Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 1

“Kumwamba Kunatseguka”

“Kumwamba Kunatseguka”

EZEKIELI 1:1

MFUNDO YAIKULU: Tiona mwachidule zokhudza kumwamba kumene Yehova amakhala

Palibe munthu amene angaone Yehova, Mulungu wamphamvuyonse n’kukhalabe ndi moyo. (Eks. 33:20) Koma Yehova anaonetsa Ezekieli masomphenya amene amatithandiza kudziwa mbali yakumwamba ya gulu lake. Masomphenya amenewa amatichititsa mantha komanso amatipangitsa kuti tiziyamikira kwambiri mwayi umene tili nawo wolambira Mulungu woona.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 3

“Ndinayamba Kuona Masomphenya a Mulungu”

Masomphenya oyamba amene Ezekieli anaona anamuchititsa mantha kwambiri. Masomphenyawa ali ndi tanthauzo lofunika kwambiri kwa atumiki okhulupirika a Mulungu masiku ano.

MUTU 4

Kodi ‘Angelo Ankhope 4 Aliyense’ Akuimira Chiyani?

Yehova anaonetsa Ezekieli zinthu zimene zimatithandiza kumvetsa zinthu zimene sitikanatha kuzimvetsa.