Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 22

“Lambira Mulungu”

“Lambira Mulungu”

CHIVUMBULUTSO 22:9

MFUNDO YAIKULU: Kubwereza mfundo zikuluzikulu za m’buku la Ezekieli komanso mmene tingazigwiritsire ntchito panopa komanso m’tsogolo

1, 2. (a) Kodi tonsefe tili ndi mwayi wosankha chiyani? (b) Kodi mngelo wokhulupirika anachita chiyani pamene munthu ankafuna kumulambira?

 ALIYENSE wa ife akuyenera kuyankha funso lofunika lakuti: Kodi ndizilambira ndani? Anthu ambiri anganene kuti nkhani imeneyi ndi yovuta ndipo n’zovuta kusankha kuti ungalambire ndani. Koma zoona zake n’zakuti n’zosavuta kusankha woyenera kumulambira. Tili ndi ufulu wosankha kulambira Yehova Mulungu kapena kulambira Satana Mdyerekezi.

2 Satana amafunitsitsa kuti tizimulambira. Zimenezi zinaonekera bwino kwambiri pamene ankayesa Yesu. Monga mmene tinaonera m’mutu woyamba wa buku lino, Satana analonjeza Yesu kuti amupatsa mphoto yaikulu, yomwe ndi mphamvu yolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Kodi Mdyerekezi ankafuna kuti Yesu achite chiyani? Iye anauza Yesu kuti: ‘Mugwade pansi kamodzi kokha nʼkundilambira.’ (Mat. 4:9) Mosiyana ndi zimenezi, mngelo amene anapereka uthenga wa m’chivumbulutso kwa mtumwi Yohane anakana kulambiridwa. (Werengani Chivumbulutso 22:8, 9.) Pamene Yohane ankafuna kulambira mngeloyo, mwana wauzimu wa Mulungu wodzichepetsayo anayankha kuti: “Usachite zimenezo!” M’malo monena kuti, ‘Lambira ine,’ iye ananena kuti: “Lambira Mulungu.”

3. (a) Kodi cholinga cha bukuli ndi chiyani? (b) Kodi tsopano tikambirana chiyani?

3 Cholinga cha bukuli ndi kutilimbikitsa kuti tizimvera zimene mngeloyo analamula zoti tizilambira Yehova Mulungu yekha basi. (Deut. 10:20; Mat. 4:10) Tiyeni tikambirane mwachidule zomwe taphunzira zokhudza kulambira koyera kuchokera m’maulosi komanso m’masomphenya amene Ezekieli anaona. Kenako pogwiritsa ntchito Malemba tiona zimene zidzachitike m’tsogolo pa nthawi imene munthu aliyense padziko lapansi adzayesedwe komaliza. Mayesero amenewa adzathandiza kudziwa amene adzakhale ndi moyo n’kuona kulambira koyera kutabwezeretsedwa mpaka kalekale.

Mfundo Zitatu Zimene Zafotokozedwa Bwino M’buku la Ezekieli

4. Kodi ndi mfundo zikuluzikulu zitatu ziti zimene zatsindikidwa m’buku la Ezekieli?

4 Buku la Ezekieli likutiphunzitsa kuti kulambira koyera si kungochita zinthu mwamwambo. Koma kumafuna kuti (1) tizilambira Yehova yekha, (2) tizikhala ogwirizana polambira Yehova ndipo (3) tizisonyeza chikondi kwa anzathu. Tiyeni tione mmene maulosi komanso masomphenya amene afotokozedwa m’bukuli akusonyezera kufunika kwa mfundo zitatuzi.

Mfundo yoyamba: Tizilambira Yehova yekha basi

5-9. Kodi taphunzira chiyani pa nkhani ya kulambira Yehova yekha?

5 Mutu 3: Masomphenya ochititsa chidwi osonyeza Yehova atazunguliridwa ndi utawaleza komanso atakwera pa angelo amphamvu, akutithandiza kumvetsa mfundo yofunika yakuti Wamphamvuyonse yekha ndi amene tikuyenera kumulambira.​—Ezek. 1:4, 15-28.

6 Mutu 5: Zinali zokhumudwitsa kwambiri kuona masomphenya osonyeza kachisi wa Yehova akudetsedwa. Masomphenyawa akusonyeza kuti palibe chimene chimakhala chobisika kwa Yehova. Iye amaona zinthu zosonyeza kusakhulupirika zimene anthu akuchita, ngati pamene anthu ake ayamba kulambira mafano, ngakhale kuti zimene akuchitazo anthu sangathe kuziona. Iye amakhumudwa ndi zinthu zimenezi ndipo amapereka chilango kwa anthu amene amachita zimenezi.​—Ezek. 8:1-18.

7 Mutu 7: Ziweruzo zimene Yehova anapereka ku mitundu yozungulira imene ‘inkanyoza’ Aisiraeli, zimasonyeza kuti Yehova amapereka chilango kwa anthu amene amazunza anthu ake. (Ezek. 25:6) Koma tikuphunziranso chinthu china tikaona mmene Aisiraeli ankachitira zinthu ndi anthu amitundu inawo. Chinthu chake ndi chakuti tiziona kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa china chilichonse. Sitingalole kuphwanya mfundo zimene timatsatira pongofuna kusangalatsa achibale athu omwe salambira Yehova. Komanso sitingayambe kukhulupirira chuma kapena kulowerera ndale popereka ulemu ndi ulemerero kwa maboma, zimene Yehova yekha ndi amene akuyenera kulandira.

8 Mutu 13 ndi 14: Masomphenya osonyeza kachisi ali paphiri lalitali akutikumbutsa kuti tikufunika kutsatira mfundo zapamwamba zamakhalidwe abwino za Yehova pozindikira kuti iyeyo ndi wapamwamba kuposa milungu ina yonse.​—Ezek. 40:1–48:35.

9 Mutu 15: Maulosi oyerekezera Isiraeli komanso Yuda ndi mahule akutikumbutsa kuti Yehova amanyansidwa kwambiri ndi kulambira mafano.​—Ezekieli chaputala 16 ndi 23.

Mfundo yachiwiri: Tizikhala ogwirizana polambira Yehova

10-14. Kodi mfundo yosonyeza kufunika kolambira Yehova mogwirizana yatsindikidwa bwanji?

10 Mutu 8: Maulosi okhudza malonjezo a Yehova akuti adzaika “m’busa mmodzi” kuti azisamalira anthu ake, akutsindika kufunika kogwira ntchito mogwirizana komanso mwamtendere motsogoleredwa ndi Yesu.​—Ezek. 34:23, 24; 37:24-28.

11 Mutu 9: Masomphenya a Ezekieli okhudza anthu a Mulungu atamasulidwa kuchokera ku ukapolo ku Babulo n’kubwezeretsedwa ku dziko lakwawo, akupereka uthenga wofunika kwa anthu amene akufuna kusangalatsa Yehova masiku ano. Anthu amene amalambira Yehova akufunika kuchoka m’chipembedzo chabodza komanso kupewa kuchita nawo zinthu zilizonse zokhudzana ndi chipembedzo chimenechi. Tikufunika kupitiriza kukhala ogwirizana zomwe zimatithandiza kudziwika kuti ndife anthu a Mulungu. Tikuyenera kuchita zimenezi ngakhale kuti tinachokera m’zipembedzo zosiyanasiyana, timapeza zinthu mosiyana komanso tinachokera m’zikhalidwe zosiyanasiyana.​—Ezek. 11:17, 18; 12:24; Yoh. 17:20-23.

12 Mutu 10: Mfundo ya mgwirizano inatsindikidwa ndi masomphenya osonyeza mafupa ouma atakhalanso ndi moyo. Tilitu ndi mwayi kukhala m’gulu la anthu omwe ayeretsedwa n’kuyamba kulambiranso Yehova mogwirizana ngati gulu la asilikali.​—Ezek. 37:1-14.

13 Mutu 12: Ulosi wa ndodo ziwiri zimene zinaphatikizidwa n’kukhala ndodo imodzi unatsindika kufunika kwa mgwirizano. Chikhulupiriro chathu chimalimba tikamaona odzozedwa komanso a nkhosa zina akukwaniritsa ulosi umenewu. Ngakhale kuti tikukhala m’dziko lomwe ndi logawanika chifukwa cha udani wa zipembedzo komanso ndale, ife timakhala ogwirizana chifukwa cha chikondi komanso kukhulupirika.​—Ezek. 37:15-23.

14 Mutu 16: Masomphenya a munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki komanso amuna onyamula zida zowonongera, ali ndi chenjezo lofunika kwambiri. Chenjezo lake ndi lakuti anthu okhawo amene amalambira Mulungu woona, amene adzadutse pa “chisautso chachikulu,” ndi amene adzakhale ndi mwayi wolembedwa chizindikiro kuti apulumuke.​—Mat. 24:21; Ezek. 9:1-11.

Mfundo yachitatu: Tizisonyeza chikondi kwa anzathu

15-18. N’chifukwa chiyani tikufunika kupitiriza kusonyezana chikondi, nanga tingachite bwanji zimenezi?

15 Mutu 4: Masomphenya okhudza angelo 4 anatiphunzitsa za makhalidwe a Yehova. Lalikulu pa makhalidwe onse amene Yehova ali nawo ndi chikondi. Tikamalankhula komanso kuchita zinthu mwa chikondi, timasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wathu.​—Ezek. 1:5-14; 1 Yoh. 4:8.

16 Mutu 6 ndi 11: Chikondi cha Mulungu chinamulimbikitsa kuti aike alonda monga Ezekieli. Popeza Mulungu ndi chikondi, iye safuna kuti aliyense adzawonongedwe pa nthawi imene adzawononge dziko limene likulamuliridwa ndi Satanali. (2 Pet. 3:9) Tili ndi mwayi wosonyeza chikondi cha Yehova pokwaniritsa udindo wathu wothandiza pa ntchito imene mlonda wamasiku ano akugwira.​—Ezek. 33:1-9.

17 Mutu 17 ndi 18: Yehova akudziwa kuti anthu ambiri adzakana chifundo chimene akuwasonyeza ndipo adzayesa kuwononga anthu amene akumulambira mokhulupirika. Chikondi chidzapangitsa Yehova kuti ateteze anthu ake pamene “Gogi wa kudziko la Magogi” adzaukire anthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika. Kukonda anthu kumatilimbikitsa kuti tichenjeze anthu ambiri mmene tingathere kuti Yehova adzawononga anthu amene amazunza anthu ake.​—Ezek. 38:1–39:20; 2 Ates. 1:6, 7.

18 Mutu 19 ndi 20: Chikondi cha Yehova pa anthu ake chikuonekera bwino kwambiri m’masomphenya osonyeza mtsinje wa madzi opatsa moyo komanso kugawa kwa malo. Masomphenyawa akusonyeza njira yaikulu kwambiri imene Yehova anasonyezera chikondi chake popereka Mwana wake kuti machimo athu akhululukidwe komanso kuti tidzasangalale ndi moyo wangwiro m’banja la Mulungu. Imodzi mwa njira zimene tingasonyezere kuti timakonda anthu ndi kuwauza za tsogolo labwino kwambiri limene Yehova wakonzera anthu amene amakhulupirira Mwana wake.​—Ezek. 45:1-7; 47:1–48:35; Chiv. 21:1-4; 22:17.

Pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu ndi Olamulira Anzake Adzasonyeza Kudzichepetsa Kwakukulu

19. Kodi Yesu adzachita chiyani mu Ulamuliro wa Zaka 1,000? (Onani bokosi lakuti “Kukumana ndi Mayesero Omaliza.”)

19 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu adzaukitsa anthu mabiliyoni ambiri ndipo adzathetsa ululu umene umabwera chifukwa cha ‘imfa, yomwe ndi mdani.’ (1 Akor. 15:26; Maliko 5:38-42; Mac. 24:15) Mbiri ya anthu ili ngati nkhani yomvetsa chisoni komanso yokhumudwitsa. Koma mibadwo ya anthu ikamadzaukitsidwa, Yesu azidzafufuta nkhani yomvetsa chisoniyi n’kupereka mwayi kwa anthu omwe adzaukitsidwe kuti alembe nkhani yosangalatsa kwambiri. Pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu Khristu adzachotsa mavuto onse obwera chifukwa cha kudwala, nkhondo, matenda komanso njala. Koma kuposa zonsezi, adzatithandiza kuchotsa chimene chimayambitsa chisoni chathu, chomwe ndi uchimo umene tinatengera kwa Adamu. (Aroma 5:18, 19) Yesu ‘adzawonongeratu ntchito za Mdyerekezi.’ (1 Yoh. 3:8) Ndiye kodi kenako chidzachitike ndi chiyani?

Anthu amene adzaukitsidwe adzakhala ndi mwayi wolemba nkhani yabwino kwambiri

20. Kodi Yesu ndi a 144,000, adzasonyeza bwanji kudzichepetsa kwakukulu? Fotokozani. (Onani chithunzi choyambirira.)

20 Werengani 1 Akorinto 15:24-28. Anthu onse akadzakhala angwiro komanso dziko lonse lapansi likadzakhala Paradaiso ngati mmene Yehova ankafunira poyamba, Yesu ndi olamulira anzake a 144,000 adzasonyeza kudzichepetsa kwakukulu, iwo adzapereka Ufumu kwa Yehova. Mofunitsitsa komanso mwamtendere, iwo adzapereka ulamuliro womwe anali nawo kwa zaka 1,000. Zinthu zonse zimene Ufumuwu udzakhale utachita zidzakhalapo mpaka kalekale.

Mayesero Omaliza

21, 22. (a) Kodi dziko lidzakhala lotani kumapeto kwa zaka 1,000? (b) N’chifukwa chiyani Yehova adzamasule Satana ndi ziwanda?

21 Kenako Yehova adzachita chinthu china chochititsa chidwi kwambiri, chinthu chimene chidzasonyeze kuti amakhulupirira kwambiri atumiki ake apadziko lapansi. Iye adzalamula kuti Satana ndi ziwanda zake atulutsidwe kuphompho kumene anatsekeredwa kwa zaka 1,000. (Werengani Chivumbulutso 20:1-3.) Dziko komanso anthu amene Satana ndi ziwanda zake adzawaone, adzakhala osiyana kwambiri ndi amene ankawadziwa poyamba. Aramagedo isanachitike, anthu ambiri adzakhala oti anasocheretsedwa ndi Satana ndipo adzakhala osagwirizana chifukwa cha chidani komanso tsankho. (Chiv. 12:9) Koma pambuyo pa zaka 1,000, anthu onse azidzalambira Yehova monga banja limodzi logwirizana komanso lokondana. Dziko lonse lapansi lidzakhala Paradaiso.

22 N’chifukwa chiyani Yehova adzalole kuti Satana ndi ziwanda zake, omwe ndi zigawenga adzatuluke n’kulowa m’dziko lokongolali? Chifukwa chakuti anthu ambiri amene adzakhale ndi moyo kumapeto kwa zaka 1,000, adzakhala oti sanayesedwepo kuti asonyeze ngati ali okhulupirika kwa Yehova. Anthu ambiri adzakhala oti anafa asakudziwa Yehova ndipo adzaukitsidwira m’Paradaiso. Yehova adzawapatsa moyo komanso zinthu zonse zofunika pa moyo, zauzimu ndi zakuthupi zomwe. Iwo sadzasokonezedwa ndi anthu oipa chifukwa azidzakhala ndi anthu abwino okhaokha amene amakonda komanso kutumikira Yehova. Satana adzawanenera zofanana ndi zimene ananenera Yobu kuti amatumikira Mulungu chabe chifukwa chakuti akuwateteza komanso kuwadalitsa. (Yobu 1:9, 10) Choncho Yehova asanalembe kwamuyaya mayina athu m’buku la moyo, adzalola kuti tisonyeze popanda chokayikitsa chilichonse kuti ndife okhulupirika kwa iye monga Atate wathu ndi Wolamulira wathu Wamkulu.​—Chiv. 20:12, 15.

23. Kodi munthu aliyense adzafunika kusankha chiyani?

23 Kwa kanthawi kochepa, Satana adzapatsidwa mwayi kuti ayese anthu n’kuwasiyitsa kutumikira Mulungu. Kodi mayesero amenewo adzakhala otani? N’zosakayikitsa kuti munthu wina aliyense adzafunika kusankha ngati mmene zinalili ndi Adamu ndi Hava pakati pa kuvomereza mfundo za Yehova, kukhala kumbali ya ulamuliro wake n’kumamulambira kapena kupandukira Mulungu n’kumatumikira Satana.

24. N’chifukwa chiyani anthu amene adzapanduke akutchedwa Gogi komanso Magogi?

24 Werengani Chivumbulutso 20:7-10. N’zochititsa chidwi kuti anthu amene adzapanduke kumapeto kwa zaka 1,000, akutchulidwa kuti Gogi komanso Magogi. Iwo adzasonyeza makhalidwe ofanana ndi amene anthu opanduka anasonyeza. Anthu opandukawa ndi amene Ezekieli analosera kuti adzaukira anthu a Mulungu pa chisautso chachikulu. Gulu la anthu amenewa, limene Ezekieli analitchula kuti “Gogi wa kudziko la Magogi,” ndi gulu la anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana amene akutsutsa ulamuliro wa Yehova. (Ezek. 38:2) Mofanana ndi zimenezi, anthu amene adzapandukire Mulungu kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, akufotokozedwa kuti ndi “mayiko.” Zimenezitu ndi zochititsa chidwi kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, mayiko onse amene amagawanitsa anthu adzakhala atachotsedwa ndipo anthu onse azidzalamuliridwa ndi boma limodzi lomwe ndi Ufumu wa Mulungu. Tonse tidzakhala mtundu umodzi wogwirizana. Potchula opandukawo kuti Gogi komanso Magogi ndiponso ponena kuti ndi “mayiko,” ulosiwu ukusonyeza kuti Satana adzakwanitsa kugawanitsa anthu ena amene ali pakati pa anthu a Mulungu. Koma palibe amene adzakakamizidwe kukhala kumbali ya Satana. Munthu aliyense amene pa nthawiyo adzakhala wangwiro adzasankha yekha mbali imene akufuna kukhala.

Anthu amene adzapanduke akutchedwa Gogi komanso Magogi (Onani ndime 24)

25, 26. Kodi ndi anthu angati amene adzakhale kumbali ya Satana ndipo n’chiyani chimene chidzawachitikire?

25 Kodi ndi anthu angati amene adzakhale kumbali ya Satana? Anthu amene adzapanduke adzakhala “ochuluka ngati mchenga wakunyanja.” Mawu amenewa sakusonyeza kuti amene adzapanduke adzakhala anthu ambiri. Tikudziwa bwanji zimenezi? Taganizirani lonjezo limene Yehova anauza Abulahamu. Yehova ananena kuti mbadwa za Abulahamu zidzakhala “ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja.” (Gen. 22:17, 18) Komatu chiwerengero cha anthu amene anapanga mbadwa zake chinalipo 144,001 basi. (Agal. 3:16, 29) Ngakhale kuti nambala imeneyi ndi yaikulu, koma ndi kagawo kochepa chabe poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu onse. Mofanana ndi zimenezi, chiwerengero cha anthu amene adzakhale kumbali ya Satana chikhoza kudzakhala chachikulu koma sikuti chidzachita kukhala chachikulu kwambiri modabwitsa. Anthu amene adzapandukewo sadzasokoneza kwambiri anthu amene azidzatumikira Yehova mokhulupirika.

26 Anthu amene adzapanduke adzawonongedwa mwamsanga. Iwo limodzi ndi Satana komanso ziwanda, sadzakhalaponso ndipo sadzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse choti adzakhalanso ndi moyo. Anthu azidzangokumbukira mpaka kalekale zinthu zolakwika zimene opandukawo anasankha komanso zotsatirapo zoipa za zosankha zawozo.​—Chiv. 20:10.

27-29. N’chiyani chimene chidzachitike kwa anthu amene adzapambane pa mayesero omaliza?

27 Koma anthu amene adzapambane pa mayesero omaliza mayina awo adzalembedwa “m’buku la moyo” mpaka kalekale. (Chiv. 20:15) Ndiyeno monga banja limodzi logwirizana, ana onse a Yehova, aakazi ndi aamuna adzakhala ogwirizana pomulambira monga woyenera kulambiridwa.

28 Taganizirani mmene zidzakhalire pa nthawiyo. Kutsogoloku tidzakhala ndi ntchito yabwino kwambiri komanso tidzakhala ndi mwayi wokhala ndi anzathu abwino. Inuyo komanso anthu amene mumawakonda simudzavutikanso. Sitidzafunikanso nsembe ya Yesu Khristu kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova, chifukwa tidzakhala kuti tilibe uchimo uliwonse. Aliyense adzakhala pa ubwenzi wapamtima ndi Mulungu popanda cholepheretsa chilichonse. Ndipo chinthu chofunika pa zonsezi n’chakuti kumwamba komanso padziko lapansi aliyense azidzalambira Yehova ali wangwiro. Apatu kulambira koyera kudzakhala kuti kwabwezeretsedweratu.

Mukadzakhala angwiro, simudzafunikanso nsembe ya Yesu kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa mudzakhala kuti mulibe uchimo uliwonse (Onani ndime 28)

29 Kodi inuyo mudzakhala ndi moyo n’kumaona zinthu zimenezi zikuchitika? Mudzakhalapo ngati mukupitiriza kutsatira mfundo zitatu zikuluzikulu za m’buku la Ezekieli zomwe ndi kulambira Yehova yekha, kukhala ogwirizana polambira Yehova komanso kusonyeza chikondi kwa ena. Maulosi a Ezekieli akutipatsa phunziro lomaliza lomwe ndi lofunika kwambiri. Kodi phunziro limeneli ndi liti?

Taganizirani mmene zidzakhalire zosangalatsa, onse kumwamba ndi padziko lapansi akadzakhala ogwirizana polambira Yehova (Onani ndime 27-29)

“Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova”

30, 31. Kodi mawu akuti “adzadziwa kuti ine ndine Yehova” adzatanthauza chiyani (a) kwa adani a Mulungu? (b) kwa anthu a Mulungu?

30 M’buku lonse la Ezekieli mawu akuti “adzadziwa kuti ine ndine Yehova” akupezeka kambirimbiri komanso mobwerezabwereza. (Ezek. 6:10; 39:28) Kwa adani a Mulungu, mawu amenewa adzatanthauza nkhondo komanso imfa. Iwo adzakakamizika kuchita zambiri kuwonjezera pa kuvomereza kuti Yehova alipodi. Iwo adzaphunzira mowawa tanthauzo la dzina lake lakuti, “Amachititsa Kukhala.” “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,” adzakhala “msilikali wamphamvu” kwambiri amene adzamenyane nawo. (1 Sam. 17:45; Eks. 15:3) Iwo adzamvetsa mfundo ya choonadi yokhudza Yehova koma mudzakhala m’mbuyo mwa alendo. Mfundo yake ndi yakuti: Palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa zolinga zake.

31 Koma kwa anthu a Mulungu, mawu akuti “iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova” adzatanthauza mtendere komanso moyo. Yehova adzachititsa kuti tikhale mmene ankafunira poyamba. Tidzakhala ana aakazi ndi aamuna amene azidzasonyeza makhalidwe ake angwiro. (Gen. 1:26) Panopa, Yehova wakhala kale Atate wathu wachikondi komanso M’busa wathu amene amatiteteza. Posachedwapa akhala Mfumu yathu yotimenyera nkhondo. Pamene tikuyembekezera nthawi imeneyo, tiyeni tiziganizira uthenga wa Ezekieli. Tiyeni tizisonyeza m’zolankhula ndi zochita zathu kuti tikumudziwa bwino Yehova komanso zimene dzina lake limaimira. Tikamachita zimenezi mphepo zowononga za chisautso chachikulu zikadzamasulidwa, sitidzachita mantha. M’malomwake, tidzatukula mitu yathu chifukwa tidzakhala tikudziwa kuti chipulumutso chathu chikuyandikira. (Luka 21:28) Padakali pano, tiyeni tithandize anthu kulikonse kuti adziwe komanso kukonda Yehova, Mulungu amene ndi woyenera kumulambira, Mulungu amene ali ndi dzina lalikulu kuposa mayina onse lakuti Yehova.​—Ezek. 28:26.