Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 1

Mawu Oyamba Abwino

Mawu Oyamba Abwino

Machitidwe 17:22

MFUNDO YAIKULU: M’mawu anu oyamba, muyenera kunena zinthu zochititsa chidwi, kutchula zokhudza nkhani yanu komanso kusonyeza chifukwa chake nkhaniyo ili yothandiza kwambiri kwa omvera.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Kukopa chidwi. Sankhani funso, mawu enaake, zochitika zenizeni kapena nkhani imene omvera anu angachite nayo chidwi.

  • Fotokozani nkhani yanu. M’mawu anu oyamba muyenera kuthandiza anthu kudziwa nkhani imene mukambirane komanso cholinga chake.

  • Sonyezani chifukwa chake nkhaniyo ndi yofunika. Konzekerani nkhani yanu m’njira yoti igwirizane ndi zimene zingathandize anthu amene mukukambirana nawo. Anthuwo ayenera kuona mosavuta kuti nkhaniyo iwathandizadi.