Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 4

Kodi ‘Angelo Ankhope 4 Aliyense’ Akuimira Chiyani?

Kodi ‘Angelo Ankhope 4 Aliyense’ Akuimira Chiyani?

EZEKIELI 1:15

MFUNDO YAIKULU: Zimene tikuphunzira kuchokera kwa angelo

1, 2. N’chifukwa chiyani Yehova nthawi zina amagwiritsa ntchito zinthu zooneka akamafotokoza mfundo za choonadi kwa atumiki ake padziko lapansi pano?

 TIYEREKEZE kuti banja limene lili ndi ana aang’ono lakhala pamodzi ndipo likuphunzira Baibulo. Pofuna kuthandiza anawo kuti amvetse mfundo ya m’Malemba, bambo awo akuwaonetsa zithunzi. Anawo akumwetulira komanso akupereka ndemanga zolimbikitsa ndipo zimenezi zikusonyeza kuti zimene bambo awo akuwaphunzitsazo zikuwafika pamtima. Kugwiritsa ntchito zithunzi pophunzitsa kwathandiza kuti anawo amvetse zimene akuphunzira zokhudza Yehova, zomwe mwina sakanatha kuzimvetsa chifukwa choti ndi ana.

2 Mofanana ndi zimenezi Yehova amagwiritsa ntchito zinthu zooneka pophunzitsa ana ake apadziko lapansi kuti amvetse zinthu zosaoneka zimene sakanatha kuzimvetsa. Mwachitsanzo, pofotokoza mfundo zozama zokhudza iyeyo, Yehova anaonetsa Ezekieli masomphenya amene anali ndi zithunzi zambiri zochititsa chidwi. M’mutu 3 wa bukuli takambirana chimodzi mwa zithunzi zimenezi. Tsopano tiyeni tikambirane mbali imodzi ya masomphenya ochititsa chidwiwa, n’kuona mmene kumvetsa tanthauzo lake kungatithandizire kuti tiyandikire kwambiri Yehova.

“Ndinaona . . . Zinazake Zooneka Ngati Angelo 4”

3. (a) Mogwirizana ndi Ezekieli 1:4, 5, kodi Ezekieli anaona chiyani m’masomphenya? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi mwaona zotani zokhudza mmene Ezekieli ankalembera zimene anaona?

3 Werengani Ezekieli 1:4, 5. Ezekieli anafotokoza kuti “zinazake zooneka ngati angelo 4” zinalinso ndi mbali zina zooneka ngati munthu komanso zinyama. Onani mmene Ezekieli anafotokozera zimene anaona. Iye ananena kuti anaona “zinazake zooneka ngati angelo.” Mukamawerenga masomphenya onse opezeka mu Ezekieli chaputala 1, muona kuti mobwerezabwereza mneneriyu anagwiritsa ntchito mawu akuti “ankaoneka ngati,” “zooneka ngati,” “ankamveka ngati,” “chooneka ngati” komanso “wooneka ngati.” (Ezek. 1:13, 24, 26) Izi zikusonyeza kuti Ezekieli ankadziwa kuti akungoona zithunzi kapena kuti zinthu zofanana ndi zinthu zenizeni zimene zili kumwamba.

4. (a) Kodi masomphenya amene Ezekieli anaona anamukhudza bwanji? (b) Kodi sitikukayikira kuti Ezekieli ankadziwa zotani zokhudza akerubi?

4 Ezekieli ayenera kuti anachita mantha ndi zimene anaona komanso kumva m’masomphenyawo. Angelo 4 amenewo ankaoneka ngati “makala oyaka moto.” Angelowo ankayenda mofulumira kwambiri “ngati mphezi.” Phokoso la mapiko awo “linkamveka ngati phokoso la madzi omwe akuthamanga” ndipo “akamayenda, ankamveka ngati phokoso la gulu la asilikali.” (Ezek. 1:13, 14, 24-28; onani bokosi lakuti “Ndinkayangʼana Angelowo.”) M’masomphenya ena, Ezekieli ananena kuti angelo amenewa ndi “akerubi” kapena kuti angelo amphamvu. (Ezek. 10:2) Popeza kuti Ezekieli anakulira m’banja la ansembe, n’zosakayikitsa kuti ankadziwa kuti akerubi amatumikira Mulungu ndipo nthawi zambiri amakhala naye pafupi kwambiri.​—1 Mbiri 28:18; Sal. 18:10.

“Mngelo Aliyense Anali Ndi Nkhope 4”

5. (a) Kodi akerubi komanso nkhope zawo 4 zinasonyeza bwanji kukula kwa mphamvu komanso ulemerero wa Yehova? (b) N’chifukwa chiyani mbali imeneyi ya masomphenya ikutikumbutsa tanthauzo la dzina la Mulungu? (Onani mawu am’munsi.)

5 Werengani Ezekieli 1:6, 10. Ezekieli anaonanso kuti kerubi aliyense anali ndi nkhope 4. Anali ndi nkhope ya munthu, ya mkango, ya ng’ombe yamphongo ndi ya chiwombankhanga. Nkhope 4 zimene Ezekieli anaonazi ziyenera kuti zinamuphunzitsa zambiri zokhudza mphamvu komanso ulemerero wa Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Nkhope iliyonse inali ya chinthu chamoyo chimene chinkaimira ulemerero, nyonga ndi mphamvu. Mkango ndi nyama yakutchire yaulemerero, ng’ombe yamphongo ndi nyama yoweta yochititsa chidwi, chiwombankhanga ndi mbalame yamphamvu ndipo munthu ndi chinthu chapadera kwambiri chimene Mulungu analenga padziko lapansi, chifukwa ali ndi udindo wolamulira zonse zimene Mulungu analenga padziko lapansi. (Sal. 8:4-6) Koma m’masomphenya amenewa, Ezekieli anaona kuti zinthu zonse 4 zamphamvu zomwe zikuimira zinthu zimene Mulungu analenga, monga mmene nkhope 4 za kerubi aliyense zikusonyezera, zinali pansi pa mpando wachifumu wa Yehova, amene ndi Wolamulira Wamkulu Koposa. Apatu Yehova anasonyeza bwino kwambiri kuti angagwiritse ntchito zinthu zimene analenga pokwaniritsa cholinga chake. a Inde, monga mmene wolemba Masalimo ananenera zokhudza Yehova, “ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.”​—Sal. 148:13.

Kodi angelo 4 ndi nkhope zawo 4 zikutiuza chiyani za mphamvu za Yehova, ulemerero wake ndi makhalidwe ake? (Onani ndime 5, 13)

6. Kodi n’chiyani chiyenera kuti chinathandiza Ezekieli kuti amvetse zinthu zina zimene nkhope 4 zimaimira?

6 Patadutsa nthawi komanso Ezekieli ataganizira zimene anaona, ayenera kuti anakumbukira kuti atumiki a Mulungu amene analipo iye asanabadwe anagwiritsa ntchito zinyama m’mafanizo awo. Mwachitsanzo, kholo lakale Yakobo anayerekezera mwana wake Yuda ndi mkango ndipo Benjamini anamuyerekezera ndi mmbulu.(Gen. 49:9, 27) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mkango ndi mmbulu zimaimira makhalidwe amene ana amenewa anadzasonyeza. Choncho Ezekieli akaganizira zitsanzo zimenezi kuchokera m’malemba ouziridwa amene Mose analemba, ayenera kuti ankaona kuti nkhope za akerubiwo zikuimiranso makhalidwe apadera. Koma kodi makhalidwe ake ndi ati?

Makhalidwe Amene Yehova Komanso Banja Lake Lakumwamba Ali Nawo

7, 8. Kodi ndi makhalidwe ati amene kawirikawiri timawagwirizanitsa ndi nkhope 4 za akerubi?

7 Kodi anthu amene analemba Baibulo, amene anakhala ndi moyo Ezekieli asanabadwe anagwirizanitsa mkango, chiwombankhanga komanso ng’ombe yamphongo ndi makhalidwe ati? Taganizirani mawu a m’Baibulo akuti: “Mwamuna wolimba mtima ngati mkango.” (2 Sam. 17:10; Miy. 28:1) “Chiwombankhanga chimauluka mʼmwamba” ndipo “maso ake amaona kutali kwambiri.” (Yobu 39:27, 29) “Zokolola zimachuluka ngati pali ngʼombe yamphongo yamphamvu.” (Miy. 14:4) Mogwirizana ndi malemba amenewa, nkhope ya mkango ikuimira kuchita chilungamo molimba mtima. Nkhope ya chiwombankhanga ikuimira nzeru zoona patali. Nkhope ya ng’ombe yamphongo ikuimira mphamvu zochuluka, monga mmene mabuku athu akhala akunenera.

8 Koma kodi ‘nkhope ya munthu’ ikuimira chiyani? (Ezek. 10:14) Iyenera kuti ikuimira khalidwe limene silingasonyezedwe ndi nyama iliyonse, koma anthu amene anapangidwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Gen. 1:27) Khalidwe limeneli, lomwe anthu okha padziko lapansi ndi amene amatha kulisonyeza, tikulipeza m’malamulo amene Mulungu anapereka akuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse” komanso “uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Deut. 6:5; Lev. 19:18) Tikamamvera malamulo amenewa posonyeza chikondi chopanda dyera, timasonyeza chikondi chimene Yehova ali nacho. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Yohane analemba, “ife timasonyeza chikondi, chifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yoh. 4:8, 19) Choncho ‘nkhope ya munthu’ ikuimira chikondi.

9. Kodi makhalidwe amene timawagwirizanitsa ndi nkhope za akerubi ndi a ndani?

9 Kodi ndi ndani amene ali ndi makhalidwe amenewa? Popeza kuti nkhopezi ndi za akerubi, ndiye kuti makhalidwewa ndi a angelo onse okhulupirika omwe akupanga banja lakumwamba la Yehova. Tikutero chifukwa akerubi amene Ezekieli anaona m’masomphenyawa akuimira angelo onse okhulupirika. (Chiv. 5:11) Komanso Yehova ndi amene analenga akerubiwo, choncho ndi iyeyo amenenso anawapatsa makhalidwewa. (Sal. 36:9) Izi zikusonyeza kuti nkhope za akerubiwo zikuimira makhalidwe a Yehova. (Yobu 37:23; Sal. 99:4; Miy. 2:6; Mika 7:18) Kodi ndi njira zochepa ziti zimene Yehova amasonyezera makhalidwe apaderawa?

10, 11. Kodi timapindula m’njira ziti ndi makhalidwe 4 akuluakulu a Yehova?

10 Chilungamo. Monga Mulungu amene “amakonda chilungamo,” Yehova “sakondera munthu aliyense.” (Sal. 37:28; Deut. 10:17) Choncho tonsefe tili ndi mwayi woti tikhoza kukhala atumiki ake n’kudzalandira madalitso posatengera mmene anthu amationera kapena kumene tikuchokera. Nzeru. Popeza kuti Yehova ndi Mulungu amene “ali ndi mtima wanzeru,” iye anatipatsa buku limene lili ndi “nzeru zopindulitsa.” (Yobu 9:4; Miy. 2:7) Kutsatira malangizo anzeru opezeka m’Baibulo, kumatithandiza kuti tizithana ndi mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku komanso kuti tizikhala ndi moyo wabwino. Mphamvu. Popeza Yehova ndi Mulungu amene “ali ndi mphamvu zambiri,” iye amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera potipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.” Mphamvu zimenezi zimatithandiza kuti tizikwanitsa kupirira mayesero aliwonse aakulu komanso opweteka amene tingakumane nawo.​—Nah. 1:3; 2 Akor. 4:7; Sal. 46:1.

11 Chikondi. Yehova ndi Mulungu “wachikondi chokhulupirika chochuluka,” ndipo sasiya atumiki ake okhulupirika. (Sal. 103:8; 2 Sam. 22:26) Choncho ngakhale titakhumudwa chifukwa choti thanzi lathu kapena uchikulire zikutilepheretsa kuchita zambiri potumikira Yehova ngati mmene tinkachitira poyamba, timalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova akukumbukira zimene tinamuchitira m’mbuyomu chifukwa chomukonda. (Aheb. 6:10) N’zoonekeratu kuti tapindula kale kwambiri ndi zimene Yehova wachita posonyeza chilungamo, nzeru, mphamvu komanso chikondi ndipo tipitiriza kupindula ndi makhalidwe 4 akuluakulu amenewa mpaka kalekale.

12. Kodi tizikumbukira chiyani pa zimene tingakwanitse kumvetsa zokhudza makhalidwe a Yehova?

12 Komabe tiyenera kukumbukira kuti zimene anthufe tingathe kumvetsa zokhudza makhalidwe a Yehova zangokhala “kambali kakangʼono chabe ka zochita zake.” (Yobu 26:14) “Wamphamvuyonse sitingathe kumumvetsa” chifukwa “palibe amene angamvetse ukulu wake.” (Yobu 37:23; Sal. 145:3) Choncho tikudziwa kuti makhalidwe a Yehova sangawerengeke kapena kuikidwa m’magulu. (Werengani Aroma 11:33, 34.) Ndipotu masomphenya amene Ezekieli anaona amasonyeza kuti makhalidwe a Mulungu ndi osawerengeka kapena kuti alibe malire. (Sal. 139:17, 18) Kodi ndi mbali iti ya masomphenyawa imene ikusonyeza mfundo yofunikayi?

‘Nkhope 4, Mapiko 4, Mbali 4’

13, 14. Kodi nkhope 4 za akerubi zikuimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tikutero?

13 Ezekieli anaona m’masomphenya kuti kerubi aliyense anali ndi nkhope 4, osati imodzi. Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani? Kumbukirani kuti m’Mawu a Mulungu, kawirikawiri nambala ya 4 imagwiritsidwa ntchito poimirira chinthu chathunthu kapena cha zonse mommo kapenanso chokwanira. (Yes. 11:12; Mat. 24:31; Chiv. 7:1) N’zochititsa chidwi kuti m’masomphenya awa okha, Ezekieli anatchula nambala ya 4 maulendo osachepera 11. (Ezek. 1:5-18) Ndiye kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Monga mmene taonera kuti akerubi 4 akuimira angelo onse okhulupirika, choncho nkhope 4 za akerubiwa, zonse tikaziona pamodzi, zikuimira makhalidwe onse amene Yehova ali nawo. b

14 Kuti timvetse mfundo yakuti nkhope 4 za akerubi sizikungoimira makhalidwe 4 okha amene Yehova ali nawo, ganizirani zimene zikuchitika ndi mawilo 4 a galeta lija m’masomphenyawa. Wilo lililonse palokha ndi lochititsa chidwi, koma mawilo onse 4 tikawaona pa nthawi imodzi, amakhala ochititsa chidwi kwambiri kuposa wilo limodzi chifukwa ndi amene anyamula galetalo. Mofanana ndi zimenezi, nkhope 4 za akerubiwo tikaziona pamodzi, zimaimira makhalidwe ambiri ochititsa chidwi osati 4 okha, chifukwa chakuti zikuimira makhalidwe onse a Yehova omwe ndi mbali yofunika kwambiri ya umunthu wake.

Yehova Ali Pafupi ndi Atumiki Ake Onse Okhulupirika

15. Kodi Ezekieli anaphunzira mfundo yolimbikitsa iti ataona masomphenya oyambirira?

15 M’masomphenya onse oyambawa, Ezekieli anaphunzira mfundo yofunika komanso yolimbikitsa yokhudza ubwenzi wake ndi Yehova. Kodi mfundo yake ndi yotani? Mfundo imeneyi tikuipeza m’mawu oyamba a buku limene mneneriyu analemba. Atanena kuti anali “mʼdziko la Akasidi,” Ezekieli anafotokoza zimene zinamuchitikira kuti: “Kumeneko mphamvu za Yehova zinayamba kugwira ntchito pa iye.” (Ezek. 1:3) Onani kuti Ezekieli sananene kuti anaona masomphenyawa ali ku Yerusalemu, koma kumeneko, kutanthauza ku Babulo. c Kodi zimenezi zinkasonyeza chiyani kwa Ezekieli? Zinkasonyeza kuti, ngakhale kuti anali kapolo amene anali kutali ndi Yerusalemu komanso kachisi wake, iye sanali kutali ndi Yehova ndipo ankamulambirabe. Zimene Yehova anachita poonekera kwa Ezekieli ku Babulo zinasonyeza kuti kulambira Mulungu woona sikunkadalira kuti akhale pamalo enaake kapena kuti akhale mwanjira inayake. M’malomwake, zinkadalira zimene zinali mumtima mwa Ezekieli komanso mtima wake wofunitsitsa kutumikira Yehova.

16. (a) Kodi tikupeza mfundo yolimbikitsa iti m’masomphenya a Ezekieli? (b) N’chiyani chimene chimakulimbikitsani kuti muzitumikira Yehova ndi mtima wanu wonse?

16 N’chifukwa chiyani mfundo imene Ezekieli anaphunzira ili yofunika kwambiri kwa ife masiku ano? Ikutitsimikizira kuti tikamatumikira Yehova ndi mtima wonse, iye amakhala nafe pafupi kulikonse kumene tingakhale, kaya tili ndi nkhawa kapena tikukumana ndi zotani pa moyo wathu. (Sal. 25:14; Mac. 17:27) Chifukwa cha chikondi chokhulupirika chimene Yehova ali nacho pa mtumiki wake aliyense, iye safulumira kuganiza kuti ndife okanika. (Eks. 34:6) Choncho tisamaganize kuti Yehova sangatisonyeze chikondi chake chokhulupirika. (Sal. 100:5; Aroma 8:35-39) Komanso masomphenya ochititsa chidwiwa, omwe akusonyeza kuti Yehova ndi woyera komanso kuti ali ndi mphamvu zambiri, akutikumbutsa kuti Yehova yekha ndi amene ali woyenera kumulambira. (Chiv. 4:9-11) Timayamikira kwambiri kuti Yehova anagwiritsa ntchito masomphenya ngati amenewa kuti atithandize kumvetsa mfundo zina zofunika kwambiri zokhudza iyeyo komanso makhalidwe ake. Tikamamvetsa bwino makhalidwe ochititsa chidwi a Yehova zimatithandiza kuti timuyandikire komanso zimatilimbikitsa kuti tizimutamanda ndi kumutumikira ndi mtima wathu wonse komanso mphamvu zathu zonse.​—Luka 10:27.

Yehova angathe kutisonyeza chikondi chokhulupirika mosaganizira za umunthu wathu kapena kumene tili (Onani ndime 16)

17. Kodi tikambirana mafunso ati m’mitu yotsatira?

17 Koma n’zomvetsa chisoni kuti m’nthawi ya Ezekieli kulambira koyera kunadetsedwa. Kodi kunadetsedwa bwanji? Kodi Yehova anachita chiyani? Nanga zimene zinachitikazo zikutiphunzitsa chiyani ifeyo masiku ano? Mafunso amenewa ayankhidwa m’mitu yotsatira.

a Zimene Ezekieli anafotokoza zokhudza angelo amenewa zimatikumbutsa za dzina la Mulungu lakuti Yehova, limene limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Monga mmene mbali ina ya tanthauzo la dzinali ikusonyezera, Yehova angachititse zinthu zimene analenga kukhala chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse cholinga chake.​—Onani Zakumapeto A4 mu Baibulo la Dziko Latsopano.

b Kwa zaka zambiri, mabuku athu akhala akufotokoza makhalidwe osiyanasiyana pafupifupi 50 a Yehova.​—Onani Watch Tower Publications Index pamutu wakuti “Jehovah,” komanso kamutu kakang’ono kakuti “Qualities by Name.”

c Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti mawu amodzi akuti “kumeneko, akusonyeza kuti pa nthawiyo anazindikira mfundo yosangalatsa kwambiri . . . yakuti Mulungu ali kumeneko ku Babulo!” Zimenezi zinali zolimbikitsa kwambiri!”