Ziwerengero Zonse za 2019
Nthambi za Mboni za Yehova: 87
Mayiko Amene Anatumiza Lipoti: 240
Mipingo Yonse: 119,712
Opezeka pa Chikumbutso Padziko Lonse: 20,919,041
Amene Anadya Zizindikiro Padziko Lonse: 20,526
Ofalitsa Onse Amene Anagwira Ntchito Yolalikira *: 8,683,117
Avereji ya Ofalitsa Amene Ankalalikira Mwezi Uliwonse: 8,471,008
Kuwonjezeka kwa Ofalitsa Kuchokera mu 2018: 1.3
Obatizidwa Onse *: 303,866
Avereji ya Apainiya * Okhazikika Mwezi Uliwonse: 1,277,738
Avereji ya Apainiya Othandiza Mwezi Uliwonse: 464,980
Maola Onse Amene Tinalalikira: 2,088,560,437
Avereji ya Maphunziro a Baibulo * Mwezi Uliwonse: 9,618,182
M’chaka cha utumiki cha 2019, * a Mboni za Yehova anagwiritsa ntchito ndalama zoposa madola $224 miliyoni posamalira apainiya apadera, amishonale ndi oyang’anira dera pa utumiki wawo. Padziko lonse pali abale ndi alongo okwana 20,858 amene akutumikira m’maofesi a nthambi. Onsewa ali m’Gulu Lapadziko Lonse la Atumiki Apadera a Nthawi Zonse a Mboni za Yehova.
^ ndime 7 Wofalitsa ndi munthu amene amalalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kuti mudziwe mmene timapezera chiwerengerochi, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi a Mboni za Yehova Alipo Angati Padziko Lonse?”
^ ndime 10 Kuti mudziwe zimene mungachite kuti mubatizidwe n’kukhala wa Mboni za Yehova, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale wa Mboni za Yehova?”
^ ndime 11 Mpainiya ndi wa Mboni wachitsanzo chabwino amene amadzipereka kuti azilalikira uthenga wabwino kwa maola enaake mwezi uliwonse.
^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Phunziro la Baibulo N’chiyani?”
^ ndime 15 Chaka chautumiki cha 2019 chinayamba pa 1 September 2018, ndipo chinatha pa 31 August 2019.