Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 13A

Akachisi Osiyana Ofotokoza Zinthu Zosiyana

Akachisi Osiyana Ofotokoza Zinthu Zosiyana

Kachisi Amene Ezekieli Anaona M’masomphenya:

  • Anafotokozedwa ndi Ezekieli pofuna kuthandiza Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo

  • Ali ndi guwa lansembe pamene pankaperekedwa nsembe zambiri

  • Akusonyeza mfundo zolungama zimene Yehova amafuna kuti tizitsatira pomulambira

  • Akutithandiza kumvetsa kubwezeretsa kwauzimu kumene kunayambika mu 1919

Kachisi Wamkulu Wauzimu:

  • Anafotokozedwa ndi Paulo m’kalata imene analembera Akhristu a Chiheberi

  • Ali ndi guwa lansembe pamene panaperekedwa nsembe imodzi “kamodzi kokha” (Aheb. 10:10)

  • Akufotokoza za kulambira Yehova m’njira yovomerezeka kudzera mu nsembe ya dipo ya Khristu zomwe zinkaimiliridwa ndi chihema komanso akachisi

  • Amatithandiza kumvetsa ntchito imene Khristu anagwira monga Mkulu wa Ansembe wamkulu kuchokera mu 29 mpaka 33 C.E.