Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 15

Kulankhula Motsimikiza

Kulankhula Motsimikiza

1 Atesalonika 1:5

MFUNDO YAIKULU: Muzisonyeza kuti mumakhulupirira kwambiri mfundo za choonadi ndipo simukukayikira kuti mfundo zimene mukunena n’zothandiza.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzikonzekera bwino. Pokonzekera muzidzifunsa kuti, Kodi mfundo za m’Malemba zingathandize bwanji munthu kufika pozindikira zoona zake pa nkhaniyi? Muzigwiritsa ntchito mawu osavuta pofotokoza mfundo zikuluzikulu. Muziganizira mmene zingathandizire anthu amene mukukambirana nawo. Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera.

  • Muzigwiritsa ntchito mawu osonyeza kutsimikiza. M’malo monena ndendende mmene mawu anawalembera m’mabuku athu, muzigwiritsa ntchito mawu anuanu. Muzigwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti simukukayikira zimene mukunena.

  • Muzilankhula mochokera pansi pa mtima komanso mosakayikira. Mawu anu asakwere kwambiri kapena kutsika kwambiri. Ngati n’zololeka kwanuko, muziyang’ana anthu amene mukukambirana nawo.