Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 14A

Zimene Tikuphunzira M’masomphenya a Kachisi Amene Ezekieli Anaona

Zimene Tikuphunzira M’masomphenya a Kachisi Amene Ezekieli Anaona

Kulambira Koyera Kunakwezedwa Komanso Kutetezedwa

Kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya anali “paphiri lalitali kwambiri” (1). Kodi takweza kulambira koyera n’kukuika pamalo oyamba pa moyo wathu?

Mpanda (2), umene unazungulira malo onse aakulu pamene panali kachisi (3), umatikumbutsa kuti sitikuyenera kulola china chilichonse kuti chiipitse kulambira koyera. Lemba la Ezekieli 42:20 likunena kuti panali mpanda umene unkasiyanitsa “malo opatulika ndi malo wamba.” Ndiye ngati “malo opatulika” ankasiyanitsidwa ndi “malo wamba” ngakhale kuti m’malo wambawo simunkachitika choipa chilichonse, kodi amene akulambira Yehova masiku ano sakuyenera kupewa khalidwe lodetsa kapena lachiwerewere?

Madalitso Osatha

Mtsinje ukuchokera kukachisi ndipo ukukula n’kubweretsa moyo ndi chonde m’dziko (4). Tidzakambirana madalitso amenewa m’mutu 19 wa buku lino.

Onse Amatsatira Mfundo Zofanana

Mageti ataliatali (5) komanso mageti amkati (9) akutikumbutsa kuti Yehova ali ndi mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino zimene amafuna kuti onse amene akumulambira azizitsatira. Onani kuti mageti amkati ndi akunja ndi ofanana mbali zonse. Zimenezi n’zomveka chifukwa mfundo zolungama za Yehova n’zofanana kwa atumiki ake onse kaya ali ndi udindo otani kapena akuchita utumiki wotani.

Kudya Patebulo la Yehova

Zipinda zodyera (8) zimatikumbutsa kuti nthawi zakale, anthu ankadyanso nsembe zina zimene ankabweretsa kukachisi ndipo zinali ngati akudyera limodzi ndi Yehova. Koma zimenezi sizichitika m’kachisi wauzimu mmene Akhristu amalambirira Mulungu masiku ano chifukwa chakuti “nsembe imodzi” ya Khristu inaperekedwa kale. (Aheb. 10:12) Komabe timapereka nsembe zathu zotamanda Mulungu.​—Aheb. 13:15.

Zimene Mulungu Akutitsimikizira

Mwina mungaone kuti miyezo yosiyanasiyana imene yatchulidwa m’masomphenyawa ndi yovuta kumvetsa. Koma ikutiphunzitsa mfundo yofunika. Miyezoyi ikutsimikizira kuti cholinga cha Yehova chobwezeretsa kulambira koyera chidzakwaniritsidwa ndipo ndi chotsimikizika, n’cholondola komanso sichingasinthe mofanana ndi miyezo imeneyo. Ngakhale kuti Ezekieli sakutchula kuti anaona munthu aliyense m’masomphenyawo, iye analemba malangizo amphamvu a Yehova opita kwa ansembe, atsogoleri komanso anthu. Atumiki onse a Mulungu akuyenera kutsatira mfundo zake zolungama.