Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 2

“Iwe Unaipitsa Malo Anga Opatulika”​—Kulambira Koyera Kunadetsedwa

“Iwe Unaipitsa Malo Anga Opatulika”​—Kulambira Koyera Kunadetsedwa

EZEKIELI 5:11

MFUNDO YAIKULU: Makhalidwe komanso moyo wauzimu wa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu zinafika poipa

Yehova ankakonda komanso kusamalira Aisiraeli chifukwa anali ‘chuma chake chapadera.’ (Eks. 19:5) Koma Aisiraeliwo sanayamikire zimene Yehova anawachitira. M’malomwake iwo anayamba kulambira milungu yabodza m’kachisi amene ankadziwika ndi dzina lake. Iwo anakhumudwitsa kwambiri Yehova ndipo anachititsa kuti dzina lake lidetsedwe. N’chifukwa chiyani Aisiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa choncho? Kodi tingaphunzire chiyani pa ulosi wa Ezekieli wokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu? Nanga tingaphunzire chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi mitundu yowazungulira?

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 5

“Uone Zinthu Zoipa Ndi Zonyansa Zimene Anthu Akuchita”

Ezekieli akuona zinthu zochititsa mantha zimene zikusonyeza kuti mtundu wonse unali utasiya kulambira Mulungu woona.

MUTU 6

“Mapeto Akufikira”

Zinthu zokhudza ulosi zimene Ezekieli anachita zinalosera zimene Yehova adzachitire Yerusalemu posonyeza mkwiyo wake.

MUTU 7

Anthu a Mitundu Ina “Adzadziwa kuti Ine Ndine Yehova”

Mitundu imene inanyoza dzina la Yehova komanso kuzunza kapena kusokoneza makhalidwe a anthu ake sidzalephera kulangidwa. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi mitundu imeneyi?