Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhawa

Nkhawa

Kodi muli ndi nkhawa chifukwa choopa mavuto monga umphawi, njala ndi kusowa pokhala?

Miy 10:15; 19:7; 30:8

Kodi muli ndi nkhawa chifukwa choopa kuti simungapeze anzanu, muzingokhala nokhanokha kapenanso simungakondedwe?

Yob 19:19; Mla 4:10, 12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 18:22; 19:9, 10​—Mneneri Eliya ankaona kuti watsala yekhayekha monga mtumiki wokhulupirika wa Yehova

    • Yer 15:16-21​—Mneneri Yeremiya ankadziona kuti ali yekhayekha pakati pa anthu omwe ankakonda kumangosangalala m’malo momvetsera uthenga wake

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

    • 1Mf 19:1-19​—Yehova anathandiza mneneri Eliya pomupatsa madzi ndi chakudya, kumumvetsera pamene ankafotokoza nkhawa zake, komanso kumulimbikitsa pomukumbutsa kuti Iye ndi wamphamvu

    • Yoh 16:32, 33​—Yesu ankadziwa kuti otsatira ake adzamusiya yekhayekha koma ankadziwanso kuti Yehova ali naye nthawi zonse