Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 15A

Atsikana Apachibale Omwe Anali Mahule

Atsikana Apachibale Omwe Anali Mahule

Mu Ezekieli chaputala 23 timapezamo uthenga wamphamvu wa chiweruzo umene anthu a Mulungu adzalandire chifukwa chosakhulupirika. Chaputala chimenechi chikufanana ndi chaputala 16 m’njira zambiri. Mofanana ndi uthenga umene uli m’chaputala chimenechi, chaputala 23 chagwiritsa ntchito chitsanzo cha uhule. Yerusalemu akufotokozedwa kuti ndi mchemwali wake wa Samariya ndipo wamkulu pa awiriwa ndi Samariya. Machaputala awiri onsewa akusonyeza mmene wamng’onoyu anayambira kuchita za uhule potengera chitsanzo cha mkulu wake ndipo kenako anayamba kuchita makhalidwe oipa kwambiri kuposa mkulu wakeyo. Muchaputala 23 Yehova anapereka mayina kwa atsikana awiriwa. Wamkulu anamupatsa dzina lakuti Ohola yemwe ndi Samariya, likulu la ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli. Wamng’ono ndi Oholiba yemwe ndi Yerusalemu, likulu la Yuda. a​—Ezek. 23:1-4.

Machaputala awiriwa alinso ndi nkhani zina zomwe ndi zofanana. Mwina zimene zikudziwika kwambiri ndi izi: Poyamba mahulewa anali ngati akazi a Yehova koma kenako anamusiya. Komanso muli lonjezo lopatsa chiyembekezo. Chaputala 23 sichikufotokoza zambiri zokhudza kupulumutsidwa koma chikufanana ndi chaputala 16 pamene Yehova ananena kuti: “Ine ndidzathetsa khalidwe lako lonyansa ndiponso uhule wako.”​—Ezek. 16:16, 20, 21, 37, 38, 41, 42; 23:4, 11, 22, 23, 27, 37.

Kodi Akuimira Matchalitchi Amene Amati ndi a Chikhristu?

M’mbuyomu mabuku athu ankanena kuti atsikana awiri apachibalewa, omwe ndi Ohola ndi Oholiba, akuimira matchalitchi omwe amati ndi a Chikhristu makamaka mbali zake ziwiri zomwe ndi Chikatolika ndi Chipulotesitanti. Komabe titapemphera kwambiri komanso kufufuza mwakhama, tinadzifunsa kuti: Kodi matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu anayamba akhalapo mkazi wa Yehova? Kodi anayamba achitapo pangano ndi Yehova? Ayi ndithu. Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu kunalibe pamene Yesu anakhala mkhalapakati wa “pangano latsopano” limene anapanga ndi Isiraeli wauzimu komanso sanali mbali ya mtundu wa Isiraeli wauzimu wa Akhristu odzozedwa. (Yer. 31:31; Luka 22:20) Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu kunalibeko ndipo anayamba kupezeka pambuyo poti atumwi onse amwalira. Matchalitchiwa anayamba kupezeka pambuyo pa chaka cha 300 C.E. ndipo ankadziwika ngati ampatuko, gulu losokoneza limene limapanga “namsongole” omwe ndi Akhristu abodza amene Yesu anawatchula mufanizo lake la tirigu ndi namsongole.​—Mat. 13:24-30.

Kusiyana kwina ndi kwakuti Yehova anapereka uthenga wa chiyembekezo kwa Yerusalemu ndi Samariya amene anali osakhulupirika. (Ezek. 16:41, 42, 53-55) Kodi Baibulo limapereka uthenga wachiyembekezo ngati umenewu kwa matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu? Ayi. Matchalitchi amenewa alibe chiyembekezo chilichonse mofanana ndi Babulo Wamkulu.

Choncho Ohola ndi Oholiba sakuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Komabe kupezeka kwa matchalitchiwa kumatithandiza kumvetsa mfundo ina yofunika kwambiri. Kumatithandiza kumvetsa mmene Yehova amaonera anthu amene amadetsa dzina lake loyera komanso kuphwanya mfundo zake zokhudza kulambira koyera. Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu ali ndi mlandu pa nkhani imeneyi chifukwa iwo amanena kuti akuimira Mulungu wotchulidwa m’Baibulo. Ndipotu chinthu china chomvetsa chisoni n’chakuti amanena kuti Mwana wokondedwa wa Yehova, yemwe ndi Yesu Khristu ndi mtsogoleri wawo. Koma amasonyeza kuti zimene amanenazo n’zabodza chifukwa amanena kuti Yesu ndi mbali ya milungu itatu mwa mulungu mmodzi komanso samvera lamulo lomveka bwino loti asamakhale “mbali ya dziko.” (Yoh. 15:19) Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu asonyezadi kuti ndi mbali ya “hule lalikulu” chifukwa amalimbikitsa kulambira mafano komanso kulowerera ndale. (Chiv. 17:1) Mosakayikira matchalitchi amenewa adzawonongedwa monga mmene zidzakhalire ndi zipembedzo zonse zabodza.

a Mayinawa ali ndi tanthauzo lapadera. Dzina lakuti Ohola limatanthauza “Tenti Yake [yolambirira.]”​—mwina tanthauzo la dzinali likugwirizana ndi zimene Aisiraeli ankachita pokhazikitsa malo awo olambirira m’malo mopita kukachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Koma dzina lakuti Oholiba limatanthauza kuti “Tenti Yanga [yolambirira] Ili mwa Iye.” Ku Yerusalemu ndi kumene kunali nyumba yolambirira ya Yehova.