Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 8

“Ndidzazipatsa Mʼbusa Mmodzi”

“Ndidzazipatsa Mʼbusa Mmodzi”

EZEKIELI 34:23

MFUNDO YAIKULU: Maulosi 4 okhudza Mesiya komanso mmene Khristu anawakwaniritsira

1-3. N’chifukwa chiyani Ezekieli anakhumudwa, ndipo kodi anauziridwa kuti alembe chiyani?

 M’CHAKA cha 6 mneneri Ezekieli ali ku ukapolo, a ankakhumudwa kwambiri akaganizira mmene zinthu zinaipira pa nkhani ya ulamuliro kwawo ku Yuda, dziko limene ankalikonda kwambiri lomwe linali kutali. M’nthawi yake, anaona mafumu osiyanasiyana akulamulira Yuda.

2 Ezekieli anabadwa mkatikati mwa ulamuliro wa Yosiya, yemwe anali mfumu yokhulupirika. Ezekieli ayenera kuti anasangalala atamva zimene Yosiya anachita powononga mafano n’kubwezeretsa kulambira koyera mu Yuda. (2 Mbiri 34:1-8) Koma zimene Yosiya anachita sizinakhalitse chifukwa mafumu amene anabwera pambuyo pake anapitiriza kulambira mafano. N’zosadabwitsa kuti pa nthawi imene mafumu oipawo ankalamulira, Aisiraeli ankachita makhalidwe ambiri oipa ndipo sanalinso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Koma kodi panali chiyembekezo chilichonse choti anthuwa adzasintha? Inde.

3 Yehova anauzira mneneri wake wokhulupirika kuti alembe ulosi woyamba pa maulosi ambiri amene analemba okhudza Mesiya, yemwe m’tsogolo adzakhale Wolamulira komanso M’busa amene adzabwezeretse kwamuyaya kulambira koyera ndiponso kusamalira mwachikondi nkhosa za Yehova. Tingachite bwino kuphunzira maulosi amenewa mosamala chifukwa kuti tidzakhale ndi moyo wosatha, zikudalira kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa. Choncho tiyeni tikambirane maulosi 4 okhudza Mesiya amene akupezeka m’buku la Ezekieli.

“Mphukira Yanthete” Inakhala “Mtengo Waukulu wa Mkungudza”

4. Kodi Ezekieli ananena ulosi wokhudza chiyani, nanga kodi Yehova anayamba kufotokoza bwanji ulosi umenewo?

4 Cha m’ma 612 B.C.E., ‘Yehova analankhula’ ndi Ezekieli ndipo iye ananena ulosi umene umafotokoza za ulamuliro wa Mesiya komanso kufunika koti tizikhulupirira Ufumu wake. Poyamba kufotokoza ulosiwu, Yehova anauza Ezekieli kuti auze Ayuda anzake amene anali nawo ku ukapolo, mawu ophiphiritsa aulosi amene anasonyeza kuti olamulira a ku Yuda anali osakhulupirika komanso anasonyeza kuti anthu akufunikira Mesiya yemwe ndi Wolamulira wolungama.​—Ezek. 17:1, 2.

5. Kodi mfundo yaikulu ya mawu ophiphiritsa amene Ezekieli ananena ndi chiyani?

5 Werengani Ezekieli 17:3-10. Mfundo yaikulu ya mawu ophiphiritsawo ndi yakuti: “Chiwombankhanga chachikulu” chinathyola nsonga ya mtengo wa mkungudza n’kukaidzala “mumzinda umene munali anthu ochita malonda.” Kenako chiwombankhangacho chinatenga “mbewu imodzi mwa mbewu zamʼdzikomo” nʼkuidzala mʼmunda wachonde, “mʼmphepete mwa madzi ambiri.” Mbewuyo inamera ndipo inakula n’kukhala “mtengo wa mpesa . . . wamasamba ambiri.” Kenako “kunabwera chiwombankhanga china chachikulu.” “Mwamsanga” mtengo wa mpesawo unatambasula mizu yake kupita kumene kunali chiwombankhanga chachiwiricho ndipo unkafuna kuti utengedwe ndi chiwombankhangacho n’kukadzalidwa pamadzi ambiri. Yehova anadzudzula mtengo wampesawo chifukwa cha zimene unachitazi ndipo ananena kuti mizu yake idzadulidwa moti mtengowo “udzauma kwambiri.”

Chiwombankhanga chachikulu choyamba chinkaimira Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo (Onani ndime 6)

6. Fotokozani tanthauzo la mawu ophiphiritsa amene Ezekieli ananena?

6 Kodi mawu ophiphiritsawa ankatanthauza chiyani? (Werengani Ezekieli 17:11-15.) Mu 617 B.C.E., Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo (‘chiwombankhanga chachikulu’ choyamba) inaukira Yerusalemu. Iye anathothola Yehoyakini, mfumu ya Yuda (“nsonga yapamwamba penipeni”) kumuchotsa pampando wake wachifumu n’kupita naye ku Babulo (mzinda wa “anthu ochita malonda”). Nebukadinezara anaika Zedekiya (amene anali ‘imodzi mwa mbewu zachifumu zamʼdzikomo’) pampando wachifumu ku Yerusalemu. Mfumu yatsopanoyi anailumbiritsa m’dzina la Mulungu kuti idzakhala yokhulupirika kwa mfumu ya Babulo. (2 Mbiri 36:13) Koma Zedekiya sanasunge lumbiro lake ndipo anagalukira Ababulo n’kupita kukapempha Farao wa ku Iguputo (‘chiwombankhanga chachikulu’ chachiwiri) kuti amuthandize pa nkhondo, koma sizinathandize. Yehova anadzudzula Zedekiya chifukwa chochita zinthu mosakhulupirika polephera kusunga lumbiro. (Ezek. 17:16-21) Zotsatira zake n’zakuti Zedekiya anachotsedwa pampando wachifumu ndipo anakafera m’ndende ku Babulo.​—Yer. 52:6-11.

7. Kodi Mawu ophiphiritsa amenewa akutiphunzitsa chiyani?

7 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yophiphiritsa yaulosiyi? Choyamba, monga anthu amene timalambira Mulungu woona, tiyenera kukwaniritsa zimene talonjeza. Yesu ananena kuti: “Tangotsimikizani kuti mukati ‘Indeʼ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayiʼ akhaledi ayi.” (Mat. 5:37) Ngati pakufunika kuti tilumbire pamaso pa Mulungu kuti tinena zoona, ngati mmene zimakhalira kukhoti, lumbiro limenelo sitimaliona mopepuka. Chachiwiri, tisamangokhulupirira wina aliyense. Baibulo limatichenjeza kuti: “Musamakhulupirire anthu olemekezeka kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso.”​—Sal. 146:3.

8-10. Kodi Yehova anamufotokoza bwanji Mesiya yemwe adzalamulire m’tsogolo, nanga ulosi umenewu unakwaniritsidwa bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “Ulosi Wokhudza Mesiya​—Mtengo Waukulu wa Mkungudza.”)

8 Koma pali wolamulira wina amene tikuyenera kumukhulupirira ndi mtima wonse komanso kumudalira. Atanena nkhani yophiphiritsa yokhudza nsonga imene inakadzalidwa pamalo ena, Yehova anagwiritsa ntchito nkhani yophiphiritsa yomweyo posonyeza kuti m’tsogolo kudzabwera Wolamulira wina amenenso ndi Mesiya.

9 Zimene ulosi umanena. (Werengani Ezekieli 17:22-24.) Apatu zikuoneka kuti Yehova mwiniwakeyo ndi amene adzachitepo kanthu osati ziwombankhanga zazikulu zija. Iye adzabudula mphukira yanthete “yapamwamba penipeni pa mtengo wa mkungudza” nʼkuidzala “pamwamba pa phiri lalitali kwambiri.” Mphukira imeneyi idzamera “nʼkukhala mtengo waukulu wa mkungudza” ndipo “mbalame zamitundu yonse” zidzapeza malo okhala mumtengowo. Zikadzatero, “mitengo yonse yamʼthengo” idzadziwa kuti Yehova ndi amene wachititsa kuti mtengowu umele n’kukhala waukulu.

10 Mmene ulosiwu unakwaniritsidwira. Yehova anabudula Mwana wake, Yesu Khristu, m’banja lachifumu la Davide (“mtengo waukulu wa mkungudza”) n’kukamudzala paphiri la Ziyoni kumwamba (“phiri lalitali kwambiri”). (Sal. 2:6; Yer. 23:5; Chiv. 14:1) Pamenepa Yehova anatenga Mwana wake, amene adani ake ankamuona ngati “munthu wonyozeka kwambiri” ndipo anamukweza pomupatsa “mpando wachifumu wa Davide atate wake.” (Dan. 4:17; Luka 1:32, 33) Mofanana ndi mtengo waukulu wa mkungudza, Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu komanso Mesiya, adzalamulira dziko lonse lapansi ali kumwamba ndipo adzapereka madalitso kwa onse amene azidzawalamulira. Wolamulira woyenera kumudalira ndi ameneyu. Yesu akamadzalamulira monga mfumu, anthu omvera padziko lonse lapansi “adzakhala motetezeka ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”​—Miy. 1:33.

11. Kodi ndi phunziro lofunika liti limene tikuphunzira pa “mphukira yanthete” imene inakhala “mtengo waukulu wa mkungudza”?

11 Zimene tikuphunzira mu ulosiwu. Ulosi wochititsa chidwi wokhudza “mphukira yanthete” imene inakula n’kukhala “mtengo waukulu wa mkungudza” ukutithandiza kuyankha funso lofunika kwambiri lakuti: Kodi tikuyenera kudalira ndani? Kudalira maboma a anthu komanso mphamvu za asilikali awo n’kupusa. Kuti tikhaledi otetezeka, tingachite bwino kudalira komanso kukhulupirira kwambiri Yesu Khristu, amene ndi Mfumu komanso Mesiya. Boma lakumwamba limene wolamulira wake ndi Yesu, ndi boma lokhalo limene lidzakwaniritse zofuna za anthu.​—Chiv. 11:15.

“Amene Ali Woyenerera Mwalamulo”

12. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti sanaiwale pangano lake ndi Davide?

12 Zimene Mulungu ananena potanthauzira ulosi wokhudza ziwombankhanga ziwiri zija zinathandiza Ezekieli kumvetsa kuti Zedekiya, amene anali mfumu yosakhulupirika ya m’banja lachifumu la Davide, adzachotsedwa pa udindo n’kutengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. N’kutheka kuti mneneriyu ankadzifunsa kuti, ‘Kodi pangano limene Mulungu anachita ndi Davide lakuti, mfumu ya m’banja la Davide idzalamulira mpaka kalekale lidzakwaniritsidwa bwanji?’ (2 Sam. 7:12, 16) Ngati Ezekieli ankadzifunsadi funso limeneli, ndiye kuti sipanapite nthawi yaitali kuti apeze yankho. Cha m’ma 611 B.C.E., m’chaka cha 7 Ayuda ali ku ukapolo, Zedekiya akulamulirabe ku Yuda, Yehova analankhula ndi Ezekieli. (Ezek. 20:2) Yehova anamuuza kuti anene ulosi wina wokhudza Mesiya, umene unafotokoza momveka bwino kuti Mulungu sanaiwale pangano limene anachita ndi Davide. Ulosiwo unasonyeza kuti m’tsogolo Mesiya adzakhala woyenerera mwalamulo kutenga mpando wachifumu wa Davide.

13, 14. Kodi ndi Mfundo yaikulu iti imene ili mu ulosi wa pa Ezekieli 21:25-27, ndipo kodi ulosiwo unakwaniritsidwa bwanji?

13 Zimene ulosi umanena. (Werengani Ezekieli 21:25-27.) Kudzera mwa Ezekieli, Yehova analankhula ndi “mtsogoleri wa Isiraeli, amene ndi woipa” ndipo nthawi yoti alandire chilango inali itakwana. Yehova anauza wolamulira woipayo mosapita m’mbali kuti “nduwira” yake komanso “chisoti chachifumu” (zomwe zikuimira mphamvu za ufumu) zidzachotsedwa pa iye. Kenako, amene anali ndi mphamvu zolamulira zochepa anawawonjezera mphamvu ndipo amene anali ndi zambiri zinachepetsedwa. Amene anawawonjezera mphamvu zolamulira aja, anapitiriza kulamulira “mpaka atabwera amene [anali] woyenerera mwalamulo” ndipo Yehova anamupatsa Ufumu.

14 Mmene ulosiwu unakwaniritsidwira. Yerusalemu atawonongedwa mu 607 B.C.E., ufumu wa Yuda umene unali “wolemekezeka,” womwe likulu lake linali ku Yerusalemu, unatsitsidwa pamene Ababulo anawononga mzindawo, kuchotsa Mfumu Zedekiya pa udindo wake n’kumutenga kupita naye ku ukapolo. Zitatero, panalibe mfumu ya m’banja la Davide imene inkalamulira ku Yerusalemu ndipo ulamuliro “wonyozeka” wa anthu amitundu ina unakwezedwa. Ulamuliro umenewu unayamba kulamulira dziko lonse lapansi koma kwa kanthawi kochepa. Nthawi za Akunja kapena kuti “nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo” zinatha mu 1914 pamene Yehova anapereka ufumu kwa Yesu Khristu. (Luka 21:24) Popeza kuti Yesu anali mbadwa ya Mfumu Davide, analidi “woyenerera mwalamulo” kukhala Mfumu komanso Mesiya. b (Gen. 49:10) Choncho kudzera mwa Yesu, Yehova anakwaniritsa zimene analonjeza Davide kuti mbadwa yake idzalamulira mpaka kalekale mu Ufumu womwe sudzatha.​—Luka 1:32, 33.

Yesu ndi woyenerera mwalamulo kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu (Onani ndime 15)

15. N’chiyani chimatipangitsa kuti tizikhulupirira kwambiri mfumu yathu, Yesu Khristu?

15 Zimene tikuphunzira mu ulosiwu. Tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu. Chifukwa chiyani? Chifukwa mosiyana ndi olamulira a m’dzikoli amene amachita kusankhidwa ndi anthu kapena kuchita kulanda ulamuliro, Yesu anasankhidwa ndi Yehova ndipo “anamupatsa . . . ufumu” moti ndi “woyenerera mwalamulo” kulamulira mu ufumu umenewu. (Dan. 7:13, 14) Kunena zoona tikuyeneradi kudalira Mfumu imene Yehova anaisankha.

“Mtumiki Wanga Davide” Adzakhala “Mʼbusa Wawo”

16. Kodi Yehova amaziona bwanji nkhosa zake, nanga mu nthawi ya Ezekieli “abusa a Isiraeli” ankachita bwanji zinthu ndi nkhosa?

16 Yehova yemwe ndi M’busa Wamkulu, amasamalira mwachikondi nkhosa zake kapena kuti anthu amene amamulambira padziko lapansi. (Sal. 100:3) Akapereka udindo wosamalira nkhosazi kwa abusa aang’ono kapena kuti akulu amene ali ndi udindo m’gulu lake, amaonetsetsa mmene abusawo akusamalirira nkhosa zakezo. Ndiye taganizirani mmene Yehova anamvera ndi zimene “abusa a Isiraeli” a m’nthawi ya Ezekieli ankachita. Mopanda manyazi, abusa amenewo ankalamulira “mwankhanza komanso mopondereza.” Zimenezi zinachititsa kuti nkhosa za Mulungu zizivutika ndipo anthu ambiri anasiya kulambira Mulungu woona.​—Ezek. 34:1-6.

17. Kodi Yehova anapulumutsa bwanji nkhosa zake?

17 Kodi Yehova anachita chiyani? Iye anauza olamulira ankhanza a mu Isiraeliwo kuti: “Ndiwauza kuti andibwezere nkhosa zanga.” Ndiyeno analonjeza kuti: “Ndidzalanditsa nkhosa zanga.” (Ezek. 34:10) Nthawi zonse Yehova amakwaniritsa zimene walonjeza. (Yos. 21:45) Mu 607 B.C.E., iye anapulumutsa nkhosa zake pogwiritsa ntchito Ababulo amene anachotsa ulamuliro wa abusa adyerawo. Patapita zake 70, Mulungu analanditsa anthu ake amene anali ngati nkhosa kuchokera ku Babulo n’kuwapititsa kudziko lawo kuti akabwezeretse kulambira koona. Koma nkhosa za Yehova zinkakumanabe ndi mavuto chifukwa zinapitiriza kulamuliridwa ndi mafumu a m’dzikoli. Panapita zaka zambiri “nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo” zisanathe.​—Luka 21:24.

18, 19. Kodi Ezekieli ananena ulosi uti mu 606 B.C.E.? (Onani chithunzi choyambirira.)

18 Mu 606 B.C.E., patadutsa pafupifupi chaka chimodzi kuchokera pamene Yerusalemu anawonongedwa koma kutatsala zaka zambiri kuti Aisiraeli amasulidwe ku ukapolo ku Babulo, Yehova anauzira Ezekieli kuti anene ulosi umene umasonyeza kuti M’busa Wamkulu amasamalira nkhosa zake ndipo amafuna kuti zikhale ndi moyo mpaka kalekale. Ulosiwo umafotokoza mmene Wolamulira yemwenso ndi Mesiya adzawetere nkhosa za Yehova.

19 Zimene ulosi umanena. (Werengani Ezekieli 34:22-24.) Mulungu ananena kuti adzapereka “mʼbusa mmodzi” ndipo anamutchula kuti “mtumiki wanga Davide.” Mawu akuti “mʼbusa mmodzi” komanso akuti “mtumiki,” kutanthauza kuti ndi mmodzi, akusonyeza kuti Wolamulirayu sadzayambitsanso mzera wa mafumu a m’banja la Davide koma ndi iye yekha amene adzakhale pampando wachifumu wa Davide mpaka kalekale. Wolamulira ameneyu yemwenso ndi M’busa adzadyetsa nkhosa za Mulungu ndipo adzakhala “mtsogoleri pakati pawo.” Yehova adzachita “pangano lamtendere” ndi nkhosa zakezo. ‘Madalitso adzawagwera ambiri ngati mvula’ moti adzasangalala chifukwa azidzakhala mwamtendere ndipo zinthu zidzawayendera bwino. Ndipotu mtendere umenewu sudzakhala pakati pa anthu okha koma udzakhalanso pakati pa anthu ndi nyama.​—Ezek. 34:25-28.

20, 21. (a) Kodi ulosi wonena za “mtumiki wanga Davide,” unakwaniritsidwa bwanji? (b) Kodi zimene Ezekieli ananena zokhudza “pangano lamtendere” zikusonyeza kuti m’tsogolomu muchitika zotani?

20 Mmene ulosiwu unakwaniritsidwira. Potchula Wolamulira ameneyu kuti “mtumiki wanga Davide,” Mulungu ankalosera za Yesu yemwe ndi mbadwa ya Davide amene ali woyenerera mwalamulo kukhala wolamulira. (Sal. 89:35, 36) Ali padziko lapansi, Yesu anasonyeza kuti ndi “m’busa wabwino” moti anapereka moyo wake “chifukwa cha nkhosazo.” (Yoh. 10:14, 15) Koma panopa M’busa ameneyu ali kumwamba. (Aheb. 13:20) Mu 1914, Mulungu anapatsa Yesu ufumu komanso udindo woweta ndi kudyetsa nkhosa za Mulungu padziko lapansi. Pasanapite nthawi yaitali, mu 1919 Mfumu yatsopanoyi inasankha “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” kuti azipereka chakudya kwa “antchito ake apakhomo,” omwe ndi atumiki okhulupirika a Mulungu amene akuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi. (Mat. 24:45-47) Motsogoleredwa ndi Khristu, kapolo wokhulupirikayu wakhala akupereka chakudya chauzimu chabwino kwambiri kwa nkhosa za Mulungu. Chakudya chimenechi chathandiza nkhosazi kuti zizikhala mwamtendere komanso motetezeka m’paradaiso wauzimu amene akukulirakulira.

21 Kodi zimene Ezekieli ananena zokhudza “pangano lamtendere” komanso madalitso ambiri amene adzagwe ngati mvula, zikusonyeza kuti m’tsogolomu muchitika zotani? M’dziko latsopano limene likubweralo, anthu amene akulambira Yehova padziko lapansi pano adzasangalala mokwanira ndi madalitso amene adzalandire chifukwa cha “pangano lamtendere.” M’paradaiso weniweni amene adzakhale padziko lonse, anthu okhulupirika sadzachitanso mantha ndi nkhondo, uchigawenga, njala, matenda kapena nyama zakutchire. (Yes. 11:6-9; 35:5, 6; 65:21-23) Kodi simukusangalala mukaganizira kuti mudzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi, pamene nkhosa za Mulungu ‘zidzakhala motetezeka popanda aliyense woziopseza?’​—Ezek. 34:28.

Monga M’busa wakumwamba, Yesu amaona zimene abusa akuchita ndi nkhosa za Mulungu (Onani ndime 22)

22. Kodi Yesu amaziona bwanji nkhosa zake, ndipo kodi abusa aang’ono angamutsanzire bwanji?

22 Zimene tikuphunzira mu ulosiwu. Mofanana ndi Atate ake, Yesu amafuna kuti nkhosa za Mulungu zizisangalala. M’busa ameneyu yomwenso ndi Mfumu amaonetsetsa kuti nkhosa za Atate ake zikudyetsedwa bwino mwauzimu komanso kuti zikukhala mwamtendere ndiponso motetezeka m’paradaiso wauzimu. N’zolimbikitsa kwambiri kusamaliridwa ndi Wolamulira wotere. Onse amene ndi abusa aang’ono ayenera kukonda nkhosa za Mulungu ngati mmene Yesu anazikondera. Akulu ayenera kuweta nkhosa “mofunitsitsa” komanso “ndi mtima wonse” ndipo ayenera kukhala zitsanzo zabwino kwa nkhosazo. (1 Pet. 5:2, 3) M’busa aliyense sakuyenera kuzunza nkhosa iliyonse ya Yehova. Kumbukirani zimene Yehova anauza abusa ankhanza a mu Isiraeli m’masiku a Ezekieli kuti: “Ndiwauza kuti andibwezere nkhosa zanga.” (Ezek. 34:10) M’busa Wamkulu amaonetsetsa zimene abusa akuchita ndi nkhosa zake ndipo Mwana wake amachitanso chimodzimodzi.

“Davide Mtumiki Wanga Adzakhala Mtsogoleri Wawo Mpaka Kalekale”

23. Kodi Yehova analonjeza chiyani pa nkhani yogwirizanitsa mtundu wa Isiraeli, nanga anakwaniritsa bwanji zimene analonjezazo?

23 Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira azitumikira limodzi mogwirizana. Mu ulosi wokhudza kubwezeretsa kulambira koona, Mulungu analonjeza kuti adzasonkhanitsa anthu ake, kapena kuti anthu amene akuimira ufumu wa Yuda wa mafuko awiri komanso ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10. Analonjeza kuti adzagwirizanitsa anthuwa n’kukhala “mtundu umodzi” ndipo zidzakhala ngati akuphatikiza “ndodo” ziwiri kuti zikhale “ndodo imodzi” mʼdzanja lake. (Ezek. 37:15-23) Pokwaniritsa ulosi umenewu, Mulungu anabwezeretsa mtundu wogwirizana wa Isiraeli ku Dziko Lolonjezedwa mu 537 B.C.E. c Koma mgwirizano umenewo unali chitsanzo chochepa chabe cha mgwirizano waukulu komanso wosatha umene ukubwera m’tsogolo. Yehova atalonjeza kuti adzagwirizanitsa Aisiraeli, anapatsa Ezekieli ulosi wosonyeza mmene Wolamulira wam’tsogoloyu adzagwirizanitsire anthu amene akulambira Mulungu woona padziko lonse mu mgwirizano umene udzakhalapo mpaka kalekale.

24. Kodi Yehova anafotokoza bwanji za Mesiya yemwe ndi Wolamulira, ndipo kodi ulamuliro wa Mfumu imeneyi udzakhala wotani?

24 Zimene ulosi umanena. (Werengani Ezekieli 37:24-28.) Yehova akutchulanso Wolamulira ameneyu, yemwenso ndi Mesiya kuti “mtumiki wanga Davide,” “mʼbusa mmodzi” ndi “mtsogoleri.” Koma tsopano Yehova akutchula Wolonjezedwayu kuti “mfumu.” (Ezek. 37:22) Kodi ulamuliro wa Mfumu imeneyi udzakhala wotani? Ulamuliro wake sudzatha. Mawu akuti “mpaka kalekale” akusonyeza kuti madalitso amene ulamuliro wa Mfumuyi udzabweretse sadzatha. d Mu ulamuliro wake mudzakhala mgwirizano. Anthu amene azidzalamuliridwa ndi “mfumu imodzi” imeneyi azidzatsatira “zigamulo” zofanana ndipo “adzakhala mʼdzikomo” mogwirizana. Ulamuliro wake udzachititsa kuti anthu amene akuwalamulirawo ayandikane kwambiri ndi Yehova Mulungu. Yehova adzachita “pangano lamtendere” ndi anthu amenewa. Yehova adzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu ake. Malo ake opatulika adzakhala “pakati pawo mpaka kalekale.”

25. Kodi ulosi wokhudza Mesiya yemwenso ndi Mfumu unakwaniritsidwa bwanji?

25 Mmene ulosiwu unakwaniritsidwira. Mu 1919, Akhristu okhulupirika odzozedwa anasonyeza kuti anali ogwirizana pomvera ‘m’busa wawo mmodzi,’ Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu komanso Mesiya. Pambuyo pake, “khamu lalikulu” lochokera “mʼdziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse” linagwirizana ndi okhulupirira anzawo odzozedwawo. (Chiv. 7:9) Onsewa akhala “gulu limodzi” la nkhosa zimene zikuyang’aniridwa ndi ‘mʼbusa mmodzi.’ (Yoh. 10:16) Kaya akuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansili, onsewa amamvera zigamulo za Yehova. Zimenezi zimachititsa kuti azikhala mogwirizana m’paradaiso wauzimu ngati anthu am’banja limodzi lapadziko lonse. Yehova wawadalitsa powapatsa mtendere, ndipo malo ake opatulika omwe akuimira kulambira koyera, ali pakati pawo. Yehova ndi Mulungu wawo, ndipo iwo amasangalala akamamulambira panopa mpaka kalekale.

26. Kodi tingachite chiyani kuti tilimbikitse mgwirizano umene uli mu paradaiso wauzimu?

26 Zimene tikuphunzira mu ulosiwu. Tili ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala m’banja logwirizana la padziko lonse la abale ndi alongo amene akulambira Mulungu woona Yehova. Koma mwayi umenewu ukutibweretseranso udindo woti tizithandizira kuti mgwirizanowu upitirire. Choncho tonsefe tikuyenera kuchita mbali yathu kuti tisonyeze kuti zimene timakhulupirira komanso zochita zathu n’zofanana. (1 Akor. 1:10) Kuti zimenezo zitheke, timayesetsa kudya chakudya chauzimu chofanana, kutsatira mfundo zofanana za makhalidwe abwino zogwirizana ndi Malemba komanso timagwira ntchito yofanana yolalikira za Ufumu ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Komabe, chimene chimachititsa kuti tizigwirizana kwambiri ndi chikondi. Tikamayesetsa kuchita zinthu zosiyanasiyana zosonyeza chikondi, zomwe zikuphatikizapo kumvera ena chisoni, kusonyeza chifundo komanso kukhululuka, timathandizira kuti tizigwirizana. Baibulo limanena kuti: “Chikondi . . . chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”​—Akol. 3:12-14; 1 Akor. 13:4-7.

Yehova akudalitsa ubale wapadziko lonse wa anthu okondana amene amamulambira (Onani ndime 26)

27. (a) Kodi mukumva bwanji mukaganizira za maulosi okhudza Mesiya amene ali m’buku la Ezekieli? (b)  Kodi m’mitu yotsatira tidzakambirana chiyani?

27 Tikuyamikira kwambiri chifukwa cha maulosi okhudza Mesiya amene akupezeka m’buku la Ezekieli. Tikamawerenga komanso kuganizira mozama maulosi amenewo, timaona kuti Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu yathu yokondedwa, ndi woyenera kumudalira, ndi woyenerera mwalamulo kukhala wolamulira, amatiweta mwachikondi ndipo apitiriza kutithandiza kuti tikhale ogwirizana mpaka kalekale. Tilitu ndi mwayi waukulu kulamuliridwa ndi Mfumu yomwenso ndi Mesiya. Tisaiwale kuti maulosi amenewa okhudza Mesiya ndi mbali ya mfundo yaikulu imene ikufotokozedwa m’buku la m’Baibulo la Ezekieli, yomwe ndi kubwezeretsa kulambira koyera. Kudzera mwa Yesu, Yehova wasonkhanitsa pamodzi anthu ake n’kuwathandiza kuti ayambirenso kulambira koyera. (Ezek. 20:41) M’Mitu yotsatira ya bukuli, tikambirana nkhani yochititsa chidwi yokhudza kubwezeretsa kulambira koyera ndipo tiona mmene buku la Ezekieli lafotokozera nkhani imeneyi.

a Chaka choyamba cha ukapolo chinayamba mu 617 B.C.E. pamene gulu loyamba la Ayuda linatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Choncho chaka cha 6 chinayamba mu 612 B.C.E.

b Mzera wobadwira wa Yesu kudzera mwa Davide unafotokozedwa momveka bwino m’Mauthenga Abwino.​—Mat. 1:1-16; Luka 3:23-31.

c Ulosi wa Ezekieli wokhudza ndodo ziwiri komanso mmene unakwaniritsidwira tidzauphunzira m’Mutu 12 wa bukuli.

d Pofotokoza za mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “mpaka kalekale,” buku lina linati: “Kuwonjezera pa kunena za nthawi, mawuwa amatanthauzanso kuti chinthucho ndi chokhalitsa, chosatha, sichingadetsedwe, sichingachotsedwe komanso sichingasinthe.”