Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 19

Kuwafika Pamtima Anthu

Kuwafika Pamtima Anthu

Miyambo 3:1

MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kumvetsa zimene mukunena komanso kuzigwiritsa ntchito.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzithandiza anthu kuti azidzifufuza. Muzifunsa mafunso othandiza anthu kudzifufuza mumtima.

  • Muzithandiza anthu kukhala ndi zolinga zabwino. Thandizani anthu kudzifufuza kuti adziwe chifukwa chimene amachitira zinthu zabwino. Athandizeni kuti azichita zinthu chifukwa chokonda Yehova, anzawo komanso Mawu a Mulungu. Muzikambirana ndi anthu osati kuwauza zochita. Nkhani yanu ikamatha, anthu azikhala atalimbikitsidwa osati atachititsidwa manyazi. Azifunitsitsa kuchita zonse zimene angathe.

  • Muzithandiza anthu kuganizira za Yehova. Nkhani yanu izithandiza anthu kuona kuti malamulo komanso mfundo za m’Baibulo zimasonyeza makhalidwe a Yehova monga chikondi. Muzithandiza anthu kudziwa kuti zochita zawo zimakhudza Yehova ndipo azifunitsitsa kumusangalatsa.