Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ana; Achinyamata

Ana; Achinyamata

Mmene Mulungu amaonera ana

Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ana komanso achinyamata ndi ofunika kwambiri kwa iye?

De 6:6, 7; 14:28, 29; Sl 110:3; 127:3-5; 128:3, 4; Yak 1:27

Onaninso Yob 29:12; Sl 27:10; Miy 17:6

Onaninso “Banja

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 1:27, 28​—Cholinga cha Yehova chinali chakuti anthu abereke ana ndi kudzadza padziko lonse lapansi

    • Ge 9:1​—Pambuyo pa Chigumula, Mulungu anauza Nowa ndi ana ake kuti abereke ana ndi kudzaza dziko lonse lapansi

    • Ge 33:5​—Yakobo yemwe anali mtumiki wokhulupirika ankaona kuti ana ake ndi mphatso yochokera kwa Mulungu

    • Mko 10:13-16​—Yesu ankakonda ana ngati mmene Atate wake ankachitira

Kodi Yehova amamva bwanji anthu akamachitira nkhanza ana kapena kuwapondereza?

Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zikusonyeza kuti tisamayembekezere kuti ana azichita zinthu kapena kugwira ntchito ngati akuluakulu?

Nu 1:3; 1Ak 13:11

  • Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:

    • Ge 33:12-14​—Yakobo anazindikira kuti ana ake ang’onoang’ono sangakwanitse kuyenda mofulumira ngati akuluakulu

Kodi tiyenera kuimba Mulungu mlandu chifukwa cha zinthu zoipa zimene ana akukumana nazo padzikoli?

Yob 34:10; Yak 1:13; 1Yo 5:19

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 5:18, 20, 23-25​—Yesu anafotokoza kuti anthufe timadwala chifukwa cha uchimo

    • Aro 5:12​—Mtumwi Paulo anafotokoza chifukwa chake timachimwa ndiponso kufa

Kodi Yehova amatitsimikizira bwanji kuti adzathetsa mavuto amene ana ndi akulu omwe amakumana nawo?

Ngati makolo akuchita zinthu zoipa komanso zankhanza, kodi zikutanthauza kuti ana awo adzakhala osafunika kapenanso ankhanza ngati makolo awowo?

De 24:16; Eze 18:1-3, 14-18

Onaninso De 30:15, 16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mf 18:1-7; 2Mb 28:1-4​—Hezekiya anali mfumu yabwino komanso yokhulupirika ngakhale kuti bambo ake anali ankhanza ndipo anapha ana awo ena

    • 2Mf 21:19-26; 22:1, 2​—Yosiya anali mfumu yabwino ngakhale kuti bambo ake a Amoni anali mfumu yoipa kwambiri

    • 1Ak 10:11, 12​—Mtumwi Paulo anafotokoza kuti tingathe kuphunzirapo kanthu pa zimene ena analakwitsa n’kusankha kupewa kuchita zimene iwo analakwitsazo

    • Afi 2:12, 13​—Mtumwi Paulo anatikumbutsa kuti tipitirize kukhala okhulupirika kuti tidzapulumuke

Zimene ana ndi achinyamata ayenera kuchita

Kodi Yehova amawaona bwanji ana amene akukhalabe pakhomo la kholo lawo lomwe limaopa Yehova?

1Ak 7:14

  • Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:

    • Ge 19:12, 15​—Chifukwa china chimene angelo anatetezera ana aakazi a Loti chinali chakuti bambo awo anali munthu wolungama

Ngati ana ali ndi makolo oopa Mulungu, kodi zikutanthauza kuti nawonso ali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa cha makolo awowo?

Miy 20:11; Eze 18:5, 10-13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Le 10:1-3, 8, 9​—Ana a Mkulu wa Ansembe Aroni anaphedwa mwina chifukwa choledzera

    • 1Sa 8:1-5​—Ngakhale kuti Samueli anali mneneri wolungama, ana ake anali osakhulupirika

Kodi ana ayenera kumachita chiyani kuti azisangalatsa Mulungu?

N’chifukwa chiyani ana ayenera kumapezeka pamisonkhano?

De 31:12, 13; Ahe 10:24, 25

  • Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:

    • Mt 15:32-38​—Pamagulu a anthu amene Yesu ankawaphunzitsa, pankapezekanso ana

Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti ana azimutumikira?

Sl 8:2; 148:12, 13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 17:4, 8-10, 41, 42, 45-51​—Ngakhale kuti Davide anali mwana, Yehova anamugwiritsa ntchito kuti alemekeze dzina Lake mwa kugonjetsa munthu woopsa

    • 2Mf 5:1-15​—Yehova anagwiritsa ntchito kamtsikana ka Chiisiraeli kuti athandize mkulu wa asilikali yemwe sanali mu Isiraeli kuphunzira zokhudza Mulungu woona

    • Mt 21:15, 16​—Yesu anayamikira zimene ana anachita pomulemekeza monga Mesiya

Kodi Yehova amawaona bwanji ana amene makolo awo ndi osakhulupirira?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Nu 16:25, 26, 32, 33​—Anthu ena ataukira mneneri Mose ndi Mkulu wa Ansembe Aroni, Yehova anawalanga pamodzi ndi mabanja awo omwenso anaukira nawo limodzi

    • Nu 26:10, 11​—Kora anaphedwa chifukwa chopandukira Mulungu koma zikuoneka kuti ana ake sanaphedwe nawo chifukwa choti anali okhulupirika

N’chifukwa chiyani achinyamata masiku ano ayenera kusankha bwino anthu ocheza nawo?

Kodi achinyamata Achikhristu ayenera kumacheza ndi anthu otani?

2Ti 2:22

Onaninso “Anthu Ocheza Nawo