Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 2

Kulankhula Mokambirana ndi Anthu

Kulankhula Mokambirana ndi Anthu

2 Akorinto 2:17

MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula mwachibadwa komanso kuchokera mumtima kuti anthu adziwe mmene nkhaniyo ikukukhudzirani komanso kuti mumawaganizira.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzikonzekera mokwanira ndipo muzipemphera. Muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni n’cholinga choti muziganizira kwambiri za uthenga wanu osati za inuyo. Muziganizira kwambiri mfundo zikuluzikulu zimene mukufuna kuuza anthu. Muzifotokoza mfundozo m’mawu anuanu osati kumangotchula ndendende mmene zilili pa autilaini.

  • Muzilankhula kuchokera mumtima. Muziganizira mmene uthengawo ungathandizire anthu amene mukulankhula nawo. Muziganizira kwambiri za anthuwo. Mukatero, nkhope yanu, thupi lanu ndiponso mawu anu zidzasonyeza kuti mumawaganizira ndipo ndinu anzawo.

  • Muziyang’ana anthu. Ngati n’zololeka kudera limene mukukhala, muziyang’ana anthu m’njira yoti maso anu aziphana. Pokamba nkhani, muziyang’ana munthu mmodzi pa nthawi imodzi, osati kumangomwazamwaza maso kuti muone gulu lonse nthawi imodzi.