Mantha
Kuopa; mantha
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Eks 32:1-4, 21-24—Aroni anapanga fano chifukwa chochita mantha anthu atamupanikiza
Mko 14:50, 66-72—Yesu atamangidwa, atumwi onse anamuthawa chifukwa choopa anthu, nayenso Petulo anakana Khristu chifukwa cha mantha
Malemba otonthoza:
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
2Mb 20:1-17, 22-24—Mfumu Yehosafati ndi anthu ake anaopa chigulu cha adani awo chomwe chinali champhamvu, koma Yehova analimbikitsa ndi kupulumutsa atumiki ake
Lu 12:4-12—Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti sayenera kuopa anthu kapenanso kudera nkhawa ndi zimene akayankhe akuluakulu a boma chifukwa Yehova adzawathandiza