Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 5

“Uone Zinthu Zoipa Ndi Zonyansa Zimene Anthu Akuchita”

“Uone Zinthu Zoipa Ndi Zonyansa Zimene Anthu Akuchita”

EZEKIELI 8:9

MFUNDO YAIKULU: Moyo wauzimu komanso makhalidwe a anthu a ku Yuda amene anapandukira Yehova anafika poipa kwambiri

1-3. Kodi Yehova ankafuna kuti Ezekieli aone chiyani pakachisi ku Yerusalemu, nanga n’chifukwa chiyani? (Onani chithunzi patsamba 50 ndi 51.)

 MNENERI Ezekieli anali mwana wa wansembe, ndipo ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose. Choncho ankadziwa bwino kachisi amene anali ku Yerusalemu komanso kulambira koyera kumene kunkayenera kuchitika kumeneko. (Ezek. 1:3; Mal. 2:7) Koma zimene zinkachitika pakachisi wa Yehova mu 612 B.C.E., zinali zochititsa mantha kwa Myuda aliyense wokhulupirika, kuphatikizapo Ezekieli.

2 Yehova ankafuna kuti Ezekieli aone zinthu zoipa zimene zinkachitika pakachisi kenako akauze zimene waonazo “akuluakulu a Yuda,” omwe anali Ayuda anzake amene anatengedwa kupita ku ukapolo ndipo anali atasonkhana m’nyumba mwake. (Werengani Ezekieli 8:1-4; Ezek. 11:24, 25; 20:1-3) Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova anatenga Ezekieli (m’masomphenya) kuchokera kunyumba kwake ku Tele-abibu, pafupi ndi mtsinje wa Kebara ku Babulo, n’kupita naye kutali ku Yerusalemu. Yehova anasiya mneneriyu m’kachisi, pageti lakumpoto la bwalo lamkati. Kuchokera pamenepo, Yehova anamutenga m’masomphenya n’kuyamba kumuonetsa malo osiyanasiyana m’kachisimo.

3 Tsopano Ezekieli anaona zinthu 4 zochititsa mantha zimene zinasonyeza kuti kulambira koyera kunali kutatheratu mu Yuda. Kodi n’chiyani chimene chinachitikira kulambira koyera kwa Yehova? Kodi masomphenya amenewa akutanthauza chiyani kwa ife masiku ano? Tiyeni tiyende limodzi ndi Ezekieli pamene akumuonetsa malo osiyanasiyana. Koma choyamba tiyeni tikambirane zimene Yehova amayembekezera kuti anthu amene amamulambira azichita.

“Ndine Mulungu Amene Ndimafuna Kuti Anthu Azidzipereka kwa Ine Ndekha”

4. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita chiyani?

4 Zaka pafupifupi 900 Ezekieli asanabadwe, Yehova ananena momveka bwino zimene amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita. Mulamulo lachiwiri pa Malamulo 10, iye anauza Aisiraeli kuti: a “Ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha.” (Eks. 20:5) Ponena kuti “ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,” Yehova anasonyeza kuti safuna ngakhale pang’ono kuti tizilambira milungu ina. Monga mmene tinaonera m’Mutu 2 wa bukuli, chinthu choyamba chofunika kuti kulambira kwathu kukhale koyera n’choti tikuyenera kulambira Yehova yekha basi. Amene amamulambira ayenera kumuika pamalo oyamba pa moyo wawo. (Eks. 20:3) Mwachidule tingati Yehova amayembekezera kuti anthu amene amamulambira akhale oyera mwauzimu popewa kusakaniza kulambira koona ndi kwabodza. Mu 1513 B.C.E., mofunitsitsa Aisiraeli analowa m’pangano la Chilamulo. Pochita zimenezi, anavomereza kuti akhala odzipereka kwa Yehova yekha. (Eks. 24:3-8) Yehova amasunga mapangano ake, ndipo ankayembekezera kuti anthu ake nawonso azisunga mapangano.​—Deut. 7:9, 10; 2 Sam. 22:26.

5, 6. N’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti Aisiraeli azilambira Yehova yekha basi?

5 Kodi zinali zoyenera kuti Yehova aziyembekezera kuti Aisiraeli akhale odzipereka kwa iye yekha? Inde zinali zoyenera. Iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse komanso ndi amene anatipatsa moyo ndipo amatipatsa zonse zofunikira kuti tipitirize kukhala ndi moyo. (Sal. 36:9; Mac. 17:28) Komanso Yehova ndi amene anapulumutsa Aisiraeli. Pamene ankawapatsa Malamulo 10, iye anakumbutsa anthu akewo kuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.” (Eks. 20:2) N’zoonekeratu kuti Aisiraeliwo ankayenera kulambira Yehova yekha ndi mtima wonse.

6 Yehova samasintha. (Mal. 3:6) Nthawi zonse amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha. Ndiye taganizirani mmene anamvera chifukwa cha zinthu zonyansa 4 zimene anaonetsa Ezekieli m’masomphenya.

Chinthu Choyamba: Fano Loimira Nsanje

7. (a) Kodi Ayuda opanduka ankachita chiyani pageti lakumpoto la kachisi ndipo Yehova anachita chiyani chifukwa cha zimenezi? (Onani chithunzi choyambirira) (b) Kodi mfundo yoti Aisiraeli anachititsa kuti Yehova achite nsanje ikutanthauza chiyani? (Onani mawu am’munsi 2.)

7 Werengani Ezekieli 8:5, 6. Ezekieli ayenera kuti anachita mantha kwambiri. Pageti lakumpoto la kachisiyo, Ayuda amene anapandukira Yehova ankalambira fano. N’kutheka kuti fano limeneli linali mzati wopatulika umene unkaimira Ashera, mulungu wabodza amene Akanani ankamuona ngati mkazi wa Baala. Kaya fanoli linali lotani, Aisiraeli opandukawo anaphwanya pangano limene anachita ndi Yehova. Podzipereka kwa fanoli m’malo modzipereka kwa Yehova yekha, Aisiraeliwo anapangitsa kuti Mulungu achite nsanje komanso kuti asonyeze mkwiyo woyenerera. b (Deut. 32:16; Ezek. 5:13) Tangoganizani: Kwa zaka zoposa 400, Aisiraeli ankaona kuti kachisi ndi malo amene Yehova amakhala. (1 Maf. 8:10-13) Koma pamene anayamba kulambira mafano m’kachisi mwenimwenimo, iwo anachititsa kuti Yehova ‘atalikirane ndi malo ake opatulika.’

8. Kodi masomphenya a Ezekieli a fano loimira nsanje akutanthauza chiyani masiku ano?

8 Kodi masomphenya amene Ezekieli anaona a fano loimira nsanje akutanthauza chiyani masiku ano? Ayuda opandukawo akutikumbutsa za matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Matchalitchi amenewa amanena kuti amalambira Mulungu, koma Mulungu savomereza kulambira kwawo chifukwa choti amalambiranso mafano. Popeza Yehova sasintha, n’zoonekeratu kuti matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu amakwiyitsa Mulungu, mofanana ndi Ayuda opanduka aja. (Yak. 1:17) Izi zikusonyeza kuti Yehova ali kutali ndi matchalitchi amenewa, omwe amati ndi a Chikhristu.

9, 10. Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amene ankalambira mafano m’kachisi?

9 Kodi tikuphunzira chiyani kwa Aisiraeli amene ankalambira mafano m’kachisiwa? Kuti tikhale odzipereka kwa Yehova yekha, tiyenera kupewa “kulambira mafano.” (1 Akor. 10:14) Mwina tingamaganize kuti, ‘Ine sindingagwiritse ntchito mafano kapena zifaniziro polambira Yehova.’ Koma munthu angalambire mafano m’njira zosiyanasiyana ndipo njira zina ndi zovuta kuzizindikira. Buku lina lofotokozera Baibulo linanena kuti: “Ena amaona kuti kulambira mafano kungaimire chilichonse chimene munthu amachiona kuti ndi chofunika kwambiri kuposa kulambira Mulungu.” Choncho kulambira mafano kungaphatikizepo zinthu ngati katundu amene tili naye, ndalama, kugonana, zosangalatsa, tingoti chilichonse chimene timachiika pamalo oyamba pa moyo wathu m’malo mokhala odzipereka kwa Yehova. (Mat. 6:19-21, 24; Aef. 5:5; Akol. 3:5) Tiyenera kupewa kulambira mafano kwa mtundu uliwonse chifukwa Yehova amafuna kuti tizidzipereka kwa iye ndi mtima wonse komanso tizilambira iye yekha basi.​—1 Yoh. 5:21.

10 Chinthu choyamba chimene Yehova anaonetsa Ezekieli chinali chokhudza “zinthu zoipa komanso zonyansa kwambiri.” Koma Yehova anauza mneneri wake wokhulupirikayu kuti: “Uonanso zinthu zina zoipa zomwe ndi zonyansa kwambiri kuposa zimenezi.” Kodi ndi chiyani chimene chinali chonyansa kwambiri kuposa kulambira fano loimira nsanje lija m’kachisi?

Chinthu Chachiwiri: Akuluakulu 70 Amene Ankapereka Nsembe Zofukiza kwa Milungu Yabodza

11. Kodi Ezekieli anaona zinthu ziti zochititsa mantha atalowa m’bwalo lamkati pafupi ndi guwa lansembe m’kachisi?

11 Werengani Ezekieli 8:7-12. Atabowola khoma n’kulowa m’bwalo lamkati pafupi ndi guwa la nsembe, Ezekieli anaona zithunzi zochititsa mantha zimene zinajambulidwa pakhoma mochita kugoba. Zithunzizo zinali za “zinthu zosiyanasiyana zokwawa, nyama zonyansa komanso mafano onse onyansa.” c Zithunzi zimenezo zinkaimira milungu yabodza. Koma zinthu zotsatira zimene Ezekieli anaona zinali zochititsa mantha kwambiri. Iye anaona “akuluakulu 70 a nyumba ya Isiraeli” ataimirira “mumdima” ndipo ankapereka nsembe zofukiza kwa milungu yabodza. M’chilamulo, nsembe zofukiza za kafungo kosangalatsa zinkaimira mapemphero ovomerezeka amene atumiki okhulupirika ankapereka. (Sal. 141:2) Koma nsembe zofukiza zimene akuluakulu 70 amenewo ankapereka kwa milungu yabodza zinali zafungo lonyansa kwa Yehova. Mapemphero awo anali ngati fungo lonyansa kwa iye. (Miy. 15:8) Akuluakulu amenewo ankadzinamiza n’kumaganiza kuti: “Yehova sakutiona.” Koma Yehova ankawaona ndipo anaonetsa Ezekieli zonse zimene iwo ankachita m’kachisi wake.

Yehova amaona chinthu chilichonse chonyansa chimene chikuchitikira “mumdima” (Onanai ndime 11)

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe okhulupirika ngakhale “mumdima,” nanga ndi ndani makamaka amene akuyenera kupereka chitsanzo pa nkhani imeneyi?

12 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Ezekieli analemba zokhudza akuluakulu 70 a mu Isiraeli amene ankapereka nsembe zofukiza kwa milungu yabodza? Kuti Mulungu azimva mapemphero athu komanso kuti aziona kuti kulambira kwathu ndi koyera, tiyenera kukhalabe okhulupirika ngakhale pamene tili “mumdima.” (Miy. 15:29) Tisaiwale kuti maso a Yehova amene amaona chilichonse amationa nthawi zonse. Ngati Yehova ndi weniweni kwa ife, tidzapewa kuchita chilichonse chimene tikudziwa kuti sichingamusangalatse, ngakhale pamene tili kwatokha. (Aheb. 4:13) Makamaka akulu mumpingo ayenera kusonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yotsatira mfundo za m’Baibulo. (1 Pet. 5:2, 3) N’zomveka kuti abale ndi alongo mumpingo aziyembekezera kuti mkulu amene amawatsogolera pamisonkhano yampingo azitsatira mfundo za m’Baibulo ngakhale pamene ali “mumdima,” kapena kuti pamene anthu ena sakumuona.​—Sal. 101:2, 3.

Chinthu Chachitatu: ‘Azimayi Ankalirira Mulungu Wotchedwa Tamuzi’

13. Kodi Ezekieli anaona azimayi opanduka akuchita chiyani pageti lina la kachisi?

13 Werengani Ezekieli 8:13, 14. Yehova ataonetsa Ezekieli zinthu ziwiri zoipa zimene Aisiraeli ankachita, anamuuzanso kuti: “Uonanso zinthu zina zoipa komanso zonyansa kwambiri zimene akuchita.” Ndiye kodi kenako mneneriyu anaona chiyani? “Pakhomo la geti la nyumba ya Yehova limene linali mbali yakumpoto” anaona “azimayi atakhala pansi nʼkumalirira mulungu wotchedwa Tamuzi.” Tamuzi anali mulungu wabodza wa ku Mesopotamiya ndipo m’zolemba za Chisumeriya amatchedwa Dumuzi. Anthu ankakhulupirira kuti Tamuzi anali mwamuna wa Ishitara, amene anali mulungu wothandiza anthu kuti azibereka. d Zikuoneka kuti azimayi a ku Isiraeliwo ankalira monga mbali ya mwambo wachipembedzo wokhudzana ndi imfa ya Tamuzi. Polirira Tamuzi m’kachisi wa Yehova, azimayiwo ankachita mwambo wachikunja m’malo amene ndi chimake cha kulambira koyera. Koma sikuti kulambira milungu yabodza kunakhala koyera chifukwa chakuti kunachitikira m’kachisi wa Yehova. Tikutero chifukwa kwa Yehova, azimayi opandukawo ankachita ‘zinthu zonyansa kwambiri.’

14. Kodi mmene Yehova ankaonera zimene azimayi opandukawo ankachita zikutiphunzitsa chiyani?

14 Kodi mmene Yehova ankaonera zimene azimayiwo ankachita zikutiphunzitsa chiyani? Kuti kulambira kwathu kupitirize kukhala koyera, tikuyenera kupewa kusakaniza kulambirako ndi miyambo yoipa yachikunja. Choncho tizipewa zikondwerero zonse zimene zinayambira m’zipembedzo zabodza. Kodi kumene chikondwererocho chinayambira kuli ndi vuto lililonse? Inde. Masiku ano zimene anthu amachita pa zikondwerero zina ngati Khirisimasi ndi Isitala zingaoneke ngati zilibe vuto lililonse. Koma tisaiwale kuti Yehova anaona miyambo yachipembedzo chabodza imene pamapeto pake inasintha n’kukhala zikondwerero zimene anthu akuchita masiku ano. Kwa Yehova miyambo yoipa yachikunjayo sisiya kukhala yonyansa chifukwa chakuti anthu aichita kwa nthawi yaitali kapena chifukwa choti aisakaniza ndi kulambira koyera.​—2 Akor. 6:17; Chiv. 18:2, 4.

Chinthu cha 4: Amuna 25 Amene “Ankagwadira Dzuwa”

15, 16. Kodi amuna 25 ankachita chiyani m’bwalo lamkati la kachisi ndipo n’chifukwa chiyani zimene ankachitazo zinakhumudwitsa kwambiri Yehova?

15 Werengani Ezekieli 8:15-18. Poyamba kufotokoza chinthu cha nambala 4, Yehova akubwerezanso mawu omwe aja kuti: “Uonanso zinthu zina zoipa zomwe ndi zonyansa kwambiri kuposa zimenezi.” N’kutheka kuti mneneriyu anadzifunsa kuti: ‘Kodi pangakhale zinthu zinanso zonyansa kwambiri kuposa zimene ndaona kalezi?’ Pa nthawiyi Ezekieli anali m’bwalo lamkati la pakachisi. Pakhomo la kachisi kumeneko iye anaona amuna 25 atagwada n’kumalambira “dzuwa limene linali kum’mawa.” Zimene amuna amenewa ankachita zinakwiyitsa kwambiri Yehova. Kodi anamukwiyitsa bwanji?

16 Taganizirani mmene zinthu zinalili. Khomo la kachisi wa Mulungu linayang’ana kum’mawa. Anthu amene ankalowa m’kachisimo ankayang’ana kumadzulo ndipo misana yawo inkaloza kum’mawa kotulukira dzuwa. Koma amuna 25 amene Ezekieli anawaona m’masomphenyawo anali “atafulatira kachisi” ndipo nkhope zawo zinali zitayangʼana kum’mawa kuti azilambira dzuwa. Pochita zimenezi, iwo anafulatira Yehova chifukwa kachisiyo anali “nyumba ya Yehova.” (1 Maf. 8:10-13) Amuna 25 amenewo anali ampatuko. Iwo anakana Yehova ndipo anaphwanya lamulo limene tikulipeza pa Deuteronomo 4:15-19. Iwo anakhumudwitsa Mulungu yekhayo amene ndi woyenera kulambiridwa.

Anthu amene amalambira Yehova akuyenera kulambira iye yekha basi

17, 18. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya anthu amene ankalambira dzuwa m’kachisi? (b) Kodi zimene Aisiraeli opandukawo ankachita zinakhudza bwanji ubwenzi wawo ndi Yehova komanso anthu anzawo?

17 Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amenewa omwe ankalambira dzuwa? Kuti kulambira kwathu kupitirize kukhala koyera, tiyenera kudalira Yehova kuti azitithandiza kumvetsa mfundo zachoonadi komanso kuti tikhale anzeru. Tizikumbukira kuti “Yehova Mulungu ndi dzuwa,” ndipo Mawu ake ndi “kuwala” kounikira njira yathu. (Sal. 84:11; 119:105) Pogwiritsa ntchito Mawu ake komanso mabuku othandiza pophunzira Baibulo amene gulu lake limapereka, Mulungu amaunika maganizo ndi mitima yathu n’kutithandiza kuti tizichita zinthu zimene zingapangitse kuti tizikhala moyo wosangalala panopa komanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo. Ndiye ngati tingadalire mfundo komanso nzeru za m’dzikoli kuti zizitithandiza pa moyo wathu, tingakhale ngati tikufulatira Yehova. Zimenezo zingamukhumudwitse kwambiri ndipo zingachititse kuti amve ululu mumtima. Sitingafune kuchita zimenezi kwa Mulungu wathu. Masomphenya a Ezekieli akutichenjezanso kuti tizipewa ampatuko amene amakana choonadi.​—Miy. 11:9.

18 Pofika pano taona kuti Ezekieli anaona zinthu 4 zochititsa mantha zokhudza kulambira kwa bodza komanso kulambira mafano zimene zinasonyeza kuti kulambira kwa Ayuda opandukawo kunafika poipa kwambiri. Kulambira mafano kumene Aisiraeli ankachita kunachititsa kuti aononge ubwenzi wawo ndi Yehova. Komatu anthu akasiya kulambira koona amayambanso kuchita makhalidwe oipa. Choncho n’zosadabwitsa kuti Aisiraeli opandukawo anachita zinthu zambiri zoipa zimene zinaononga ubwenzi wawo ndi Mulungu komanso anthu anzawo. Tsopano tiyeni tione mmene mneneri Ezekieli mouziridwa anafotokozera mmene makhalidwe a Ayuda opandukawo anaipira.

Makhalidwe Onyansa​—Anthu Akuchita “Khalidwe Lonyansa Pakati Panu”

19. Kodi Ezekieli anafotokoza kuti makhalidwe a anthu amene anachita pangano ndi Yehova anaipa kufika pati?

19 Werengani Ezekieli 22:3-12. Aliyense m’dzikolo ankachita zinthu zoipa, kuyambira olamulira mpaka anthu wamba. ‘Atsogoleri’ ankagwiritsa ntchito mphamvu zimene anali nazo kupha anthu osalakwa. Zikuoneka kuti anthu ankatsatira atsogoleri awo pophwanya Malamulo a Mulungu. M’banja ana ‘ankanyoza’ makolo awo ndipo anthu ankagonana pachibale. M’dzikolo Aisiraeli opanduka ankachitira chinyengo alendo komanso ankazunza ana ndi akazi amasiye. Amuna a Chiisiraeli ankagona ndi akazi a anzawo. Anthu ankasonyeza dyera loipa pochita ziphuphu, kuba komanso kukakamiza anthu kuti azipereka chiwongoladzanja. Ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Yehova kuona anthu omwe anachita nawo pangano akunyalanyaza Chilamulo chake. Iwo analephera kuzindikira kuti Yehova anawapatsa Chilamulochi chifukwa choti ankawakonda. Makhalidwe awo oipawo anakhumudwitsa kwambiri Yehova. Iye analamula Ezekieli kuti auze anthu a makhalidwe oipawo kuti: ‘Ine mwandiiwaliratu.’

Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu achititsa kuti anthu m’dzikoli azikonda kuchita zachiwawa komanso makhalidwe oipa (Onani ndime 20)

20. N’chifukwa chiyani zimene Ezekieli ananena zokhudza makhalidwe oipa a Ayuda n’zothandiza masiku ano?

20 Kodi zimene Ezekieli ananena zokhudza makhalidwe oipa a Ayuda, zikutikhudza bwanji masiku ano? Makhalidwe oipa amene Ayuda opandukawo ankachita, akutikumbutsa kuti masiku anonso makhalidwe a anthu ndi oipa. Atsogoleri andale amagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika ndipo amapondereza anthu awo. Atsogoleri achipembedzo makamaka atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu, amapempherera mayiko amene akuchita nkhondo ndipo zimenezi zachititsa kuti anthu mamiliyoni ambiri osalakwa aphedwe. Atsogoleri achipembedzo amanyalanyaza mfundo zomveka bwino zimene Baibulo limanena zokhudza chiwerewere. Zimenezi zachititsa kuti makhalidwe a anthu apitirize kuipa. Sitikukayikira kuti zimene Yehova anauza Ayuda opanduka aja angauzenso matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu kuti: ‘Ine mwandiiwaliratu.’

21. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa makhalidwe oipa a Ayuda akale?

21 Kodi ifeyo monga anthu a Yehova tikuphunzirapo chiyani pa makhalidwe oipa a anthu akale a ku Yuda? Kuti Yehova azivomereza kulambira kwathu tiyenera kusonyeza makhalidwe oyera pa chilichonse chimene tikuchita. Komatu kuchita zimenezi sikophweka m’dziko limene ladzaza ndi makhalidwe oipali. (2 Tim. 3:1-5) Koma tikudziwa mmene Yehova amamvera akaona makhalidwe onse oipa omwe akuchitika m’dzikoli. (1 Akor. 6:9, 10) Timatsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene Yehova amatipatsa chifukwa choti timamukonda komanso timakonda malamulo ake. (Sal. 119:97; 1 Yoh. 5:3) Ngati titachita makhalidwe oipa tingasonyeze kuti sitikonda Mulungu wathu amene ndi woyera komanso wopatulika. Sitingafune olo pang’ono kuchita chilichonse chimene chingachititse Yehova kunena kuti: ‘Ine mwandiiwaliratu.’

22. (a) Kuchokera pa zimene Yehova anaonetsa Ezekieli zokhudza Ayuda akale, kodi ndife otsimikiza kuchita chiyani? (b) Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana chiyani?

22 Taphunzira mfundo zofunika kwambiri kuchokera pa zimene Yehova anaonetsa Ezekieli zokhudza Ayuda akale, amene ankalambira mafano komanso kuchita makhalidwe oipa. Zimenezi zatithandiza kuti tikhale ofunitsitsa kulambira Yehova yekha chifukwa iye ndi woyenera kulambiridwa. Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tikuyenera kupewa kulambira mafano kwa mtundu wina uliwonse ndipo tizipewa makhalidwe oipa. Koma kodi Yehova anatani ndi anthu ake osakhulupirikawo? Chakumapeto kwa ulendo wa Ezekieli wokaona kachisi, Yehova anauza mneneri wakeyu mosapita m’mbali kuti: “Ineyo ndidzawalanga nditakwiya kwambiri.” (Ezek. 8:17, 18) Tikufuna tidziwe zimene Yehova anachita ndi Ayuda osakhulupirikawa chifukwa chiweruzo chofanana ndi chimenechi chiperekedwanso kwa anthu oipa am’dzikoli. M’mutu wotsatira tiona mmene ziweruzo zomwe Yehova anapereka kwa Ayuda zinakwaniritsidwira.

a M’buku la Ezekieli, mawu akuti “Isiraeli” nthawi zambiri akumawagwiritsa ntchito ponena za anthu amene ankakhala ku Yuda ndi ku Yerusalemu.​—Ezek. 12:19, 22; 18:2; 21:2, 3.

b Pogwiritsa ntchito mawu akuti “nsanje” Yehova anasonyeza kuti amaona kuti nkhani yokhala okhulupirika kwa iye ndi yaikulu. Zikutipangitsa kuganiza za mkwiyo umene mwamuna amakhala nawo chifukwa cha nsanje mkazi wake akachita zinthu zosakhulupirika. (Miy. 6:34) Mofanana ndi mwamuna ameneyu, Yehova anakwiyiranso anthu amene anachita nawo pangano atayamba kulambira mafano. Buku lina linanena kuti: “Mulungu amachita nsanje . . . chifukwa choti ndi woyera. Popeza kuti iye yekha ndi Woyera . . . , Safuna kuti wina aliyense azipikisana naye.”​—Eks. 34:14.

c Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “mafano onyansa” ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu a Chiheberi amene amatanthauza “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kunyansidwa.

d Palibe umboni uliwonse wotsimikizira zimene ena amanena zoti Tamuzi ndi dzina lina la Nimurodi.