Kulimbikitsana
N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amafunika kulimbikitsana?
Yes 35:3, 4; Akl 3:16; 1At 5:11; Ahe 3:13
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
2Mb 32:2-8—Pamene Asuri anabwera kudzaopseza Aisiraeli, Mfumu Hezekiya inalimbikitsa anthu ake
-
Da 10:2, 8-11, 18, 19—Pamene Danieli anali wokalamba komanso wofooka, mngelo anamulimbikitsa
-
N’chifukwa chiyani Yehova amayembekezera kuti akulu azilimbikitsa anthu ena?
Onaninso Mt 11:28-30
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
De 3:28; 31:7, 8—Mogwirizana ndi malangizo ochokera kwa Yehova, mneneri Mose analimbikitsa Yoswa yemwe anali atatsala pang’ono kulowa m’malo mwake
-
Mac 11:22-26; 14:22—Mtumwi Paulo ndi Baranaba analimbikitsa Akhristu a ku Antiokeya pa nthawi ya mavuto
-
N’chifukwa chiyani tikamalimbikitsa anthu ena tiyeneranso kuwayamikira mochokera pansi pa mtima?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Owe 11:37-40—Chaka chilichonse, atsikana a mu Isiraeli ankapita kukayamikira mwana wamkazi wa Woweruza Yefita chifukwa anadzimana n’cholinga choti azitumikira panyumba ya Yehova
-
Chv 2:1-4—Ngakhale kuti Yesu anapereka malangizo kumpingo wa Akhristu a ku Efeso, anawauzanso zinthu zabwino zimene ankachita
-
Kodi atumiki a Yehova okhulupirika angalimbikitsane m’njira ziti?
Miy 15:23; Aef 4:29; Afi 1:13, 14; Akl 4:6; 1At 5:14
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
1Sa 23:16-18—Yonatani anadziwa kuti mnzake Davide akufunika kulimbikitsidwa pa nthawi yomwe anakumana ndi mavuto, choncho anamufunafuna kuti akamulimbikitse
-
Yoh 16:33—Yesu analimbikitsa ophunzira ake powakumbutsa kuti iye anagonjetsa dziko, choncho nawonso angathe kuligonjetsa ngati akutsatira chitsanzo chake
-
Mac 28:14-16—Ali pa ulendo wopita kukazengedwa mlandu ku Roma, mtumwi Paulo analimbikitsidwa ataona abale okhulupirika omwe anayenda mtunda wautali kudzakumana naye kuti akamulimbikitse
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuchita zinthu mopanda ulemu komanso kumangodandaula zilizonse?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Nu 11:10-15—Mneneri Mose anakhumudwa kwambiri chifukwa cha zinthu zoipa zimene anthu ankachita
-
Nu 13:31, 32; 14:2-6—Azondi 10 opanda chikhulupiriro atapereka lipoti loipa, anthu anafooka n’kuyamba kuukira
-
Kodi kupeza nthawi yocheza ndi abale ndi alongo anzathu kumatilimbikitsa bwanji?
Miy 27:17; Aro 1:11, 12; Ahe 10:24, 25; 12:12
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
2Mb 20:1-19—Pamene gulu la asilikali linabwera kudzaukira Yuda, Mfumu Yehosafati inaitanitsa anthu onse kuti apemphere limodzi
-
Mac 12:1-5, 12-17—Mtumwi Yakobo ataphedwa komanso mtumwi Petulo atatsekeredwa m’ndende, anthu amumpingo wa ku Yerusalemu anasonkhana pamodzi kuti apemphere
-
Kodi kuganizira zokhudza chiyembekezo chathu kumatithandiza bwanji kuti tipirire mayesero amene timakumana nawo?
Mac 5:40, 41; Aro 8:35-39; 1Ak 4:11-13; 2Ak 4:16-18; 1Pe 1:6, 7
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Ge 39:19-23; 40:1-8—Yosefe anakhalabe wokhulupirika komanso anali wofunitsitsa kuthandiza ena ngakhale kuti anaikidwa m’ndende pa mlandu womunamizira
-
2Mf 6:15-17—Mneneri Elisa sanachite mantha gulu lankhondo litawazungulira ndipo anapemphera kuti mtumiki wakenso asachite mantha
-
Baibulo lingatithandize
Kodi Yehova amatitsimikizira kuti angatithandize bwanji?
Kodi kuganizira kuleza mtima komanso chifundo cha Yehova kungatilimbikitse bwanji?
Kodi Yehova angathandize bwanji anthu amene afooka?
Sl 46:1; Yes 12:2; 40:29-31; Afi 4:13
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
1Sa 1:10, 11, 17, 18—Yehova anamvetsera pemphero la Hana ndipo anamuthandiza kuti ayambe kumva bwino pa nthawi imene anakhumudwa kwambiri
-
1Mf 19:1-19—Pamene mneneri Eliya anafooka, Yehova anamupatsa chakudya ndi madzi. Kenako, anamulimbikitsa komanso kumutonthoza pomupatsa chiyembekezo chakuti zinthu ziyenda bwino m’tsogolo
-
Kodi chiyembekezo chimene Baibulo limafotokoza chimatilimbikitsa bwanji?
2Mb 15:7; Sl 27:13, 14; Ahe 6:17-19; 12:2
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Yob 14:1, 2, 7-9, 13-15—Ngakhale kuti Yobu anadwala matenda aakulu komanso kukumana ndi mavuto osiyanasiyana, anali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova akhoza kudzamuukitsa
-
Da 12:13—Mneneri Danieli, yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka pafupifupi 100, analimbikitsidwa ndi mngelo amene anabwera kudzamuuza za madalitso omwe adzalandire m’tsogolo
-
Kodi kupemphera komanso kuganizira mozama zokhudza Yehova kungatilimbikitse bwanji?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
1Sa 30:1-9—Davide atakumana ndi mavuto, anapemphera ndipo Yehova anamupatsa mphamvu
-
Lu 22:39-43—Yesu atakumana ndi mayesero aakulu pa moyo wake, anapemphera kwambiri ndipo Yehova anamuyankha potumiza mngelo kuti adzamulimbikitse
-
Kodi mauthenga abwino amene timamva angatilimbikitse bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuuza anthu ena?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Mac 15:2-4—Mtumwi Paulo ndi Baranaba ankalimbikitsa mipingo pa nthawi imene ankaiyendera
-
3Yo 1-4—Mtumwi Yohane ali wokalamba, analimbikitsidwa kwambiri atamva kuti anthu amene anawaphunzitsa choonadi akupitirizabe kukhala okhulupirika
-