Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 10

“Mudzakhala Amoyo”

“Mudzakhala Amoyo”

EZEKIELI 37:5

MFUNDO YAIKULU: Masomphenya a “mafupa ouma” amene anakhala ndi moyo komanso kukwaniritsidwa kwake kwakukulu

1-3. N’chiyani chimene chinapangitsa kuti Ayuda amene anali ku Babulo ayambe kumva chisoni? (Onani chithunzi choyambirira.)

 ZINTHU zinasintha kwambiri kwa Ayuda amene anali ku Babulo. Kwa zaka 5, Ezekieli anakhala akulosera kuti Yerusalemu adzawonongedwa koma anthuwo sankakhulupirira kuti zimenezi zingachitike. Ngakhale kuti Ezekieli ankachita zizindikiro, kupereka mafanizo komanso kulengeza uthenga, anthu amene anali ku ukapolo aja sankakhulupirira kuti Yehova angalole kuti Yerusalemu awonongedwe. Ngakhale kuti anamva kuti mzinda wa Yerusalemu wazunguliridwa ndi asilikali a Babulo, iwo ankakhulupirirabe kuti anthu amumzindawo akhala motetezeka.

2 Koma patatha zaka ziwiri kuchokera pamene mzindawo unazunguliridwa, munthu wina amene anathawa ku Yerusalemu anafika ku Babulo n’kukanena uthenga wakuti: “Mzinda uja wawonongedwa!” Anthu amene anali ku ukapolowo anakhumudwa kwambiri ndi uthenga umenewu. Sanamvetse kuti mzinda wawo wokondedwa, kachisi wawo woyera komanso dziko limene ankalikonda zawonongedwa. Pamenepatu anagwira fuwa lamoto chifukwa zonse zimene ankaziyembekezera zinatheratu.​—Ezek. 21:7; 33:21.

3 Koma pa nthawi yovutayi, Ezekieli analandira masomphenya opatsa chiyembekezo. Kodi masomphenyawo anali ndi uthenga wotani kwa anthu okhumudwa omwe anali ku ukapolowo? Kodi masomphenyawo akukhudza bwanji anthu a Mulungu masiku ano, nanga kodi ifeyo tingapindule bwanji ndi masomphenyawo? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tione zimene Yehova anauza Ezekieli.

“Losera Zokhudza Mafupa Amenewa” Komanso “Losera kwa Mphepo”

4. Kodi Ezekieli anachita chidwi ndi chiyani m’masomphenya amene anaona?

4 Werengani Ezekieli 37:1-10. M’masomphenya, Ezekieli anamukhazika m’chigwa mmene munali mafupa okhaokha. Yehova analamula mneneriyu kuti ‘ayende’ m’chigwamo n’kuona mafupa amene anali paliponse mmenemo. Zinali ngati kuti Yehova akufuna kutsimikizira kuti Ezekieli wamvetsa tanthauzo la masomphenyawo. Pamene Ezekieli ankayenda m’chigwacho, anachita chidwi ndi zinthu ziwiri zokhudza mafupa: Chiwerengero cha mafupawo komanso mmene ankaonekera. Iye anaona kuti m’chigwamo munali “mafupa ambiri ndipo anali ouma kwambiri.”

5. Kodi Yehova analamula Ezekieli kuti achite zinthu ziwiri ziti, nanga chinachitika n’chiyani Ezekieli atachita zinthu zimenezo?

5 Kenako Yehova anapatsa Ezekieli malamulo awiri amene akanayambitsa ntchito yobwezeretsa imene inkayenera kupitirizabe. Lamulo loyamba linali lakuti: “Losera zokhudza mafupa amenewa” ndipo ankayenera kuwauza kuti ‘akhale ndi moyo.’ (Ezek. 37:4-6) Ezekieli atangolosera, “panamveka phokoso la mafupa kuti gobedegobede! Ndipo mafupawo anayamba kubwera pamodzi nʼkumalumikizana.” Kenako ‘mitsempha ndi mnofu zinakuta mafupawo ndipo khungu linabwera pamwamba pake.’ (Ezek. 37:7, 8) Lamulo lachiwiri linali lakuti: “Losera kwa mphepo” ndipo ankayenera kuiuza kuti ‘iwombe’ pa anthu amene anaphedwawo. Ezekieli atalosera, “mpweya unalowa mwa iwo. Iwo anakhala ndi moyo ndipo anaimirira. Anali gulu lalikulu kwambiri la asilikali.”​—Ezek. 37:9, 10.

“Mafupa Athu Auma Ndipo Tilibenso Chiyembekezo Chilichonse”

6. Kodi ndi mawu ati omwe Yehova analankhula amene anathandiza Ezekieli kumvetsa bwino masomphenyawo?

6 Kenako Yehova anaululira Ezekieli tanthauzo la masomphenyawo kuti: “Mafupawa akuimira nyumba yonse ya Isiraeli.” Ayuda amene anali ku ukapolo atangomva kuti Yerusalemu wawonongedwa, ankangoona ngati afa kale basi. Choncho iwo anadandaula kuti: “Mafupa athu auma ndipo tilibenso chiyembekezo chilichonse. Tatheratu!” (Ezek. 37:11) Koma poyankha, Yehova anasonyeza kuti masomphenya omvetsa chisoni okhudza mafupawa, kwenikweni anali ndi uthenga wosangalatsa wopereka chiyembekezo kwa Aisiraeli.

7. Mogwirizana ndi Ezekieli 37:12-14, kodi Yehova anamuuza chiyani Ezekieli, nanga zimenezo zinapereka chiyembekezo chotani kwa anthu ake amene anali ku ukapolo?

7 Werengani Ezekieli 37:12-14. M’masomphenyawa, Yehova anatsimikizira anthu amene anali ku ukapolo kuti adzawathandiza kukhalanso ndi moyo, adzawatsogolera pobwerera kwawo ndipo adzawalola kuti akhazikike kumeneko. Kuwonjezera pamenepo, Yehova anayamba kuwatchulanso kuti “anthu anga.” Amenewatu anali mawu olimbikitsa kwambiri kwa anthu okhumudwa amene anali ku ukapolowo. N’chifukwa chiyani sakanakayikira kuti lonjezo limeneli loti adzabwereranso kwawo lidzakwaniritsidwa? Chifukwa choti Yehova ndi amene analonjeza. Iye ananena kuti: “Ine Yehova ndinanena zimenezi ndipo ndazichita.”

8. (a) Kodi “nyumba yonse ya Isiraeli” inakhala bwanji ngati yakufa? (b) Kodi lemba la Ezekieli 37:9, likusonyeza kuti n’chiyani chimene chinachititsa kuti Aisiraeli akhale ngati akufa mophiphiritsa? (Onani mawu am’munsi.)

8 Kodi mbali yomvetsa chisoni ya masomphenyawa inakwaniritsidwa bwanji kwa mtundu wakale wa Aisiraeli? Pofika mu 740 B.C.E. ubwenzi wa Aisiraeli ndi Yehova unali utatsala pang’ono kutheratu pamene ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli unawonongedwa anthu n’kutengedwa kupita ku ukapolo. Ndiyeno patatha zaka 130 anthu a ku Yuda nawonso anatengedwa kupita ku ukapolo. Izi zinachititsa kuti “nyumba yonse ya Isiraeli” ikhale ku ukapolo. (Ezek. 37:11) Mophiphiritsa, zinali ngati kuti gulu lonse la anthu amene anali ku ukapolo linali lakufa ngati mmene zinalili ndi mafupa amene Ezekieli anaona m’masomphenya aja. a Komanso kumbukirani kuti Ezekieli sikuti anangoona mafupa koma anaona mafupa “ouma kwambiri” zimene zikusonyeza kuti anthuwa anali ngati akufa kwa nthawi yaitali. Ndipotu zimenezi ndi zoona chifukwa tikaphatikiza nthawi imene Aisiraeli ndi Ayuda anakhala ku ukapolo, ikukwana zaka zoposa 200, kuyambira mu 740 B.C.E. kufika mu 537 B.C.E.​—Yer. 50:33.

9. Kodi zimene zinachitikira Aisiraeli akale zikufanana bwanji ndi zimene zinachitikira “Isiraeli wa Mulungu”?

9 Maulosi obwezeretsa okhudza Aisiraeli ngati amene ananenedwa ndi Ezekieli anakwaniritsidwa m’njira yaikulu. (Mac. 3:21) Mtundu wakale wa Isiraeli unaphedwa, ndipo mophiphiritsa unakhala wakufa kwa nthawi yaitali. Mofanana ndi zimenezi, “Isiraeli wa Mulungu,” yemwe ndi mpingo wa Akhristu odzozedwa, anaphedwa mophiphiritsa ndipo anakhala ku ukapolo kwa nthawi yaitali zomwe zinali ngati wafa. (Agal. 6:16) Mpingo wa Akhristu odzozedwa unakhala mu ukapolo kwa nthawi yaitali ndipo moyo wawo wauzimu tingauyerekezere ndi mafupa amene anali “ouma kwambiri.” (Ezek. 37:2) Monga mmene tinaonera m’mutu wapita uja, mpingo wa Akhristu odzozedwa unalowa mu ukapolo cha m’ma 100 C.E., ndipo unakhala mu ukapolowo kwa zaka zambiri mogwirizana ndi zimene Yesu ananena mufanizo lake la Ufumu lonena za tirigu ndi namsongole.​—Mat. 13:24-30.

Mafupa “ouma” amene Ezekieli anaona, ankasonyeza kuti anthu a Mulungu anakhala mu ukapolo kwa nthawi yaitali ndipo ankaoneka ngati akufa (Onani ndime 8, 9)

“Mafupawo Anayamba Kubwera Pamodzi Nʼkumalumikizana”

10. (a) Kodi lemba la Ezekieli 37:7, 8 linalosera zinthu ziti zimene zinachitikira anthu a Mulungu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachititsa kuti pang’ono ndi pang’ono anthu a Mulungu amene anali ku ukapolo ayambirenso kukhala ndi chikhulupiriro?

10 Yehova ananeneratu kalekale kuti anthu ake adzabwezeretsedwa pang’onopang’ono n’kukhala amoyo. (Ezek. 37:7, 8) Ndiye n’chiyani chimene chinapangitsa anthu a Mulungu amene anali ku ukapolo kuyamba kukhulupirira pang’onopang’ono kuti zimene analonjezedwa zoti adzabwerera ku Isiraeli zidzakwaniritsidwa? Chinthu chimodzi chimene chinawathandiza kukhulupirira kuti adzabwerera ndi zimene aneneri a m’mbuyomo ananena. Mwachitsanzo, Yesaya ananeneratu kuti anthu otsalira, kapena kuti “mbewu yopatulika,” adzabwerera kwawo. (Yes. 6:13; Yobu 14:7-9) Komanso mosakayikira maulosi ambiri amene Ezekieli analemba okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera anawathandiza kukhala ndi chiyembekezo. Kuwonjezera pamenepo, kupezeka kwa anthu okhulupirika ngati mneneri Danieli ku Babulo, komanso kuwonongedwa kodabwitsa kwa mzinda wa Babulo mu 539 B.C.E., kunathandiza Ayudawo kuti azikhulupirira kwambiri kuti adzabwerera kwawo.

11, 12. (a) Kodi kubwezeretsa pang’onopang’ono kunachitika bwanji pakati pa “Isiraeli wa Mulungu”? (Onaninso bokosi lakuti, “Kulambira Koyera Kunabwezeretsedwa Pang’onopang’ono.”) (b) Kodi zimene zili pa Ezekieli 37:10 zikubweretsa funso liti?

11 Kodi kubwezeretsa pang’onopang’ono kofanana ndi kumeneku kunachitika bwanji pakati pa “Isiraeli wa Mulungu” yemwe ndi mpingo wa Akhristu odzozedwa? Patapita zaka zambiri anthu a Mulungu ali ku ukapolo, ndiponso ali ngati akufa, “panamveka phokoso la mafupa kuti gobedegobede!” Phokosoli linali la anthu oopa Mulungu amene anadzuka kuti ayambirenso kulambira koona. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1500 William Tyndale anamasulira Baibulo m’Chingelezi. Atsogoleri a chipembedzo cha Katolika anakwiya atadziwa kuti tsopano anthu wamba azithanso kuwerenga Baibulo. Tyndale anaphedwa. Ngakhale zinali choncho, anthu ena olimba mtima anapitiriza kumasulira Baibulo m’zilankhulo zinanso ndipo pang’ono ndi pang’ono anthu ambiri ankatha kuwerenga Mawu a Mulungu.

12 Pambuyo pake, Charles T. Russell ndi anzake atayamba kugwira ntchito mwakhama yobwezeretsa choonadi cha m’Baibulo, zinali ngati kuti ‘mitsempha ndi mnofu zinakuta mafupa.’ Magazini a Zion’s Watch Tower ndi mabuku ena zinathandiza anthu oona mtima kuti azindikire choonadi cha m’Baibulo ndipo zimenezi zinawalimbikitsa kuti agwirizane ndi atumiki a Mulungu odzozedwa. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, anthu a Mulungu odzozedwa analimbikitsidwanso ndi zinthu ngati “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” ndi buku la The Finished Mystery. Patangopita nthawi yochepa, nthawi inakwana yoti Mulungu ‘aimiritse’ anthu ake. (Ezek. 37:10) Kodi zimenezi zinachitika liti, ndipo zinachitika bwanji? Zinthu zimene zinachitika ku Babulo wakale, zimatithandiza kuyankha funso limeneli.

“Iwo Anakhala Ndi Moyo Ndipo Anaimirira”

13. (a) Kodi mawu opezeka pa Ezekieli 37:10, 14 anayamba bwanji kukwaniritsidwa kuyambira mu 537 B.C.E.? (b) Kodi ndi malemba ati amene amasonyeza kuti anthu ena amene anali mu ufumu wa mafuko 10 anabwerera ku Isiraeli?

13 Kuyambira mu 537 B.C.E., Ayuda amene anali ku Babulo anaona kukwaniritsidwa kwa masomphenya amenewa. Kodi chinachitika n’chiyani? Yehova anachititsa kuti akhale ndi moyo komanso kuti ‘aimirire’ powapulumutsa ku ukapolo n’kuwalola kuti abwerere ku Isiraeli. Gulu la Aisiraeli okwana 42,360 komanso anthu ena omwe sanali Aisiraeli okwana 7,000 anachoka ku Babulo n’kupita kukamanganso Yerusalemu komanso kachisi ndipo anayamba kukhala ku Isiraeli. (Ezara 1:1-4; 2:64, 65; Ezek. 37:14) Kenako pambuyo pa zaka 70, anthu pafupifupi 1,750 anapita limodzi ndi Ezara pamene ankabwerera ku Yerusalemu. (Ezara 8:1-20) Choncho Ayuda amene anabwerera, onse pamodzi anali oposa 44,000. Indedi anali “gulu lalikulu kwambiri la asilikali.” (Ezek. 37:10) Kuwonjezera pamenepo, Mawu a Mulungu amasonyeza kuti anthu ena omwe anali mu ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli, amene makolo awo anatengedwa ukapolo ndi Asuri m’zaka ma m’ma 700 B.C.E., nawonso anabwerera ku Isiraeli ndipo anathandiza nawo pa ntchito yomanga kachisi.​—1 Mbiri 9:3; Ezara 6:17; Yer. 33:7; Ezek. 36:10.

14. (a) Kodi mawu opezeka pa Ezekieli 37:24 akutithandiza bwanji kudziwa nthawi imene ulosiwu unakwaniritsidwa m’njira yaikulu? (b) N’chiyani chimene chinachitika mu 1919? (Onaninso bokosi lakuti, “‘Mafupa Ouma’ Komanso ‘Mboni Ziwiri’​—Kodi Zikugwirizana Bwanji?”)

14 Kodi mbali imeneyi ya ulosi wa Ezekieli inakwaniritsidwa bwanji m’njira yaikulu? Mogwirizana ndi zimene Yehova anauza Ezekieli mu ulosi wina, kukwaniritsidwa kwakukulu kokhudza kubwezeretsa, kunachitika Davide Wamkulu, yemwe ndi Yesu Khristu, atayamba kulamulira monga Mfumu. b (Ezek. 37:24) Zoonadi, mu 1919 Yehova anapereka mzimu wake kwa anthu ake. Zotsatira zake, anthu akewo ‘anakhala ndi moyo’ ndipo anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. (Yes. 66:8) Kenako Yehova anawalola kuti akhale m’dziko lawo, limene ndi paradaiso wauzimu. Koma kodi zinatheka bwanji kuti anthu a Yehova a masiku ano akhale ‘gulu lalikulu la asilikali’?

15, 16. (a) Kodi zinatheka bwanji kuti anthu a Yehova amasiku ano akhale ‘gulu lalikulu la asilikali’? (b) Kodi ulosi wa Ezekieli umatithandiza bwanji kupirira tikakumana ndi mavuto? (Onani bokosi lakuti, “Adzatithandiza Kuti Tiimirirenso.”)

15 Pasanapite nthawi kuchokera pamene Khristu anasankha kapolo wokhulupirika mu 1919, atumiki a Mulungu anayamba kuona kukwaniritsidwa kwa zimene Zekariya, amene anali mneneri pakati pa Ayuda omwe anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo, analosera kuti: “Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu idzabwera kudzafunafuna Yehova.” Mneneriyu anayerekezera anthu ofunafuna Yehovawa ndi “amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina.” Amunawo adzagwira mkanjo wa “Myuda,” amene ndi Isiraeli wauzimu, n’kunena kuti: “Anthu inu tikufuna tipite nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—Zek. 8:20-23.

16 Masiku ano Isiraeli wauzimu, amene akuimira odzozedwa omwe adakali padziko lapansi, komanso amuna 10 omwe ndi a nkhosa zina, onse pamodzi akupangadi “gulu lalikulu kwambiri la asilikali” limene chiwerengero chawo chikufika mamiliyoni. (Ezek. 37:10) Monga asilikali a Khristu amene tikuwonjezerekawonjezereka, tikutsatira kwambiri Mfumu yathu Yesu kuti tikalandire madalitso amene ali m’tsogolo.​—Sal. 37:29; Ezek. 37:24; Afil. 2:25; 1 Ates. 4:16, 17.

17. Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana chiyani?

17 Kubwezeretsa kulambira koyera kumeneku kukubweretsa udindo wofunika kwambiri kwa anthu a Mulungu. Udindo wotani? Kuti tipeze yankho, tikufunika kuonanso ntchito imene Yehova anapatsa Ezekieli, Yerusalemu asanawonongedwe. Tichita zimenezi m’mutu wotsatira wa bukuli.

a Mafupa amene Ezekieli anaona m’masomphenyawo sanali a anthu amene anafa chifukwa cha matenda koma a ‘anthu amene anachita kuphedwa.’ (Ezek. 37:9) “Nyumba yonse ya Isiraeli” inaphedwadi mophiphiritsa pamene anthu okhala mu ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli komanso anthu okhala mu ufumu wa mafuko awiri wa Yuda anagonjetsedwa ndi Asuri komanso Ababulo n’kutengedwa kupita ku ukapolo.

b Ulosi wokhudza Mesiya umenewu wafotokozedwa m’Mutu 8 wa bukuli.