Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 18

Nkhani Yophunzitsadi Anthu

Nkhani Yophunzitsadi Anthu

1 Akorinto 9:19-23

MFUNDO YAIKULU: Muzithandiza anthu kuganiza mpaka kufika pozindikira kuti aphunziradi mfundo zothandiza.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Ganizirani zimene anthu akudziwa kale. M’malo mongofotokoza zimene anthu akuzidziwa kale, athandizeni kuiganizira nkhaniyo m’njira yatsopano.

  • Muzifufuza komanso kuganizira kwambiri nkhaniyo. Ngati n’zotheka, muzigwiritsa ntchito mfundo zimene anthu sakuzidziwa kwambiri kapena nkhani zimene zangochitika kumene pofotokozera mfundo zikuluzikulu. Muziganizira kwambiri nkhani yanu n’kumaona ngati mfundo zimene mukufuna kugwiritsa ntchito zikugwirizanadi ndi nkhaniyo.

  • Muzithandiza anthu kuona kuti nkhaniyo ndi yofunika kwambiri. Muzifotokoza mmene Malemba angathandizire anthu pa moyo wawo. Muzifotokoza mfundo zogwirizana ndi zimene zimachitikira anthu, zimene anthu amachita komanso zimene anthu amaganiza.