Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilungamo

Chilungamo

Ndi ndani yekha amene ali ndi ulamuliro wonena zimene zili zoyenera kapena zolungama?

De 32:4; Eze 33:17-20

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 18:23-33​—Yehova anaonetsa Abulahamu kuti Iye ndi woweruza wachilungamo

    • Sl 72:1-4, 12-14​—Wamasalimo anauziridwa kulemba zotamanda Mesiya kuti idzakhala Mfumu yachilungamo ngati Yehova

Kodi timapindula bwanji tikamatsatira mfundo zolungama za Yehova?

Sl 37:25, 29; Yak 5:16; 1Pe 3:12

Onaninso Sl 35:24; Yes 26:9; Aro 1:17

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yob 37:22-24​—Elihu anatamanda chilungamo cha Yehova, yemwe amachititsa kuti atumiki ake azimulemekeza chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa

    • Sl 89:13-17​—Wamasalimo anatamanda Yehova chifukwa cha ulamuliro wake wachilungamo

Kodi kufunafuna chilungamo cha Mulungu kutanthauza chiyani?

Eze 18:25-31; Mt 6:33; Aro 12:1, 2; Aef 4:23, 24

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 6:9, 22; 7:1​—Nowa anasonyeza kuti anali wolungama potsatira mosamala zonse zimene Yehova anamupempha kuti achite

    • Aro 4:1-3, 9​—Yehova anaona Abulahamu kukhala wolungama chifukwa anasonyeza kuti amamukhulupirira kwambiri

N’chifukwa chiyani chilungamo chathu chiyenera kusonyeza kuti timakonda Yehova m’malo mongofuna kudzionetsera kuti ndife olungama pamaso pa anthu?

Mt 6:1; 23:27, 28; Lu 16:14, 15; Aro 10:10

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 5:20; 15:7-9​—Yesu anauza anthu kuti asamasonyeze chilungamo chawo potengera mfundo zimene alembi ndi Afarisi ankatsatira chifukwa anali achinyengo

    • Lu 18:9-14​—Yesu ananena fanizo pofuna kudzudzula anthu amene ankafuna kudzionetsera kuti ndi olungama kwambiri kuposa anzawo

N’chifukwa chiyani kukhala wabwino kumaposa kukhala wolungama?

N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudziona ngati ndife olungama komanso kupewa kuchita zinthu modzionetsera kuti ndife olungama kwambiri kuposa ena?