Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 9E

“Nthawi Yobwezeretsa Zinthu Zonse”

“Nthawi Yobwezeretsa Zinthu Zonse”

MACHITIDWE 3:21

Pamene mtumwi Petulo ananena za “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse,” ankalosera za nthawi yapadera imene inayamba pamene Khristu anakhala pampando wachifumu mpaka kumapeto kwa Ulamuliro wake wa Zaka 1,000.

  1. 1914​—Yesu Khristu wakhala pampando wachifumu kumwamba. Anthu a Mulungu anabwezeretsedwa mwauzimu kuyambira mu 1919

    Masiku Otsiriza

  2. ARAMAGEDO​—Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu unayamba, ndipo “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse” inaphatikizapo madalitso amene anthu okhulupirika padziko lapansi analandira

    Ulamuliro wa Zaka 1,000

  3. KUTHA KWA ULAMULIRO WA KHRISTU WA ZAKA 1,000​—Yesu wamaliza ntchito yonse yobwezeretsa zinthu ndipo akupereka Ufumu kwa Atate ake

    Paradaiso Wamuyaya

ULAMULIRO WA YESU UDZACHITITSA KUTI . . .

  • dzina la Mulungu lilemekezedwe

  • anthu asadzadwalenso

  • achikulire adzakhalenso anyamata

  • amene anafa adzauke

  • anthu okhulupirika adzakhale angwiro

  • dziko lapansi lidzakhale Paradaiso