PHUNZIRO 3
Kugwiritsa Ntchito Mafunso
Mateyu 16:13-16
MFUNDO YAIKULU: Muzigwiritsa ntchito mafunso oyenera kuti anthu akhale ndi chidwi, kuti mukambirane ndi anthu, komanso kuti mutsindike mfundo zofunika.
MMENE MUNGACHITIRE:
-
Muzithandiza anthu kuti akhale ndi chidwi. Muzifunsa mafunso othandiza anthu kuti azifuna kumva zambiri.
-
Muzikambirana ndi anthu. Kuti anthu akhulupirire mfundo zimene mukunena, muyenera kufunsa mafunso angapo owathandiza kuti atsatire mpaka kufika potsimikizira mfundozo.
-
Muzitsindika mfundo zofunika. Funsani funso limene lingachititse anthu kuyembekezera kuti amve mfundo yofunika. Muzifunsa mafunso obwereza pambuyo pa mfundo yofunika iliyonse kapena pomaliza nkhani yanu.