Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulambira Mulungu

Kulambira Mulungu

Kodi tiyenera kulambira ndani yekha?

Eks 34:14; De 5:8-10; Yes 42:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 4:8-10​—Satana ananena kuti akhoza kupereka maufumu onse adziko lapansi kwa Yesu, koma iye anakana n’kunena kuti Yehova yekha ndi woyenera kumulambira

    • Chv 19:9, 10​—Mngelo anakana kulambiridwa ndi mtumwi Yohane

Kodi Yehova amafuna kuti tizimulambira bwanji?

Yoh 4:24; Yak 1:26, 27

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yes 1:10-17​—Yehova salola kapena kuvomereza kulambira kwa anthu achiphamaso omwe satsatira mfundo zake

    • Mt 15:1-11​—Zimene Yesu ananena zikusonyeza kuti Yehova safuna kuti tizimulambira potengera miyambo ya anthu koma tizitsatira malamulo ake

Ngati zili zotheka, kodi tiyenera kulambira Yehova pamodzi ndi ndani?

Ahe 10:24, 25

Onaninso Sl 133:1-3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 2:40-42​—M’nthawi ya Atumwi, Akhristu ankasonkhana pamodzi kuti apemphere, acheze komanso aphunzire mawu ouziridwa ndi mzimu woyera

    • 1Ak 14:26-40​—Mtumwi Paulo anapereka malangizo akuti misonkhano ya mpingo iyenera kumachitika mwadongosolo komanso izikhala yolimbikitsa n’cholinga choti anthu onse aziphunzira komanso kumvetsa zimene akuphunzitsidwa

N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti kulambira kwathu kuzikhala kovomerezeka kwa Yehova?

Mt 7:21-24; 1Yo 2:17; 5:3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ahe 11:6​—Mtumwi Paulo anafotokoza kuti tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti Yehova azivomereza kulambira kwathu

    • Yak 2:14-17, 24-26​—Yakobo, m’bale wake wa Yesu anafotokoza kuti chikhulupiriro chathu chiyenera kuyendera limodzi ndi ntchito zake; chikhulupiriro chimatithandiza kuchita zinazake