Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu

Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo ndi mphatso yosangalatsa yochokera kwa Mulungu?

KODI mumamva bwanji mnzanu akakupatsani mphatso? Mumasangalala kwambiri mwinanso n’kuitsegula nthawi yomweyo. Mphatsoyo imakuthandizani kudziwa kuti mnzanuyo amakuganizirani. Ndipo mumam’thokoza chifukwa cha mphatsoyo.

2 Baibulo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Buku limeneli limatithandiza kudziwa zinthu zomwe sitikanatha kuzidziwa popanda Baibulolo. Mwachitsanzo, limatiuza kuti Mulungu analenga kumwamba, dziko lapansi komanso mwamuna ndi mkazi oyamba. Limatiuzanso mfundo zomwe zingatithandize tikakumana ndi mavuto. Baibulo limafotokozanso mmene Mulungu adzakwaniritsire cholinga chake chokonzanso dzikoli kuti likhale labwino. Zimenezi zikusonyezadi kuti Baibulo ndi mphatso yosangalatsa.

3. Kodi kuphunzira Baibulo kukuthandizani kudziwa chiyani?

3 Kuphunzira Baibulo kukuthandizani kudziwa kuti Mulungu amafuna kuti mukhale naye pa ubwenzi. Mukamaphunzira zambiri zokhudza Mulungu ubwenzi wanu ndi iye udzakhala wolimba.

4. N’chiyani chimakuchititsani chidwi ndi Baibulo?

4 Baibulo lamasuliridwa m’ziyankhulo pafupifupi 2,600, ndipo Mabaibulo mabiliyoni ambiri akhala akupangidwa. Anthu oposa 90 pa 100 alionse padziko lapansi angathe kuwerenga Baibulo m’chiyankhulo chawo. Mabaibulo oposa 1 miliyoni amafalitsidwa mlungu uliwonse. Uwu ndi umboni wakuti palibe buku lina lofanana ndi Baibulo.

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo ‘linauziridwa ndi Mulungu’?

5 Baibulo ‘linauziridwa ndi Mulungu.’ (Werengani 2 Timoteyo 3:16.) Koma anthu ena amaganiza kuti: ‘Baibulo linalembedwa ndi anthu, ndiye zingatheke bwanji kukhala lochokera kwa Mulungu?’ Baibulo limafotokoza kuti: “Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:21) Zimene zinachitika polemba Baibulo n’zofanana ndi mmene zingakhalire ngati gogo atapempha mdzukulu wake kuti amulembere kalata. Kodi pamenepo tingati kalatayo ndi ya ndani? Kalatayo ndi ya gogoyo osati mdzukulu wakeyo. N’chimodzimodzinso ndi Baibulo. Mwiniwake ndi Mulungu osati anthu amene anawatuma kuti alembewo. Mulungu anatsogolera anthuwo kuti alembe maganizo ake. Choncho Baibulo ndi “mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13; onani Mawu Akumapeto 2.

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika likupezeka m’ziyankhulo zambiri

NKHANI ZA M’BAIBULO NDI ZOLONDOLA

6, 7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti nkhani za m’Baibulo ndi zogwirizana?

6 Ntchito yolemba Baibulo inatenga zaka zoposa 1,600. Anthu omwe anatumidwa kuti alembe Baibulo anakhala ndi moyo pa nthawi zosiyanasiyana. Ena mwa anthuwo anali ophunzira pamene ena anali osaphunzira. Mwachitsanzo, wina anali dokotala ndipo ena anali alimi, asodzi, abusa, aneneri, oweruza komanso mafumu. Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa ndi anthu osiyanasiyana, koma mfundo zake zonse n’zogwirizana. Zimene limanena m’chaputala china sizitsutsana ndi za m’chaputala china. *

7 Machaputala oyambirira a m’Baibulo amafotokoza mmene mavuto anayambira, pamene machaputala omalizira amatiuza mmene Mulungu adzathetsere mavutowa n’kukonzanso dzikoli kukhala paradaiso. Baibulo limafotokoza nkhani zimene zakhala zikuchitika zaka masauzande ambirimbiri ndipo nkhanizi zimasonyeza kuti nthawi zonse Mulungu amakwaniritsa cholinga chake.

8. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Baibulo limanena zoona pa nkhani zasayansi.

8 Baibulo silinalembedwe n’cholinga choti liphunzitse anthu mfundo zasayansi kapena kuti azidzaligwiritsa ntchito pophunzitsa ana asukulu komabe mfundo zonse zasayansi zimene limafotokoza n’zolondola. Mmenemu ndi mmenedi buku lochokera kwa Mulungu liyenera kukhalira. Mwachitsanzo, m’buku la Levitiko muli malangizo omwe Mulungu anapereka kwa Aisiraeli othandiza kuti matenda asamafalikire. Malangizo amenewa analembedwa kalekale kwambiri ndipo pa nthawiyo n’kuti anthu asanadziwe zoti pali tizilombo tomwe timayambitsa matenda. Baibulo limafotokozanso molondola kuti dziko lapansili lili m’malere. (Yobu 26:7) Ndipo pa nthawi imene anthu ambiri ankaganiza kuti dziko lapansi ndi lafulati, Baibulo linali litafotokoza kale kuti dzikoli ndi lozungulira.—Yesaya 40:22.

9. Kodi timaphunzira chiyani pa zimene olemba Baibulo anachita pofotokoza zinthu moona mtima?

9 Baibulo ndi lolondolanso likamafotokoza za mbiri yakale. Koma mabuku ambiri ofotokoza mbiri yakale sakhala odalirika chifukwa olemba ake salemba zoona zokhazokha. Mwachitsanzo, iwo nthawi zambiri salemba ngati mtundu wawo wagonjetsedwa kunkhondo. Koma olemba Baibulo ankalemba zoona ngakhale zokhudza kugonjetsedwa kwa mtundu wawo wa Isiraeli. Ndiponso ankalemba ngakhale zinthu zimene iwowo analakwitsa. Mwachitsanzo, m’buku la Numeri, Mose anafotokoza za zinthu zimene analakwitsa zomwe Mulungu anam’dzudzula nazo. (Numeri 20:2-12) Choncho kuona mtima kwa olemba Baibulo kukutiphunzitsa kuti ndi buku lochokeradi kwa Mulungu ndipo tiyenera kulikhulupirira.

M’BAIBULO MULI MALANGIZO OTHANDIZA KWAMBIRI

10. N’chifukwa chiyani malangizo a m’Baibulo ali othandiza kwambiri masiku ano?

10 Baibulo linauziridwa ndi Mulungu ndipo ndi lopindulitsa pa “kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.” (2 Timoteyo 3:16) Malangizo a m’Baibulo ndi othandizadi kwambiri masiku ano. Izi zili choncho chifukwa Yehova ndi amene anatilenga ndipo amadziwa bwino mmene timaganizira komanso mmene timamvera. Iye amatidziwa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziwira ndipo amafuna kuti tizikhala osangalala. Amadziwanso zinthu zomwe zingatithandize komanso zomwe tiyenera kupewa.

11, 12. (a) Kodi Yesu anafotokoza malangizo otani m’machaputala 5 mpaka 7 a buku la Mateyu? (b) Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandizenso pa nkhani ziti?

11 M’machaputala 5 mpaka 7 a buku la Mateyu, muli malangizo abwino kwambiri amene Yesu anapereka onena za mmene tingakhalire osangalala, mmene tingathetsere kusamvana, mmene tingapempherere komanso mmene tingakhalire ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ndalama. Ngakhale kuti malangizowa anaperekedwa zaka 2,000 zapitazo, adakali amphamvu ndiponso othandiza mpaka pano.

12 M’Baibulo muli malangizo a Yehova omwe angatithandize kukhala ndi banja labwino, kukhala olimbikira ntchito komanso kukhala mwamtendere ndi anthu ena. Mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwa anthu onse ndipo malangizo ake ndi opindulitsa nthawi zonse.—Werengani Yesaya 48:17; onani Mawu Akumapeto 3.

MAULOSI A M’BAIBULO NDI ODALIRIKA

Yesaya ananeneratu kuti Babulo adzawonongedwa

13. Kodi Yesaya ananeneratu kuti n’chiyani chidzachitikire mzinda wa Babulo?

13 Maulosi ambiri a m’Baibulo anakwaniritsidwa kale. Mwachitsanzo, Yesaya ananeneratu kuti mzinda wa Babulo udzawonongedwa. (Yesaya 13:19) Iye anafotokoza bwinobwino mmene mzindawo udzagonjetsedwere. Mzinda wa Babulo unali wotetezeka chifukwa unali ndi mageti akuluakulu komanso unazunguliridwa ndi mtsinje. Koma Yesaya ananeneratu kuti madzi a mumtsinjewo adzaphwetsedwa ndiponso mageti a mzindawo adzasiyidwa osatseka ndipo oukirawo adzalanda mzindawo popanda kumenya nkhondo. Yesaya anali ataneneratunso kuti munthu amene adzagonjetse mzinda wa Babulo ndi Koresi.—Werengani Yesaya 44:27–45:2; onani Mawu Akumapeto 4.

14, 15. Kodi ulosi umene Yesaya ananena unakwaniritsidwa bwanji?

14 Patadutsa zaka 200 kuchokera pamene ulosiwu unalembedwa, asilikali anafika kuti aukire mzinda wa Babulo. Kodi mtsogoleri wawo anali ndani? Anali Koresi mfumu ya Perisiya monga mmene ulosi uja unanenera. Apa zonse zinali m’malo mwake kuti ulosi uja ukwaniritsidwe.

15 Usiku umene asilikali anaukira mzindawu, Ababulo anali paphwando. Iwo ankaona kuti ndi otetezeka chifukwa mzindawo unali ndi mpanda waukulu komanso unazunguliridwa ndi mtsinje. Koma Koresi ndi asilikali ake anakumba ngalande n’kupatutsa madzi a mumtsinjewo. Mtsinjewo unaphwera moti asilikali a ku Perisiyawo anatha kuwoloka. Koma kodi asilikaliwo akanalowa bwanji mumpanda wa mzindawo? Monga mmene ulosi uja unanenera, mageti a mzindawo anasiyidwa osatseka, choncho asilikaliwo analanda mzindawo popanda kumenya nkhondo.

16. (a) Kodi Yesaya ananeneratunso chiyani chokhudza mzinda wa Babulo? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti zimene Yesaya ananena zinakwaniritsidwa?

16 Yesaya ananeneratunso kuti m’Babulo simudzakhalanso munthu aliyense. Iye analemba kuti: “M’Babulo simudzakhalanso anthu, ndipo iye sadzakhalaponso ku mibadwomibadwo.” (Yesaya 13:20) Kodi zimenezi zinakwaniritsidwa? Inde. Malo amene panali mzinda wa Babulo, omwe ali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 80 kum’mwera kwa mzinda wa Baghdad ku Iraq, kuli mabwinja okhaokha. Mpaka pano, pamalo amenewa sipakhala munthu aliyense. Yehova anasesa mzinda wa Babulo “ndi tsache la chiwonongeko.”—Yesaya 14:22, 23. *

Malo opanda anthu, pomwe panali mzinda wa Babulo

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira zonse zimene Mulungu amatilonjeza?

17 Mfundo yoti maulosi ambiri a m’Baibulo anakwaniritsidwa imatithandiza kukhulupirira kuti zimene Baibulo linalonjeza zidzachitikadi. Sitikayikira kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake lokonzanso dzikoli kuti likhale paradaiso. (Werengani Numeri 23:19.) Tikuyembekezera “moyo wosatha, womwe Mulungu amene sanganame, analonjeza kalekale.”—Tito 1:2. *

BAIBULO LINGAKUTHANDIZENI KUSINTHA MOYO WANU

18. Kodi Paulo anafotokoza chiyani ponena za “mawu a Mulungu”?

18 Taphunzira kuti palibe buku lililonse lomwe lingafanane ndi Baibulo. Mfundo zake n’zogwirizana, ndipo likamafotokoza nkhani zasayansi kapena mbiri yakale, nthawi zonse limanena zolondola. Lilinso ndi malangizo abwino komanso maulosi amene anakwaniritsidwa kale. Komatu si zokhazi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?—Werengani Aheberi 4:12.

19, 20. (a) Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kudziwa mmene mulili? (b) Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mphatso ya Baibulo?

19 Baibulo lingakuthandizeni kusintha moyo wanu. Likhoza kukuthandizani kudziwa kuti ndinu munthu wotani. Lingakuthandizeninso kudziwa mmene mumaganizira komanso zimene zili mumtima mwanu. Mwachitsanzo, tikhoza kunena kuti timakonda Mulungu. Koma kuti tisonyeze kuti timamukondadi, tiyenera kuchita zimene Baibulo limanena.

20 Baibulo ndi buku lochokeradi kwa Mulungu ndipo iye amafuna kuti muziliwerenga, kuliphunzira komanso kulikonda. Choncho muyenera kuyamikira mphatso imeneyi ndipo musasiye kuphunzira Baibulo. Mukatero mudzamvetsa bwino cholinga cha Mulungu chokhudza anthu. M’mutu wotsatira, tidzaphunzira zambiri zokhudza cholinga chimenechi.

^ ndime 6 Anthu ena amanena kuti mfundo zina za m’Baibulo zimatsutsana, koma zimenezi si zoona. Onani Mutu 7 m’buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 Kuti mumve zambiri zokhudza maulosi a m’Baibulo, onani tsamba 27-29 m’kabuku kakuti Buku la Anthu Onse, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 17 Kuwonongedwa kwa Babulo ndi chitsanzo chimodzi cha maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa kale. Kuti mumve za maulosi onena za Yesu Khristu, onani Mawu Akumapeto 5.