Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 5

“Ndidzakhala Pakati pa Aisiraeli”​—Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera

“Ndidzakhala Pakati pa Aisiraeli”​—Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera

EZEKIELI 43:7

MFUNDO YAIKULU: Zinthu zimene zili m’masomphenya a kachisi komanso zimene zinthuzo zikutiphunzitsa zokhudza kulambira koyera

Yehova anapereka masomphenya kwa mneneri Ezekieli komanso mtumwi Yohane amene akufanana m’njira zambiri. Zimene zili m’masomphenyawa zikutiphunzitsa mfundo zofunika kwambiri zimene zingatithandize kuti tizilambira Yehova m’njira yovomerezeka panopa. Komanso zikutithandiza kuona mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso mu Ufumu wa Mulungu.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 19

“Kulikonse Kumene Mtsinjewo Ukupita, Chilichonse Chidzakhala ndi Moyo”

N’chifukwa chiyani tinganene kuti masomphenya a Ezekieli a mtsinje umene ukuyenda kuchokera m’kachisi anakwaniritsidwa m’mbuyomo, akukwaniritsidwa panopa komanso adzakwaniritsidwa m’tsogolo?

MUTU 20

‘Mugawane Dzikoli Kuti Likhale Cholowa Chanu’

M’masomphenya, Yehova anapereka malangizo kwa Ezekieli ndi Ayuda anzake amene anali ku ukapolo kuti agawe Dziko Lolonjezedwa kwa mafuko a Isiraeli.

MUTU 21

“Dzina la Mzindawo Lidzakhala Lakuti Yehova Ali Kumeneko”

Kodi tikuphunzira chiyani pa masomphenya amene Ezekieli anaona okhudza mzinda komanso dzina lake latanthauzo?

MUTU 22

“Lambira Mulungu”

Cholinga cha bukuli ndi kutilimbikitsa kuti tizilambira Yehova Mulungu yekha basi.