Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 20A

Kugawa Dziko

Kugawa Dziko

Mmene anafotokozera malire oyezedwa bwino adzikolo, zinatsimikizira Ayuda amene anali ku ukapolo kuti dziko lawo lokondedwa lidzabwezeretsedwadi. Kodi masomphenyawa akutiphunzitsa chiyani masiku ano? Onani zinthu ziwiri zimene tikuzipeza m’masomphenyawa:

Malo otetezeka komanso ntchito yofunika

Munthu aliyense amene adzabwerere kwawo kuchokera ku ukapolo adzakhala ndi cholowa m’Dziko Lolonjezedwa lobwezeretsedwa. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso atumiki onse a Yehova ali ndi malo m’paradaiso wauzimu. Kaya tikuchita zambiri kapena zochepa m’gulu la Yehova, tili ndi malo otetezeka komanso ntchito yofunika kwambiri m’paradaiso wauzimu. Yehova amaona kuti atumiki ake onse ndi ofanana komanso ndi amtengo wapatali.

Malo ofanana

M’masomphenya a Ezekieli, dera lililonse m’Dziko Lolonjezedwa lobwezeretsedwa, linkathandiza anthu okhala m’dziko limenelo kupeza zinthu zabwino za m’dzikomo mofanana. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso Yehova wapereka mwayi wofanana kwa atumiki ake onse wopeza madalitso m’paradaiso wauzimu.