Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 18A

Yehova Akuchenjeza Anthu Kuti Kukubwera Nkhondo Yaikulu

Yehova Akuchenjeza Anthu Kuti Kukubwera Nkhondo Yaikulu

M’Baibulo muli maulosi ambiri amene amachenjeza za nkhondo imene ikubwera. Pa nkhondo imeneyi Yehova adzawononga anthu onse amene amamutsutsa komanso kutsutsa anthu ake. M’munsimu muli ena mwa maulosi amenewa. Taonani kufanana kumene kulipo pakati pa machenjezowa komanso muone zimene Yehova wachita poonetsetsa kuti anthu onse ali ndi mwayi wakumva komanso kutsatira machenjezowo.

KALE KU ISIRAELI

EZEKIELI: “‘Ndidzamuyambitsira nkhondo mʼmapiri anga onse kuti amuwononge,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”​—Ezek. 38:18-23.

YEREMIYA: “[Yehova] adzapereka yekha chiweruzo kwa anthu onse. Ndipo anthu oipa adzawapha ndi lupanga.”​—Yer. 25:31-33.

DANIELI: “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene . . . udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa.”​—Dan. 2:44.

NTHAWI YA ATUMWI

YESU: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko mpaka lero, ndipo sichidzachitikanso.”​—Mat. 24:21, 22.

PAULO: “Yesu . . . limodzi ndi angelo ake amphamvu . . . adzabwezera chilango kwa anthu osadziwa Mulungu.”​—2 Ates. 1:6-9.

PETULO: “Tsiku la Yehova lidzafika ngati wakuba, . . . moti dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.”​—2 Pet. 3:10.

YOHANE: “Mʼkamwa [mwa Yesu] munkatuluka lupanga lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu.”​—Chiv. 19:11-18.

MASIKU ANO

Baibulo ndi buku limene lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse

ATUMIKI A YEHOVA A MASIKU ANO . . .

  • Akufalitsa mabuku mabiliyoni othandiza pophunzira Baibulo omwe ali m’zilankhulo mahandiredi ambiri

  • Amalalikira kwa maola mamiliyoni ambirimbiri chaka chilichonse