Ziwerengero Zonse za 2017
Nthambi za Mboni za Yehova: 90
Mayiko Amene Anatumiza Lipoti: 240
Mipingo Yonse: 120,053
Opezeka pa Chikumbutso Padziko Lonse: 20,175,477
Amene Anadya Zizindikiro Padziko Lonse: 18,564
Ofalitsa Onse Amene Anagwira Ntchito Yolalikira *: 8,457,107
Avereji ya Ofalitsa Amene Ankalalikira Mwezi Uliwonse: 8,248,982
Kuwonjezeka kwa Ofalitsa Kuchokera mu 2016: 1.4%
Obatizidwa Onse *: 284,212
Avereji ya Apainiya * Okhazikika Mwezi Uliwonse: 1,249,946
Avereji ya Apainiya Othandiza Mwezi Uliwonse: 439,571
Maola Onse Amene Tinalalikira: 2,046,000,202
Avereji ya Maphunziro a Baibulo * Mwezi Uliwonse: 10,071,524
M’chaka cha utumiki cha 2017, * a Mboni za Yehova anagwiritsa ntchito ndalama zoposa madola 202 miliyoni a ku America posamalira apainiya apadera, amishonale ndi oyang’anira dera pa utumiki wawo. Padziko lonse pali abale ndi alongo okwana 19,730 amene akutumikira m’maofesi a nthambi. Onsewa ali m’Gulu Lapadziko Lonse la Atumiki Apadera a Nthawi Zonse a Mboni za Yehova.
^ ndime 7 Wofalitsa ndi munthu amene amalalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kuti mudziwe mmene timapezera chiwerengerochi, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi a Mboni za Yehova Alipo Angati Padziko Lonse?”
^ ndime 10 Kuti mudziwe zimene mungachite kuti mubatizidwe n’kukhala wa Mboni za Yehova, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale wa Mboni za Yehova?”
^ ndime 11 Mpainiya ndi wa Mboni wachitsanzo chabwino amene amadzipereka kuti azilalikira uthenga wabwino kwa maola enaake mwezi uliwonse.
^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Phunziro la Baibulo N’chiyani?”
^ ndime 15 Chaka chautumiki cha 2017 chinayamba pa September 1, 2016, ndipo chinatha pa August 31, 2017.