Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zimene Zasintha

Mfundo Zimene Zasintha

Kwa zaka zambiri, Nsanja ya Olonda yakhala ikufotokoza mfundo zimene zasintha zokhudza mmene timafotokozera ulosi wa Ezekieli. M’buku lino lakuti Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera muli mfundo zinanso zimene zasintha. Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa.

Kodi nkhope 4 za angelo zikuimira chiyani?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Nkhope iliyonse ya angelowo kapena kuti akerubiwo ikuimira limodzi mwa makhalidwe akuluakulu 4 a Yehova.

Zimene tikukhulupirira panopa: Ngakhale kuti nkhope iliyonse ya angelowo ikuimira limodzi mwa makhalidwe akuluakulu 4 a Yehova, nkhope 4 zonsezi tikaziona pamodzi zikuimira makhalidwe onse amene Yehova ali nawo. Komanso nkhope 4 za angelowo zikutithandiza kumvetsa kuti Yehova ali ndi mphamvu komanso ulemerero waukulu.

Chifukwa chake tasintha: M’Baibulo nambala ya 4 imaimira chinthu chomwe chili ndi zonse zofunika kapena kuti chokwanira. Choncho nkhope zonse 4 zikaoneka pa nthawi imodzi, sizimangoimira makhalidwe 4 okha, koma ndi maziko a umunthu wochititsa mantha wa Yehova. Komanso nkhope iliyonse ndi ya cholengedwa chomwe chikuimira ulamuliro, mphamvu zambiri komanso nyonga. Ngakhale zili choncho, zolengedwa zamphamvu 4 zonsezi zili pansi pa mpando wachifumu wa Yehova. Zolengedwa zimenezi zikuimira zinthu zimene Mulungu analenga, monga mmene nkhope 4 za kerubi aliyense zikusonyezera. Zimenezitu zikusonyeza kuti Yehova ndi Wolamulira Wamkulu kuposa wina aliyense.

Kodi munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki akuimira ndani?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki akuimira odzozedwa amene adakali padziko lapansi. Odzozedwa akamagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, panopa amakhala akuika zizindikiro pazipumi za anthu amene ali m’gulu la “khamu lalikulu.”​—Chiv. 7:9.

Zimene tikukhulupirira panopa: Munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki akuimira Yesu Khristu. Iye adzaika chizindikiro pa anthu amene ali m’gulu la khamu lalikulu, anthuwo akadzaweruzidwa kuti ndi nkhosa mkati mwa “chisautso chachikulu.”​—Mat. 24:21.

Chifukwa chake tasintha: Yehova wapereka udindo woweruza kwa Mwana wake. (Yoh. 5:22, 23) Mogwirizana ndi lemba la Mateyu 25:31-33, Yesu ndi amene adzaweruze komaliza kuti “nkhosa” ndi ndani komanso “mbuzi” ndi ndani.

Kodi atsikana awiri apachibale, Ohola ndi Oholiba, amene ankachita uhule akuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu omwe agawikana n’kukhala Chikatolika ndi Chipulotesitanti?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Ohola, yemwe ndi wamkulu (Samariya, likulu la Isiraeli) akuimira Chikatolika. Oholiba, yemwe ndi wamng’ono (Yerusalemu, likulu la Yuda) akuimira Chipulotesitanti.

Zimene tikukhulupirira panopa: Mahule awiri apachibalewa sakuimira mbali iliyonse ya matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Koma kupezeka kwa matchalitchiwa kumatithandiza kumvetsa mmene Yehova amamvera, anthu amene poyamba ankamutumikira mokhulupirika akasiya kumulambira. Umu ndi mmene amamvera akamaona zipembedzo zonse zabodza.

Chifukwa chake tasintha: Palibe Lemba lililonse limene likusonyeza kuti Ohola ndi Oholiba akuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Pa nthawi ina, Isiraeli ndi Yuda anali ngati akazi okhulupirika a Yehova, koma matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu sanakhalepo pa mgwirizano wotero ndi Yehova. Kuwonjezera pamenepo, pamene anthu a Mulungu osakhulupirikawo akuwayerekezera ndi mahule muchaputala 16 ndi 23 cha Ezekieli, akuperekanso chiyembekezo choti adzasintha n’kukhalanso okhulupirika. Koma matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu, omwe ndi mbali ya Babulo Wamkulu, alibe chiyembekezo chimenecho.

Kodi matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu akuimira Yerusalemu wakale amene anapandukira Mulungu?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Yerusalemu wosakhulupirika akuimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Choncho kuwonongedwa kwa Yerusalemu kunkaimira kuwonongedwa kwa matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu.

Zimene tikukhulupirira panopa: Zimene zinkachitika mu Yerusalemu wosakhulupirika uja, monga kupembedza mafano komanso chinyengo chomwe chinali chofala, zimatikumbutsa za matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu. Koma sitinenanso kuti Yerusalemu ankaimira matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu.

Chifukwa chake tasintha: Palibe chifukwa chomveka cha m’Malemba choti tizinenera kuti chinthu china chikuimira chinachake. Mosiyana ndi Yerusalemu wakale, matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu sanayambe alambirapo Mulungu m’njira yovomerezeka. Tikudziwanso kuti kwakanthawi, Yehova anakhululukira Yerusalemu. Koma palibe chiyembekezo choti zimenezi zidzachitikiranso matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu.

Kodi masomphenya a chigwa chimene chinali ndi mafupa ouma anakwaniritsidwa bwanji?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Mu 1918 Akhristu odzozedwa amene ankazunzidwa, anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo Wamkulu. Zimenezi zitachitika, iwo anali ngati afa chifukwa ntchito yawo inali itatsala pang’ono kutheratu. Ukapolo wa nthawi yochepa umenewu unatha mu 1919 pamene Yehova anawathandiza kuti ayambirenso kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu.

Zimene tikukhulupirira panopa: Anthu amenewa, omwe anali mu ukapolo wauzimu, anakhala ngati akufa kwa nthawi yaitali ndipo zimenezi zinayambika chaka cha 1918 chisanafike. Ukapolo umenewu unayamba m’ma 100 C.E., ndipo unatha mu 1919 C.E. Zimenezi zikufanana ndi nthawi yaitali imene mbewu zinakhala zikukula mufanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole.

Chifukwa chake tasintha: Ukapolo wa Aisiraeli unatenga nthawi yaitali. Unayamba mu 740 B.C.E. ndipo unatha mu 537 B.C.E. Mu ulosi wokhudza mafupa, Ezekieli anafotokoza kuti mafupawo anali “ouma” kapena kuti “ouma kwambiri,” kusonyeza kuti anthu amene ankaimira mafupawo anakhala akufa kwa nthawi yaitali. Mafupawo anabwezeretsedwa mwapang’onopang’ono ndipo zinatenga nthawi yaitali.

Kodi ulosi wokhudza kuphatikiza ndodo ziwiri ukutanthauza chiyani?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, mgwirizano unasokonekera pakati pa anthu a Mulungu kwa kanthawi kochepa. Koma mu 1919, pambuyo pa nkhondoyi, Akhristu odzozedwa okhulupirika anayambiranso kuchita zinthu mogwirizana.

Zimene tikukhulupirira panopa: Ulosiwu unasonyeza kuti Yehova adzachititsa kuti anthu amene amamulambira akhale amodzi. Pambuyo pa chaka cha 1919, anthu ambiri amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padzikoli, anayamba kugwirizana ndi Akhristu odzozedwa omwe adakali padziko lapansi. Pamene nthawi ikudutsa, chiwerengero cha anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli chikungowonjezerekawonjezereka. Magulu awiri onsewa akulambira limodzi Yehova mogwirizana.

Chifukwa chake tasintha: Ulosiwu sukufotokoza za ndodo imodzi imene inathyoledwa n’kukhala ndodo ziwiri, kenako ndodozo n’kuziphatikiza kuti ikhale ndodo imodzi. Choncho ulosiwu sukufotokoza za gulu limodzi limene linagawanika n’kukhala magulu awiri, kenako n’kudzagwirizananso kukhala gulu limodzi. M’malomwake, ukufotokoza mmene magulu awiri omwe ndi osiyana adzakhalire ogwirizana.

Kodi Gogi wa ku Magogi ndi ndani?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Gogi wa ku Magogi ndi dzina la ulosi limene Satana ankadziwika nalo atathamangitsidwa kumwamba n’kubwera padziko lapansi pano.

Zimene tikukhulupirira panopa: Gogi wa ku Magogi akuimira mgwirizano wa mayiko apadziko lapansi amene adzaukire anthu omwe akulambira Mulungu m’njira yovomerezeka, pa chisautso chachikulu.

Chifukwa chake tasintha: Ulosi wofotokoza za Gogi woti adzaperekedwa kwa mbalame kuti akhale chakudya komanso kuti adzapatsidwa malo padziko lapansi kuti akhale manda ake, ukusonyeza kuti Gogi ameneyu si cholengedwa chauzimu. Kuwonjezera pamenepo, zimene Gogi adzachite poukira anthu a Mulungu, zikufanana ndi zimene buku la Danieli komanso la Chivumbulutso linafotokoza zokhudza zimene mayiko apadziko lapansi adzachite akamadzaukira anthu a Mulungu.​—Dan. 11:40, 44, 45; Chiv. 17:14; 19:19.

Kodi Ezekieli anaona komanso kuyendera kachisi wamkulu wauzimu amene pambuyo pake anafotokozedwa ndi mtumwi Paulo?

Zimene tinkakhulupirira poyamba: Kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya ndi wofanana ndi kachisi wauzimu amene mtumwi Paulo anafotokoza.

Zimene tikukhulupirira panopa: Ezekieli sanaone kachisi wauzimu amene anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E., koma anaona chifaniziro cha mmene kulambira koyera kunkayenera kuchitikira mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, pambuyo poti Ayuda abwerera kwawo kuchokera ku ukapolo. Zimene Paulo anafotokoza mouziridwa zokhudza kachisi wauzimu, zikukhudza kwambiri zimene Yesu anachita monga Mkulu wa Ansembe kuyambira mu 29 C.E., kufika mu 33 C.E. Masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona sakutchula za mkulu wa ansembe, koma akunena za kubwezeretsa kwa uzimu kumene kunayamba mu 1919 C.E. Choncho tikamafotokoza zinthu zosiyanasiyana komanso miyezo imene Ezekieli anaona m’masomphenya a kachisi, sitinenanso kuti zinthu zimenezi zikuimira zinthu zinazake. M’malomwake, timaganizira kwambiri zimene tikuphunzira m’masomphenya a Ezekieli zokhudza mfundo za Yehova za kulambira koyera.

Chifukwa chake tasintha: Kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenyawa ndi wosiyana ndi kachisi wauzimu m’njira zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, m’kachisi amene Ezekieli anaona munkaperekedwa nsembe zambiri za nyama. Koma m’kachisi wauzimu, ndi nsembe imodzi yokha imene inaperekedwa ‘kamodzi kokha kwamuyaya.’ (Aheb. 9:11, 12) Kwa zaka zambiri Khristu asanabwere padzikoli, nthawi inali isanakwane yoti Yehova aulule mfundo zozama za choonadi zokhudza kachisi wauzimu.