Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 12

“Ndidzawachititsa Kuti Akhale Mtundu Umodzi”

“Ndidzawachititsa Kuti Akhale Mtundu Umodzi”

EZEKIELI 37:22

MFUNDO YAIKULU: Lonjezo la Yehova lakuti adzasonkhanitsa anthu ake pamodzi; ulosi wokhudza ndodo ziwiri

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani anthu amene anali ku ukapolo ayenera kuti ankachita mantha? (b) N’chifukwa chiyani zimene Ezekieli anachita zinawadabwitsa? (c) Kodi tikambirana mafunso ati?

 Motsogoleredwa ndi Mulungu, Ezekieli anapereka maulosi angapo kwa Ayuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo pogwiritsa ntchito zizindikiro. Mu ulosi woyamba, Ezekieli anachita zinthu zimene zinali ndi uthenga wachiweruzo. Anachitanso zomwezo mu ulosi wachiwiri, wachitatu ndi maulosi ena onse. (Ezek. 3:24-26; 4:1-7; 5:1; 12:3-6) Ndipotu zizindikiro zonse zimene Ezekieli anachita zinali ndi uthenga woopsa wa chilango chimene Ayuda analandira.

2 Ndiye tangoganizani mmene Ayuda amene anali ku ukapolowo anachitira mantha pamene Ezekieli anaimirira patsogolo pawo kuti achite zinthu zina zokhudza ulosi. Iwo ayenera kuti ankadzifunsa kuti, ‘Kodi pano ndiye atiuza uthenga woopsa wotani? Koma zimene anachita zinawadabwitsa. Zinthu zokhudza ulosi zimene tsopano Ezekieli akuchita ndi zosiyana kwambiri ndi zimene wakhala akuchita. Iye sanachite zinthu zimene zinkasonyeza uthenga wa chiweruzo choopsa koma anachita zinthu zimene zinkapereka lonjezo losangalatsa. (Ezek. 37:23) Koma kodi Ezekieli anapereka uthenga wotani kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo? Kodi uthengawo unkatanthauza chiyani? Kodi umakhudza bwanji atumiki a Mulungu masiku ano? Tiyeni tione.

“Iwo Adzakhala Ndodo Imodzi M’dzanja Langa”

3. (a) Kodi “ndodo ya Yuda” inkaimira chiyani? (b) N’chifukwa chiyani “ndodo ya Efuraimu” inkaimira ufumu wa mafuko 10?

3 Yehova anauza Ezekieli kuti atenge ndodo ziwiri ndipo pa ndodo imodzi alembepo kuti, “ndodo ya Yuda” pamene pa ndodo inayo alembepo kuti, “ndodo ya Yosefe yoimira Efuraimu.” (Werengani Ezekieli 37:15, 16.) Kodi ndodo ziwiri zimenezi zinkaimira chiyani? Ndodo “ya Yuda” inkaimira ufumu wa mafuko awiri a Yuda ndi Benjamini. Mafumu ochokera mumzera wa Yuda ankalamulira mafuko awiriwa komanso ansembe ankachokera m’mafuko omwewa chifukwa ankatumikira ku kachisi ku Yerusalemu. (2 Mbiri 11:13, 14; 34:30) Choncho mzera wachifumu wa Davide komanso ansembe omwe anali Alevi ankachokera mu ufumu wa Yuda. ‘Ndodo ya Efuraimu’ inkaimira ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10. N’chifukwa chiyani ndodo imeneyi inkanenedwa kuti ndi ya Efuraimu? Chifukwa chakuti mfumu yoyamba ya ufumu wa mafuko 10 anali Yerobowamu amene ankachokera mu fuko la Efuraimu. Patapita nthawi, fuko la Efuraimu linakhala lotchuka kwambiri mu Isiraeli. (Deut. 33:17; 1 Maf. 11:26) Onani kuti mu ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli, munalibe mafumu ochokera m’banja la Davide kapena ansembe omwe anali Alevi.

4. Kodi zimene Ezekieli anachita ndi ndodo ziwiri zija zikuimira chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Mulungu anauzanso Ezekieli kuti aike ndodo ziwirizo pamodzi, “kuti zikhale ndodo imodzi.” Pamene Ayuda amene anali ku ukapolowo ankaonerera zimene Ezekieli ankachita, anali ndi nkhawa. Ndiyeno anamufunsa kuti: “Kodi sutiuza kuti zinthu zimenezi zikutanthauza chiyani?” Iye anayankha kuti zimene anachitazo zinkasonyeza zimene Yehova adzachite. Ponena za ndodo ziwirizo Yehova anati: ‘Ndidzaziphatikiza ndipo idzakhala ndodo imodzi. Iwo adzakhala ndodo imodzi mʼdzanja langa.’​—Ezek. 37:17-19.

5. Kodi zimene Ezekieli anachita zinkatanthauza chiyani? (Onani bokosi lakuti “Kuphatikiza Ndodo Ziwiri.”)

5 Kenako Yehova anafotokoza zimene kuphatikiza ndodo ziwirizo kunkatanthauza. (Werengani Ezekieli 37:21, 22.) Anthu ochokera mu ufumu wa Yuda wa mafuko awiri amene anali ku ukapolo komanso anthu ochokera mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 (Efuraimu) adzawabweretsa ku dziko la Isiraeli kumene adzakhale “mtundu umodzi.”​—Yer. 30:1-3; 31:2-9; 33:7.

6. Kodi ndi maulosi ena ati amene akupezeka mu Ezekieli chaputala 37?

6 Maulosi ofanana okhudza kubwezeretsa amene analembedwa mu Ezekieli chaputala 37 ndi ochititsa chidwi kwambiri. Yehova adzasonyeza kuti ali ndi mphamvu zobwezeretsa moyo (vesi 1-14) komanso ali ndi mphamvu zobwezeretsa mgwirizano (vesi 15-28). Uthenga wokhudza mtima umene uli m’maulosi awiri amenewa ndi wakuti: Anthu amene anafa, adzakhalanso ndi moyo komanso anthu amene sagwirizana, adzagwirizananso.

Kodi Yehova ‘Anawasonkhanitsa Bwanji Pamodzi’?

7. Kodi nkhani yopezeka pa 1 Mbiri 9:2, 3 ikutsimikizira bwanji kuti “zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu”?

7 Malinga ndi kuona kwa anthu, zingaoneke ngati n’zosatheka kuchotsa anthu ku ukapolo komanso kuwathandiza kuti akhale ogwirizana. a Komabe “zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.” (Mat. 19:26) Yehova anakwaniritsa ulosi wake. Ukapolo wa ku Babulo unatha mu 537 B.C.E., ndipo kenako anthu amene anali m’maufumu awiri onsewa anafika ku Yerusalemu n’kuthandiza nawo kubwezeretsa kulambira koona. Malemba ouziridwa amatitsimikizira kuti: “Mbadwa zina za Yuda, za Benjamini, za Efuraimu ndi za Manase zinkakhala ku Yerusalemu.” (1 Mbiri 9:2, 3; Ezara 6:17) Ndithudi, mogwirizana ndi zimene Yehova analosera, anthu amene anali mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 anaphatikizidwa kapena kuti kugwirizanitsidwa ndi anthu amene anali mu ufumu wa Yuda wa mafuko awiri.

8. (a) Kodi Yesaya analosera chiyani? (b) Kodi ndi mfundo zina zofunika ziti zimene zikupezeka pa Ezekieli 37:21?

8 Zaka 200 zimenezi zisanachitike, mneneri Yesaya analosera zimene zidzachitikire Aisiraeli ndi Ayuda pambuyo pa ukapolo. Iye analosera kuti Yehova adzayamba kusonkhanitsa “Aisiraeli omwe anamwazikana” komanso “Ayuda omwe anabalalika kuchokera kumakona 4 a dziko lapansi,” kuphatikizapo ‘ochokera kudziko la Asuri.’ (Yes. 11:12, 13, 16) Zoonadi, monga mmene Yehova ananenera, iye anatenga “Aisiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina.” (Ezek. 37:21) Taonani mfundo ziwiri zofunika izi: Pa nthawiyi, Yehova sakutchulanso anthu omwe anali ku ukapolo ngati “Yuda” ndi “Efuraimu” koma ngati “Aisiraeli” lomwe ndi gulu limodzi. Kuwonjezera pamenepo sakunena kuti Aisiraeliwo akuchokera mu mtundu umodzi wa Ababulo koma kumitundu yosiyanasiyana, tingoti “kuchokera kumbali zonse.”

9. Kodi Yehova anathandiza bwanji Ayuda amene anabwerera kwawo kuti akhale ogwirizana?

9 Anthu amene anali ku ukapolowo atabwerera ku Isiraeli, kodi Yehova anawathandiza bwanji kuti akhale ogwirizana? Iye anapatsa Aisiraeliwo abusa auzimu ngati Zerubabele, Mkulu wa Ansembe Yoswa, Ezara ndi Nehemiya. Mulungu anasankhanso aneneri monga Hagai, Zekariya ndi Malaki. Amuna okhulupirika onsewa anagwira ntchito mwakhama polimbikitsa mtundu wonsewo kuti uzitsatira malangizo a Mulungu. (Neh. 8:2, 3) Kuwonjezera pamenepo, Yehova anateteza mtundu wa Isiraeli pogonjetsa adani a Mulungu amene ankakonzera chiwembu anthu akewo.​—Esitere 9:24, 25; Zek. 4:6.

Yehova anapereka abusa auzimu kuti athandize anthu ake kukhala ogwirizana (Onani ndime 9)

10. Kodi pamapeto pake Satana anakwanitsa kuchita chiyani?

10 Komabe ngakhale kuti Yehova anawathandiza m’njira yachikondi, Aisiraeli ambiri anasiya kulambira koyera. Zimene anachitazo zinalembedwa m’mabuku a m’Baibulo amene analembedwa Aisiraeliwo atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo. (Ezara 9:1-3; Neh. 13:1, 2, 15) Ndipotu zaka 100 zisanathe kuchokera pamene anabwerera kwawo, Aisiraeliwo anali atatalikirana kwambiri ndi kulambira koyera moti Yehova anawalimbikitsa kuti: “Bwererani kwa ine.” (Mal. 3:7) Pa nthawi imene Yesu anabwera padziko lapansi, chipembedzo cha Ayuda chinali chitagawanika n’kukhala timagulu tambiri timene tinkatsogoleredwa ndi abusa osakhulupirika. (Mat. 16:6; Maliko 7:5-8) Satana anali atakwaniritsa cholinga chake polepheretsa Ayudawo kuti akhale ogwirizana m’mbali zonse. Ngakhale zinali choncho, ulosi wa Yehova wakuti anthu ake adzakhalanso ogwirizana udzakwaniritsidwa ndithu. Kodi udzakwaniritsidwa bwanji?

“Mtumiki Wanga Davide Adzakhala Mfumu Yawo”

11. (a) Kodi Yehova ananena chiyani zokhudza ulosi wakuti anthu ake adzakhala ogwirizana? (b) Kodi Satana anayesanso kuchita chiyani atathamangitsidwa kumwamba?

11 Werengani Ezekieli 37:24. Yehova anasonyeza kuti ulosi wake wakuti anthu ake adzakhala ogwirizana udzakwaniritsidwa wonse pakati pa anthu ake pambuyo poti ‘mtumiki wake Davide,’ yemwe ndi Yesu, wayamba kulamulira monga Mfumu ndipo zimenezi zinachitika mu 1914. b (2 Sam. 7:16; Luka 1:32) Pofika nthawi imeneyi, mtundu weniweni wa Isiraeli unali utalowedwa m’malo ndi Isiraeli wauzimu, yemwe ndi Akhristu odzozedwa. (Yer. 31:33; Agal. 3:29) Satana atamuthamangitsa kumwamba, anachitanso zinthu zina zofuna kusokoneza mgwirizano wa anthu a Mulungu. (Chiv. 12:7-10) Mwachitsanzo M’bale Russell atamwalira mu 1916, Satana anagwiritsa ntchito anthu ampatuko pofuna kugawanitsa Akhristu odzozedwa. Koma pasanapite nthawi, ampatukowo anachoka m’gulu. Satana anachititsanso kuti abale amene ankatsogolera gulu pa nthawiyo, atsekeredwe m’ndende koma zimenezinso sizinachititse kuti anthu a Yehova athe. Abale odzozedwa amene anakhalabe okhulupirika kwa Yehova anapitiriza kukhala ogwirizana.

12. N’chifukwa chiyani zimene Satana ankafuna zogawanitsa Isiraeli wauzimu zinalephereka?

12 Choncho mosiyana ndi zimene zinachitikira Isiraeli weniweni, Isiraeli wauzimu sanalole kuti zochita za Satana zimugawanitse. N’chifukwa chiyani Satana walephera kukwaniritsa zolinga zake? Chifukwa chakuti odzozedwa akhala akuyesetsa kutsatira mfundo za Yehova. Zotsatira zake akhala akutetezedwa ndi Mfumu yawo Yesu Khristu, amene akupitirizabe kugonjetsa Satana.​—Chiv. 6:2.

Yehova Adzachititsa Kuti Olambira Ake ‘Akhale Amodzi’

13. Kodi ulosi wokhudza kuphatikizidwa kwa ndodo ziwiri ukutiphunzitsa mfundo za choonadi zofunika ziti?

13 Kodi ulosi wokhudza kuphatikizidwa kwa ndodo ziwiri ukutanthauza chiyani masiku ano? Kumbukirani kuti cholinga cha ulosiwu n’kusonyeza mmene magulu onsewa adzakhalire ogwirizana. Ndipotu kuposa zonse, ulosiwu ukusonyeza kuti Yehova ndi amene adzachititse kuti mgwirizano umenewu utheke. Ndiye kodi ulosi umenewu wokhudza kuphatikizidwa kwa ndodo ziwiri, ukusonyeza mfundo ya choonadi yofunika iti yokhudza kulambira koyera? Mwachidule mfundo yake ndi yakuti: Yehova ndi amene adzachititse kuti olambira ake ‘akhale amodzi.’​—Ezek. 37:19.

14. Kuyambira mu 1919, kodi ulosi wokhudza kuphatikizidwa kwa ndodo ziwiri wakwaniritsidwa bwanji m’njira yaikulu?

14 Kungoyambira mu 1919, pambuyo poti anthu a Mulungu ayeretsedwa mwauzimu ndipo ayamba kulowa mu paradaiso wauzimu, ulosi wokhudza kuphatikiza ndodo ziwiri unayamba kukwaniritsidwa m’njira yaikulu. Pa nthawi imeneyo, anthu ambiri amene anagwirizanitsidwa anali ndi chiyembekezo chodzakhala mafumu ndi ansembe kumwamba. (Chiv. 20:6) Mophiphiritsa, odzozedwa amenewa anali ngati “ndodo ya Yuda” womwe ndi mtundu umene munkachokera mafumu a m’banja la Davide komanso ansembe omwe anali Alevi. Koma patapita nthawi Akhristu ambiri omwe anali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padziko lapansi anayamba kugwirizana ndi Akhristu odzozedwa. Anthu amenewa anali ngati ‘ndodo ya Efuraimu’ womwe ndi mtundu umene unalibe mafumu ochokera mumzera wa mafumu a m’banja la Davide komanso ansembe omwe anali Alevi. Onse pamodzi magulu awiriwa akutumikira Yehova mogwirizana motsogoleredwa ndi mfumu imodzi Yesu Khristu.​—Ezek. 37:24.

“Iwo Adzakhala Anthu Anga”

15. Kodi ulosi wopezeka pa Ezekieli 37:26, 27 ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

15 Ulosi wa Ezekieli ukusonyeza kuti anthu ambiri adzagwirizana ndi odzozedwa n’kuyamba kulambira koyera. Ponena za anthu ake Yehova ananena kuti: “Ine . . . ndidzawachulukitsa” ndipo “tenti yanga idzawaphimba.”(Ezek. 37:26, 27; mawu am’munsi.) Mawu amenewa akutikumbutsa zimene Yehova analosera kudzera mwa mtumwi Yohane zaka 700 pambuyo pa nthawi ya Ezekieli. Iye anati, ‘Amene wakhala pampando wachifumuyo adzaphimba [“khamu lalikulu”] ndi tenti yake kuti aliteteze.’ (Chiv. 7:9, 15) Masiku ano a khamu lalikulu komanso odzozedwa akukhala monga mtundu umodzi, anthu a Mulungu omwe ndi otetezeka mutenti yake.

16. Kodi Zekariya ananena ulosi wotani wokhudza kugwirizana kwa Isiraeli wauzimu ndi anthu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko lapansi?

16 Nayenso Zekariya, amene anali m’gulu la anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo, analoseranso za kugwirizana kwa Ayuda auzimu ndi anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. Iye ananena kuti: ‘Amuna 10 ochokera m’mitundu ina adzagwira mkanjo wa Myuda nʼkunena kuti: “Anthu inu tikufuna tipite nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”’ (Zek. 8:23) Mawu akuti “Myuda” sakunena za munthu mmodzi koma gulu la anthu chifukwa akunena kuti “anthu inu.” Masiku ano gulu limeneli likuimira Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi kapena kuti Ayuda auzimu. (Aroma 2:28, 29) “Amuna 10” akuimira anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. Iwo ‘agwira’ mwamphamvu odzozedwa ndipo ‘akupita’ nawo limodzi. (Yes. 2:2, 3; Mat. 25:40) Mawu akuti ‘kugwira’ mwamphamvu komanso akuti ‘kupita limodzi’ akusonyeza kuti magulu awiriwa ndi ogwirizana kwambiri.

17. Kodi Yesu anafotokoza bwanji mgwirizano umene tikusangalala nawo panopa?

17 N’kutheka kuti Yesu ankaganizira za ulosi wa Ezekieli wonena za kugwirizana kwa anthu a Mulungu pamene ananena kuti iye ndi m’busa amene akutsogolera nkhosa zake. Nkhosa zimenezi ndi odzozedwa komanso “nkhosa zina,” omwe ndi anthu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko lapansi, ndipo ananena kuti magulu awiriwa adzakhala “gulu limodzi.” (Yoh. 10:16; Ezek. 34:23; 37:24, 25) Mawu a Yesu amenewa komanso a aneneri akale akufotokoza za mgwirizano wauzimu wodabwitsa womwe tikusangalala nawo panopa mosaganizira chiyembekezo chimene tili nacho. Chipembedzo chonyenga chagawanika n’kukhala timagulu tosawerengeka koma ife tikusangalala ndi mgwirizano wodabwitsa.

Masiku ano odzozedwa ndi a “nkhosa zina” akulambira Yehova mogwirizana monga “gulu limodzi” (Onani ndime 17)

“Malo Anga Opatulika Adzakhala Pakati Pawo Mpaka Kalekale”

18. Mogwirizana ndi Ezekieli 37:28, n’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti anthu a Mulungu asakhale “mbali ya dziko”?

18 Mawu omalizira mu ulosi wa Ezekieli okhudza mgwirizano wa anthu a Mulungu akusonyeza zimene zimatitsimikizira kuti mgwirizano wathuwu sudzatha. (Werengani Ezekieli 37:28.) Anthu a Yehova ndi ogwirizana chifukwa chakuti malo ake opatulika kapena kuti kulambira koyera kuli “pakati pawo.” Malo opatulikawo adzapitirizabe kukhala pakati pawo ngati iwo angapitirize kukhala oyera kapena kuti osiyana ndi dziko la Satanali. (1 Akor. 6:11; Chiv. 7:14) Yesu anatsindika kufunika kokhala osiyana ndi dzikoli. Popempherera ophunzira akewo kuchokera pansi pamtima iye anati: “Atate Woyera, ayangʼanireni . . . kuti akhale amodzi . . . “Iwo sali mbali ya dziko . . . Ayeretseni pogwiritsa ntchito choonadi.” (Yoh. 17:11, 16, 17) Onani mmene Yesu anagwirizanitsira kukhala “amodzi” ndi kusakhala “mbali ya dziko.”

19. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timatsanzira Mulungu’? (b) Usiku womaliza asanaphedwe, kodi Yesu anatsindika mfundo yofunika iti yokhudza mgwirizano?

19 Ndi malo awa okha m’Baibulo pamene Yesu anatchula Mulungu kuti “Atate Woyera.” Yehova ndi woyera kwambiri komanso wolungama. Yehova analamula Aisiraeli akale kuti: “Muzikhala oyera, chifukwa ine ndine woyera.” (Lev. 11:45) Popeza ‘timatsanzira Mulungu,’ tikuyenera kumvera lamulo limeneli pa zochita zathu zonse. (Aef. 5:1; 1 Pet. 1:14, 15) Tikamanena za anthu, kukhala “oyera,” kumatanthauza kukhala “opatulika.” Choncho usiku womaliza Yesu asanafe, anauza ophunzira ake kuti adzakhala ogwirizana ngati atakhala osiyana ndi dzikoli lomwe ndi logawanitsa anthu.

“Muwateteze kwa Woipayo”

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani timakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzatiteteza? (b) Kodi ndinu ofunitsitsa kuchita chiyani?

20 Mgwirizano wochititsa chidwi umene umaonekera pakati pa anthu a Yehova masiku ano, umasonyeza kuti Yehova anayankha pemphero la Yesu lakuti: “Muwateteze kwa woipayo.” (Werengani Yohane 17:14, 15.) Zoonadi, tikaona kuti Satana walephera kuwononga mgwirizano wa anthu a Mulungu, tizikhulupirira kwambiri kuti Mulungu akutiteteza. Mu ulosi wa Ezekieli, Yehova ananena kuti ndodo ziwirizo zidzakhala ndodo imodzi m’dzanja lake. Choncho modabwitsa, Yehova wagwirizanitsa anthu ake ndipo akuwateteza ndi dzanja lake moti Satana sangawakhudze.

21 Ndiye kodi tikhale otsimikiza kuchita chiyani? Tikhale otsimikiza kuti tipitiriza kuyesetsa mwakhama kuthandiza kuti mgwirizano wamtengo wapatali umene tikusangalala nawo upitirire. Kodi ndi njira iti imene aliyense angachitire zimenezi? Tiziyesetsa kuchita zinthu zokhudza kulambira koyera m’kachisi wauzimu wa Yehova. M’mitu yotsatira tidzakambirana zimene kulambira kumeneku kumafuna.

a Zaka pafupifupi 200 Ezekieli asanauzidwe ulosiwu, anthu amene ankakhala mu ufumu wa mafuko 10 (“ndodo ya Efuraimu”) anatengedwa ndi Asuri kupita ku ukapolo.​—2 Maf. 17:23.

b Ulosi umenewu wafotokozedwa mwatsatanetsatane m’Mutu 8 wa buku lino.