Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 7B

Mawu Odziwika Kwambiri Opezeka M’buku la Ezekieli

Mawu Odziwika Kwambiri Opezeka M’buku la Ezekieli

“Mwana wa Munthu”

AKUPEZEKA MALO OPOSA 90

Kwa maulendo oposa 90, Ezekieli akutchulidwa kuti “mwana wa munthu.” (Ezek. 2:1) Pochita zimenezi Yehova anamukumbutsa kuti anali munthu ngakhale kuti anapatsidwa utumiki wapadera. N’zochititsa chidwi kuti mu nkhani za m’Mauthenga Abwino, Yesu akutchulidwa kuti “Mwana wa munthu” maulendo 80, kusonyeza kuti anali munthu weniweni osati mngelo amene anavala thupi la munthu.​—Mat. 8:20.

“. . . Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova”

AKUPEZEKA MALO OPOSA 50

Kwa maulendo oposa 50, Ezekieli analemba zimene Mulungu ananena kuti anthu ‘adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’ kusonyeza kuti Yehova yekha ndi amene ali woyenera kulambiridwa.​—Ezek. 6:7.

“Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa”

AKUPEZEKA MALO 217

Mawu akuti “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa” akupezeka malo 217. Zimenezi zathandiza kuti dzina la Mulungu lidziwike komanso zikutsindika mfundo yakuti chilengedwe chonse chikuyenera kugonjera Yehova.​—Ezek. 2:4.