Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 11

Kulankhula ndi Mtima Wonse

Kulankhula ndi Mtima Wonse

Aroma 12:11

MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula ndi mtima wonse kuti muziwafika pamtima anthu amene mukukambirana nawo.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzilankhula kuchokera mumtima. Mukamakonzekera komanso kukamba nkhani, muziganizira mmene ingathandizire anthu. Muziidziwa bwino nkhaniyo moti muzilankhula mfundo zanu kuchokera mumtima.

  • Muziganizira anthu. Muziganizira mmene mfundo imene mungawerenge kapena kuphunzitsa ingathandizire anthu. Muzifotokoza mfundozo m’njira yoti anthu aziona kuti ndi zothandiza.

  • Nkhani yanu izikhala yamoyo. Muzisonyeza kuti nkhaniyo yakufikani pamtima. Ndiyeno manja ndi nkhope yanu zizisonyeza mmene mukumvera mumtima.