BOKOSI 9D
Maulosi Okhudza Ukapolo ndi Kubwezeretsedwa
Maulosi ambiri okhudza ukapolo wa Ayuda ku Babulo wakale anakwaniritsidwa m’njira ziwiri. Kukwaniritsidwa kwakukulu kunachitika pamene Akhristu anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo Wamkulu. Onani zitsanzo zotsatirazi.
1. MACHENJEZO |
2. UKAPOLO |
3. KUBWEZERETSEDWA |
|
---|---|---|---|
KUKWANIRITSIDWA KOYAMBA |
Chaka cha 607 B.C.E. chisanafike—Yesaya, Yeremiya ndi Ezekieli anachenjeza anthu a Mulungu koma anthu ambiri anapitiriza kupandukira Mulungu |
607 B.C.E.—Yerusalemu anawonongedwa, anthu a Mulungu anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo |
537 B.C.E. kupita m’tsogolo—Ayuda okhulupirika amene anatsala anabwerera ku Yerusalemu, anamanga kachisi n’kuyambiranso kulambira koyera |
KUKWANIRITSIDWA KWAKUKULU |
Nthawi ya atumwi—Yesu, Paulo ndi Yohane anachenjeza mpingo komabe anthu anapitiriza kupandukira Mulungu |
Kuyambira zaka za m’ma 100 C.E.—Akhristu oona anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo Wamkulu |
1919 C.E. kupita m’tsogolo—Yesu atayamba kulamulira monga mfumu, Akhristu okhulupirika odzozedwa anamasulidwa ku ukapolo wauzimu ndipo kulambira koyera kunabwezeretsedwa |