Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 19B

Mtsinje Waung’ono Unakhala Waukulu

Mtsinje Waung’ono Unakhala Waukulu

Ezekieli anaona kamtsinje kakang’ono kakuchokera m’nyumba yopatulika ya Yehova ndipo mozizwitsa unakhala mtsinje waukulu utangodutsa kamtunda kochepa. M’mbali mwa mtsinjewo, Ezekieli anaona mitengo ikuluikulu imene imabereka zipatso zokoma komanso kuchiritsa anthu. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

Mtsinjewo Ukubweretsa Madalitso

KALE: Ayuda omwe anali ku ukapolo atabwerera kudziko lakwawo analandira madalitso ochuluka pamene anathandiza nawo kubwezeretsa kulambira koyera pakachisi

MASIKU ANO: Mu 1919 kulambira koyera kunabwezeretsedwa ndipo zinatsegula mwayi wa madalitso ankhaninkhani kwa atumiki okhulupirika a Mulungu

M’TSOGOLO: Pambuyo pa Aramagedo, Yehova adzatidalitsa mwakuthupi komanso mwauzimu

Madzi Opatsa Moyo

KALE: Yehova anadalitsa kwambiri anthu ake omvera ngakhale pamene chiwerengero chawo chinkawonjezeka ndipo anawathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino mwauzimu

MASIKU ANO: M’Paradaiso wauzimu amene akukulirakulira anthu ambiri akulandira madalitso auzimu kuchokera kwa Yehova ndipo zawathandiza kuti akhale amoyo mwauzimu

M’TSOGOLO: Anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo komanso anthu mamiliyoni ambirimbiri amene adzaukitsidwe, adzasangalala ndi madalitso ochokera kwa Yehova ndipo madalitsowo adzakhala okwanira kwa aliyense

Mitengo ya Zipatso Komanso Yochiritsa

KALE: Mwauzimu Yehova anadyetsa anthu ake okhulupirika m’dziko lobwezeretsedwa. Iye anawachiritsanso matenda auzimu amene anadwala kwa nthawi yaitali

MASIKU ANO: Mfundo zambiri za choonadi cha m’Baibulo zikuthandiza anthu a Mulungu kuti akhalebe okhulupirika kwa iye komanso kuti azipewa machimo akuluakulu ndimaganizo oipa a anthu am’dzikoli

M’TSOGOLO: Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000, adzathandiza anthu onse omvera kuti akhale angwiro ndipo adzasangalala ndi moyo wathanzi komanso wangwiro kwamuyaya