Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 1A

Kodi Kulambira N’kutani?

Kodi Kulambira N’kutani?

Tinganene kuti kulambira “ndi njira yosonyezera ulemu komanso chikondi kwa mulungu.” M’Baibulo mawu a chilankhulo choyambirira amene anawamasulira kuti “kulambira” angatanthauze kulemekeza kwambiri kapena kugonjera zolengedwa. (Mat. 28:9) Mawuwa angagwiritsidwenso ntchito pofotokoza zimene anthu azipembedzo amachitira Mulungu kapena mafano. (Yoh. 4:23, 24) Kuti tidziwe tanthauzo la mawuwa, zimadalira mmene agwiritsidwira ntchito m’chiganizo.

Tikuyenera kudzipereka kwa Yehova yekha, amene ndi Mlengi komanso Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. (Chiv. 4:10, 11) Timalambira Yehova tikamalemekeza ulamuliro wake komanso dzina lake. (Sal. 86:9; Mat. 6:9, 10) Mfundo zikuluzikulu ziwirizi, zomwe ndi Ulamuliro wa Yehova komanso dzina lake, zafotokozedwa mobwerezabwereza m’buku la Ezekieli. Mawu akuti “Ambuye Wamkulu Koposa” akupezeka malo 217 m’buku la Ezekieli lokha ndipo mawu akuti “mudzadziwa kuti ine ndine Yehova,” akupezeka malo 55.​—Ezek. 2:4; 6:7.

Kulambira kwathu si kumangothera mumtima koma kulambira koona kumafuna kuti tizichita zinthu zina. (Yak. 2:26) Tikapereka moyo wathu kwa Yehova timalumbira kuti pa chilichonse chomwe tikuchita pa moyo wathu, tidzamumvera monga Wolamulira wathu Wamkulu komanso kulemekeza kwambiri dzina lake. Kumbukirani kuti pamene ankayankha pa mayesero achitatu, Yesu anagwirizanitsa kulambira ndi “kutumikira” Mulungu yekha basi. (Mat. 4:10) Monga olambira Yehova timafunitsitsa kumutumikira. a (Deut. 10:12) Timachita utumiki wopatulika kwa Mulungu tikamachita zinthu zokhudza kulambira zimene zimafuna kudzimana. Kodi zinthu zake ndi ziti?

Timachita utumiki wopatulika m’njira zosiyanasiyana koma mautumiki onsewo ndi amtengo wapatali kwa Yehova. Mwachitsanzo, timachita utumiki wopatulika tikamalalikira, tikamakamba nkhani kapena kuyankha pamisonkhano komanso tikamasamalira ndi kumanga malo olambirira. Timachitanso utumiki wopatulika tikamachita kulambira kwa pabanja, tikamathandiza nawo pa ntchito yopereka thandizo kwa abale ndi alongo athu amene akuvutika, tikamadzipereka kugwira ntchito zosiyanasiyana pamisonkhano ikuluikulu kapena kukatumikira ku Beteli. (Aheb. 13:16; Yak. 1:27) Tikamaona kuti kulambira koyera n’kofunika kwambiri tidzachita “utumiki wopatulika usana ndi usiku.” Timasangalala kulambira Mulungu wathu Yehova.​—Chiv. 7:15.

a Mawu ena a Chiheberi amene amatanthauza kulambira amatanthauzanso “kutumikira.” Choncho kulambira kumaphatikizapo kutumikira.​—Eks. 3:12, mawu am’munsi.