Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 10

Kusinthasintha Mawu

Kusinthasintha Mawu

Miyambo 8:4, 7

MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula momveka bwino ndipo muzisinthasintha mawu, pena kukweza pena kutsitsa, pena kulankhula mofulumira pena pang’onopang’ono.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Pena muzikweza mawu pena kuwatsitsa. Mungakweze mawu kuti mutsindike mfundo yofunika kapena kuti mulimbikitse anthu kuchita zinazake. Mungachitenso zomwezo powerenga uthenga wachiweruzo wa m’Baibulo. Mungatsitse mawu pothandiza anthu kuyembekezera kumva mfundo inayake kapena pofotokoza zinthu zochititsa mantha kapena zodetsa nkhawa.

  • Pena muzilankhula mawu aakulu pena aang’ono. Ngati n’zololeka m’chilankhulo chanu, muzisintha mawu potsindika mfundo, ponena zinthu zazikulu kapena pofotokoza zinthu zimene zili patali. Muzisinthanso mawu ponena zinthu zomvetsa chisoni kapena zodetsa nkhawa.

  • Pena muzilankhula mofulumira pena pang’onopang’ono. Muzilankhula mofulumira posonyeza kusangalala koma pang’onopang’ono mukamatchula mfundo yofunika kwambiri.