Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi

Chikondi

Kodi anasonyeza bwanji chikondi?

Yer 31:3; Yoh 3:16; Aro 5:8; 1Yo 4:8, 19

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 1:1, 26-31; 2:8, 9, 15, 16​—Yehova anasonyeza chikondi pokonza dziko lapansili kukhala paradaiso ndipo anapatsa anthu oyambirira zinthu zambiri zabwino m’munda wa Edeni

    • Sl 104:27-30​—Wamasalimo anayamikira Yehova chifukwa chosonyeza chikondi pa cholengedwa chilichonse

Kodi tingasonyeze bwanji chikondi?

Yoh 13:34, 35; 15:12, 13; 1Pe 4:8; 1Yo 4:10, 11; 5:3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 22:36-39​—Yesu ananena za malamulo awiri aakulu kwambiri ndipo onsewo ndi okhudza chikondi

    • 1Ak 13:1-8​—Mtumwi Paulo anafotokoza kufunika kwa chikondi; komanso anatisonyeza zimene tingachite posonyeza chikondi