BOKOSI 16B
Kuusa Moyo ndi Kubuula, Kulemba Chizindikiro Komanso Kuphwanya—Kodi Zimenezi Zidzachitika Liti Nanga Zidzachitika Bwanji?
Masomphenya amene ali mu Ezekieli chaputala 9 akukwaniritsidwanso masiku ano. Tikamvetsa mmene zinthu zidzakhalire, zingatithandize kukhala olimba mtima pamene mapeto a dziko loipali akuyandikira
“Kuusa moyo ndi kubuula”
KODI KUDZACHITIKA LITI?: M’masiku otsiriza chisautso chachikulu chisanayambe
KODI KUDZACHITIKA BWANJI?: Anthu owongoka mtima akusonyeza mwa zolankhula ndi zochita zawo kuti akudana ndi makhalidwe oipa a m’dzikoli. Anthu amenewa amamvetsera uthenga wabwino umene ukulalikidwa, akupitiriza kusonyeza makhalidwe a Khristu, amabatizidwa posonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova ndipo amathandiza mokhulupirika abale ake a Khristu
“Kulemba chizindikiro”
KODI KUDZACHITIKA LITI?: Pa chisautso chachikulu
KODI KUDZACHITIKA BWANJI?: Munthu amene ali ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki akuimira Yesu Khristu akadzabwera ngati woweruza wa mitundu yonse ya anthu. A khamu lalikulu adzaweruzidwa kapena kuti kulembedwa chizindikiro kuti ndi nkhosa. Zimenezi zikusonyeza kuti adzapulumuka pa Aramagedo
“Kuphwanya”
KODI KUDZACHITIKA LITI?: Pa Aramagedo
KODI KUDZACHITIKA BWANJI?: Yesu Khristu ndi gulu lake lankhondo lakumwamba, lomwe ndi angelo komanso olamulira anzake okwana 144,000, adzawonongeratu dziko loipali n’kupulumutsa anthu amene akulambira Mulungu woona ndipo adzawalowetsa dziko lapansi latsopano lolungama