Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuleza Mtima

Kuleza Mtima

Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuleza mtima?

Aro 2:4; 9:22

Onaninso Ne 9:30

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yer 7:23-25​—Yehova anafotokoza mwachidule mmene anasonyezera kuleza mtima kwa anthu ake osamvera amene ankamuchimwira mobwerezabwereza

    • 2Pe 3:3-9, 15​—Mtumwi Petulo anafotokoza mmene Yehova anasonyezera kuleza mtima kwakukulu komanso chifukwa chake anachitira zimenezo ndipo ananena kuti kuleza mtima kwa Yehova sikudzakhala mpaka kalekale

N’chifukwa chiyani tifunika kuphunzira kuleza mtima?

Miy 25:15; Aef 4:1-3; 2Ti 2:24, 25; 4:2

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 39:19-21; 40:14, 15, 23; 41:1, 9-14​—Ngakhale kuti Yosefe anagulitsidwa monga kapolo n’kuikidwa m’ndende ku Iguputo kwa zaka zambiri, iye anapirira moleza mtima komanso anakhalabe ndi chikhulupiriro cholimba

    • Ahe 6:10-15​—Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Abulahamu pophunzitsa Akhristu kufunika kokhala oleza mtima