BOKOSI 10C
Adzatithandiza Kuti Tiimirirenso
TINGALIMBIKITSIDWE tikamaganizira zimene tikuphunzira m’masomphenya ochititsa chidwi opezeka pa Ezekieli 37:1-14. Tingagwiritse ntchito zimene tikuphunzirazo pa moyo wathu. Kodi tikuphunzira chiyani?
Nthawi zina tingamade nkhawa kwambiri chifukwa cha mavuto komanso mayesero amene tikukumana nawo pa moyo wathu ndipo tingatope n’kumavutika kupirira. Koma pa nthawi ngati imeneyi tingalimbikitsidwe tikamaganizira za masomphenya obwezeretsa amene Ezekieli anawafotokoza momveka bwino. N’chifukwa chiyani tikutero? Ulosiwu ukutiphunzitsa kuti Mulungu amene ali ndi mphamvu zopereka moyo kwa mafupa opanda moyo, angathe kutipatsa mphamvu zoti tilimbane ndi mavuto amene tikukumana nawo ngakhale amene angaoneke ngati ndi osatheka kuwagonjetsa. Komanso amafunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo pothandiza anthu ake.—Werengani Salimo 18:29; Afil. 4:13.
Zimenezi zikutikumbutsa zomwe mneneri Mose ananena zaka zambiri nthawi ya Ezekieli isanafike, kuti Yehova ali ndi mphamvu komanso amafunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo pothandiza anthu ake. Mose analemba kuti: “Mulungu ndi malo ako othawirapo kuyambira kalekale, iye wakunyamula mʼmanja ake omwe adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27) Inde, tisamakayikire kuti tikamadalira Yehova pamene tikukumana ndi mavuto, iye adzatinyamula m’manja mwake n’kumatidzutsa pang’onopang’ono mpaka titaimiriranso.—Ezek. 37:10.