Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 16A

Kodi Yerusalemu Ankaimira Matchalitchi Amene Amati ndi a Chikhristu?

Kodi Yerusalemu Ankaimira Matchalitchi Amene Amati ndi a Chikhristu?

M’mbuyomu mabuku athu ankanena kuti Yerusalemu amene anapandukira Yehova akuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Zimene zinkachitika ku Yerusalemu, kuphatikizapo kulambira mafano komanso zopanda chilungamo zimene zinali ponseponse, zimatikumbutsa zimene zikuchitika m’matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Koma m’zaka zaposachedwapa mabuku athu kuphatikizapo limene mukuwerengali, sanenanso kuti chinthu china chikuimira chinthu chinachake pofotokoza ulosi pokhapokha ngati pali zifukwa zomveka bwino za m’Baibulo. Kodi pali zifukwa za m’Malemba zonenera kuti Yerusalemu ankaimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu? Ayi palibe.

Taganizirani mfundo iyi: Nthawi inayake Yerusalemu anali likulu la kulambira koyera. Patapita nthawi, anthu a mumzindawo anapandukira Mulungu. Mosiyana ndi zimenezi, matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu sanayambe alambirapo Mulungu m’njira yovomerezeka. Kungochokera pamene matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu anayambika mu 400  C.E., nthawi zonse akhala akuphunzitsa zabodza.

Kuwonjezera pamenepo, Yerusalemu atawonongedwa ndi a Babulo, Yehova anabwezeretsa mzindawo ndipo unakhalanso likulu la kulambira koona. Koma mosiyana ndi zimenezi, matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu sanayambe akhalapo pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo akadzawonongedwa pa chisautso chachikulu sadzabwezeretsedwanso.

Ndiye tikaganizira mfundo zimenezi tinganene kuti chiyani? Tikaona maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa pa Yerusalemu amene anali wosakhulupirika, tinganene kuti ‘Zimenezi n’zofanana ndi zimene tikuona m’matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu masiku ano.’ Koma zikuoneka kuti palibe chifukwa cha m’Malemba chonenera kuti Yerusalemu akuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu.