek. 33:13) Kaya tatumikira Yehova kwa nthawi yayitali bwanji, n’zofunika kuti tikhale odzichepetsa komanso omvera.

12. Kodi tizikumbukira chiyani ngati tinachita machimo akuluakulu m’mbuyomo?

12 Koma bwanji ngati panopa tikudzimvera chisoni chifukwa cha machimo akuluakulu amene tinachita m’mbuyomo? Kuchokera pa zimene Ezekieli ananena tikuphunzira kuti Yehova adzalanga anthu osalapa. Komanso tikuphunzira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi osati wobwezera zoipa. (1 Yoh. 4:8) Ngati zochita zathu zikusonyeza kuti talapa, tisamaganize kuti Mulungu sangatikhululukire machimo athu. (Yak. 5:14, 15) Yehova anali wofunitsitsa kukhululukira Aisiraeli amene ankachita chigololo mwauzimu ndipo ndi wofunitsitsanso kutikhululukira ifeyo.​—Sal. 86:5.

“Lankhula ndi Anthu a Mtundu Wako”

13, 14. (a) Kodi alonda ankalengeza uthenga wotani? (b) Kodi Yesaya analengeza uthenga wotani?

13 Werengani Ezekieli 33:2, 3. Kodi alonda a Yehova ankayenera kulengeza uthenga wotani? Mbali yofunika kwambiri ya ntchito yawo inali kuchenjeza anthu komanso kulengeza uthenga wabwino. Tiyeni tione zitsanzo.

14 Yesaya amene anatumikira kuyambira cha m’ma 778 mpaka mu 732 B.C.E., anachenjeza kuti Ababulo adzalanda mzinda wa Yerusalemu ndipo adzatenga anthu okhala mumzindawo kupita nawo ku ukapolo. (Yes. 39:5-7) Iye anauziridwanso kuti alembe kuti: “Tamvera! Alonda ako akufuula. Onse akufuula pamodzi mosangalala, chifukwa akuona bwinobwino pamene Yehova akusonkhanitsanso anthu okhala mu Ziyoni.” (Yes. 52:8) Yesaya analengeza nkhani yabwino kwambiri yakuti kulambira koona kudzabwezeretsedwa.

15. Kodi Yeremiya ankalengeza uthenga wotani?

15 Yeremiya amene anatumikira kuyambira mu 647 mpaka mu 580 B.C.E., kawirikawiri ankamunena kuti ndi “munthu amene amakonda kulengeza za tsoka.” Mosakaikira iye anagwira ntchito yofunika kwambiri yochenjeza Aisiraeli amene ankachita zinthu zoipa kuti Yehova adzawabweretsera masoka. a Koma analengezanso uthenga wabwino chifukwa analosera kuti anthu a Mulungu adzabwerera kudziko lawo n’kuyambiranso kulambira koyera.​—Yer. 29:10-14; 33:10, 11.

16. Kodi uthenga wa Ezekieli unathandiza bwanji Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo?

16 Ezekieli anaikidwa kukhala mlonda mu 613 B.C.E., ndipo anachita utumiki wake mpaka kufika mu 591 B.C.E. Monga mmene taonera m’Mutu 5 ndi 6 wa bukuli, Ezekieli anagwira mwakhama ntchito yochenjeza Aisiraeli za chilango chimene adzalandire. Zimenezi zinapangitsa kuti asakhale ndi mlandu wa magazi a anthu amene adzaphedwe. Pochita zimenezi anachenjeza anthu amene anali ku ukapolo kuti Yehova adzalanga anthu ampatuko omwe ali ku Yerusalemu. Komanso anathandiza anthu omwe anali ku ukapolo ku Babulo kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso kuti akhale okonzeka kudzagwira ntchito m’tsogolo. Zaka 70 za ukapolo zikadzatha, anthu amene anali ku ukapolowo, Yehova adzawabwezeretsa ku dziko la Isiraeli. (Ezek. 36:7-11) Anthu amene adzabwerere kwawowo kwenikweni adzakhala ana ndi zidzukulu za anthu amene anamvera chenjezo la Ezekieli. Monga mmene mitu ina m’gawo 3 la buku lino ikusonyezera, Ezekieli anali ndi zinthu zambiri zabwino zoti auze anthu, zotsimikizira kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa ku Yerusalemu.

17. Kodi Yehova anasankha liti alonda?

17 Kodi aneneri amenewa omwe ankalankhula ndi anthu a Mulungu Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa mu 607 B.C.E., ndi okhawo amene Yehova anawagwiritsa ntchito kuti akhale ngati alonda? Yankho ndi lakuti ayi. Nthawi zonse pakakhala zochitika zapadera zokwaniritsa cholinga cha Mulungu, Yehova ankaika alonda kuti achenjeze anthu oipa komanso kulengeza uthenga wabwino.

Alonda a M’nthawi ya Yesu

18. Kodi Yohane M’batizi anagwira ntchito yotani?

18 M’nthawi ya Yesu, Yohane M’batizi anagwira ntchito ya mlonda. Iye ankachenjeza Ayuda kuti akanidwa pasanapite nthawi yaitali. (Mat. 3:1, 2, 9-11) Koma sizokhazo zimene anachita. Yesu ananena kuti Yohane anali “mthenga” amene malemba ananeneratu kuti adzakonza njira ya Mesiya. (Mal. 3:1; Mat. 11:7-10) Zina zimene anachita zikuphatikizapo kulengeza uthenga wabwino wakuti, “Mwanawankhosa wa Mulungu” yemwe ndi Yesu wafika ndipo “akuchotsa uchimo wa dziko.”​—Yoh. 1:29, 30.

19, 20. Kodi Yesu ndi ophunzira ake anagwira ntchito bwanji ngati alonda?

19 Pa alonda onse, Yesu anali mlonda wamkulu. Mofanana ndi Ezekieli, iye anatumidwa ndi Yehova ku “nyumba ya Isiraeli.” (Ezek. 3:17; Mat. 15:24) Yesu anachenjeza kuti mtundu wa Isiraeli unali utatsala pang’ono kukanidwa komanso kuti Yerusalemu adzawonongedwa. (Mat. 23:37, 38; 24:1, 2; Luka 21:20-24) Koma ntchito yake yaikulu inali yolengeza uthenga wabwino.​—Luka 4:17-21.

20 Yesu ali padziko lapansi anauza ophunzira ake mosapita m’mbali kuti: “Khalanibe maso.” (Mat. 24:42) Ophunzirawo anamvera zimene Yesu anawalamula ndipo anagwira ntchito ngati alonda. Iwo ankachenjeza anthu kuti Yehova anakana nyumba ya Isiraeli komanso mzinda wa Yerusalemu wapadziko lapansi. (Aroma 9:6-8; Agal. 4:25, 26) Mofanana ndi alonda omwe analiko iwo asanakhaleko, nawonso anali ndi uthenga wabwino woti alengeze. Uthenga wawo unaphatikizapo chilengezo chapadera chakuti anthu a mitundu ina tsopano ali ndi mwayi wokhala m’gulu la Isiraeli wa Mulungu, yemwe ndi wopangidwa ndi Akhristu odzozedwa, ndipo adzasangalala ndi mwayi wothandiza Khristu pobwezeretsa kulambira koyera padziko lapansi.​—Mac. 15:14; Agal. 6:15, 16; Chiv. 5:9, 10.

21. Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani?

21 Pa gulu la alonda a m’nthawi ya atumwi, mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino. Iye ankaona kuti udindo wake ndi wofunika kwambiri. Mofanana ndi Ezekieli, iye ankadziwa kuti adzakhala ndi mlandu wamagazi ngati atalephera kukwaniritsa utumiki wake. (Mac. 20:26, 27) Mofanana ndi zimene alonda ena ankachita, Paulo sankangochenjeza anthu ena koma ankalengezanso uthenga wabwino. (Mac. 15:35; Aroma 1:1-4) Ndipotu motsogoleredwa ndi mzimu woyera, iye ananena mawu amene Yesaya analemba kuti: “Mapazi a munthu amene akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino ndi okongola kwambiri.” Ndipo ananena kuti zimenezi ndi zimene otsatira Khristu akuchita polalikira zokhudza Ufumu wa Mulungu.​—Yes. 52:7, 8; Aroma 10:13-15.

22. Kodi chinachitika n’chiyani atumwi atamwalira?

22 Atumwi onse atamwalira, mpatuko umene ananeneratu kuti udzachitika, unasokoneza mpingo wa Chikhristu. (Mac. 20:29, 30; 2 Ates. 2:3-8) Pa nthawi yaitali imene mbewu zinkakula, Akhristu achinyengo omwe anali ngati namsongole anachuluka kuposa otsatira a Khristu amene anali ngati tirigu ndipo uthenga womveka bwino wokhudza Ufumu wa Mulungu unaphimbika chifukwa cha ziphunzitso zabodza. (Mat. 13:36-43) Koma nthawi itakwana kuti Yehova alowerere pa zochita za anthu, anasonyezanso chikondi ndi chilungamo chake posankha alonda kuti apereke chenjezo lomveka bwino komanso kulengeza uthenga wabwino. Kodi alonda amenewa anali ndani?

Yehova Anasankhanso Alonda Kuti Achenjeze Anthu Oipa

23. Kodi C. T. Russell ndi anzake anagwira ntchito yotani?

23 Chaka cha 1914 chisanafike, Charles Taze Russell ndi anzake, anali ngati “mthenga” amene anakonza njira Ufumu wa Mesiya usanakhazikitsidwe. b (Mal. 3:1) Gulu limenelo linkagwira ntchito ngati mlonda ndipo ankagwiritsa ntchito magazini a Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence pochenjeza anthu za chiweruzo cha Yehova komanso kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

24. (a) Kodi kapolo wokhulupirika akugwira ntchito bwanji ngati mlonda? (b) Kodi mwaphunzira chiyani pa chitsanzo cha alonda akale? (Onani tchati chakuti “Alonda Ena Achitsanzo Chabwino.”)

24 Ufumu utakhazikitsidwa, Yesu anasankha kagulu kakang’ono ka amuna kuti atumikire monga kapolo wokhulupirika. (Mat. 24:45-47) Kuyambira nthawi imeneyo, kapolo wokhulupirika amene panopa amadziwikanso kuti Bungwe Lolamulira, wakhala akugwira ntchito ngati mlonda. Bungwe Lolamulirali lakhala likutsogolera pa ntchito yochenjeza anthu za “tsiku lobwezera” komanso kulengeza za “chaka cha Yehova chokomera anthu mtima.”​—Yes. 61:2; 2 Akor. 6:1, 2.

25, 26. (a) Kodi otsatira onse a Khristu akufunika kugwira ntchito yotani ndipo ntchitoyo imagwiridwa bwanji? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu wotsatira?

25 Pamene kapolo wokhulupirika akutsogolera pa ntchito ya mlonda, Yesu akuchenjeza otsatira ake “onse,” kuti apitirizebe ‘kukhala maso.’ (Maliko 13:33-37) Timamvera lamulo limeneli pokhalabe maso mwauzimu n’kumathandiza mokhulupirika mlonda wa masiku ano. Timasonyeza kuti tili maso tikamakwaniritsa udindo wathu wolalikira. (2 Tim. 4:2) Kodi n’chiyani chimene chimatilimbikitsa kugwira ntchito imeneyi? Mwa zina n’chifukwa chakuti timafunitsitsa kupulumutsa anthu. (1 Tim. 4:16) Posachedwapa anthu ambiri aphedwa chifukwa chakuti akunyalanyaza chenjezo limene mlonda wamasiku ano akupereka. (Ezek. 3:19) Koma cholinga chachikulu chimene timagwirira ntchito imeneyi ndi kuuza ena uthenga wabwino wakuti kulambira koyera kwabwezeretsedwa. Panopa ‘m’chaka cha Yehova chokomera anthu mtima,’ khomo ndi lotseguka kuti anthu ambiri abwere kudzalambira nafe Yehova Mulungu wathu, amene ndi wachilungamo komanso wachikondi. Posachedwapa, anthu onse omwe adzapulumuke dziko loipali likamadzawonongedwa, adzasangalala ndi ulamuliro wachifundo wa Mwana wake Khristu Yesu. Sitingalephere ngakhale pang’ono kuthandiza mlonda wamasiku anoyu pouza anthu uthenga wabwino umenewu.​—Mat. 24:14.

Timathandiza mlonda wamasiku ano mosangalala tikamalalikira uthenga wabwino (Onani ndime 25)

26 Ngakhale panopa dziko loipali lisanathe, Yehova wagwirizanitsa anthu ake m’njira yodabwitsa. Mutu wotsatira udzafotokoza ulosi wokhudza ndodo ziwiri umene umafotokoza mmene zimenezi zachitikira.

a M’buku la Yeremiya, mawu akuti “tsoka” amapezeka malo pafupifupi 60.

b Kuti mudziwe zokhudza ulosiwu komanso mmene unakwaniritsidwira, onani buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulira, mutu 2 wakuti, “Ufumu Wakhazikitsidwa Kumwamba.”