Tchimo
Kodi tchimo ndi chiyani? Nanga limatikhudza bwanji tonsefe?
Kodi Baibulo limatitsimikizira bwanji kuti tingathe kulimbana ndi chilakolako chochita zoipa?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
2Sa 11:2-5, 14, 15, 26, 27; 12:1-13—Mfumu Davide atachita machimo akuluakulu, analandira chilango champhamvu kenako anayesetsa kulapa machimo akewo
-
Aro 7:15-24—Ngakhale kuti Mtumwi Paulo anali ndi chikhulupiriro cholimba komanso wodzipereka kwa Mulungu, ankavutika ndi chilakolako chofuna kuchita zinthu zoipa
-
N’chifukwa chiyani anthu ambiri amachimwa?
Mac 3:17; 17:29, 30; 1Ti 1:13; 1Pe 1:14
Onaninso Nu 15:27-29
N’chifukwa chiyani kuchita tchimo mwadala n’koopsa kwambiri?
Onaninso Nu 15:30; Aro 1:28-32; 1Ti 5:20
Kodi Satana akhoza kugwiritsa ntchito chiyani pofuna kuyesa atumiki a Mulungu kuti achite tchimo?
Miy 1:10, 11, 15; Mt 5:28; Yak 1:14, 15
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Ge 3:1-6—Satana analankhula kudzera mwa njoka poyesa Hava kuti achite tchimo pogwiritsa ntchito chilakolako chake chadyera, ndipo zimenezi zinachititsa kuti ayambe kukayikira Yehova
-
Miy 7:6-10, 21-23—Mfumu Solomo anafotokoza zimene zinachitika kuti mnyamata wina wopanda nzeru achite tchimo lachiwerewere ndi hule
-
Kodi tingapewe bwanji misampha ya Satana?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Miy 5:1-14—Mofanana ndi mmene bambo amachitira ndi mwana wake, Mfumu Solomo anapereka malangizo abwino ochokera kwa Yehova osonyeza chifukwa chake tiyenera kupewa kuchita chiwerewere, komanso mmene tingapewere kuchita zimenezi
-
Mt 4:1-11—Yesu anagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pokana mayesero ochokera kwa Satana
-
Kodi Akhristu ayenera kupewa kuchita machimo akuluakulu ati?
Onani “Makhalidwe Oipa”
Kuulula machimo
N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyesa kubisa machimo athu?
Kodi tiyenera kuulula machimo athu kwa ndani?
Ndi ndani amene ‘amatithandiza’ pochonderera kwa Yehova m’malo mwa ife?
Kodi munthu amene wachita tchimo angasonyeze bwanji kuti walapa zenizeni?
Onaninso “Kulapa”
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Eks 22:1-12—Chilamulo cha Mose, chinkanena kuti munthu akaba azibweza kwa mwiniwake zimene wabazo
-
Lu 19:8, 9—Zakeyu yemwe anali mkulu wa okhometsa msonkho, anasonyeza kuti walapa posintha khalidwe lake komanso kubweza zonse zimene anabera anthu
-
N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova amakhululuka machimo?
Onani “Kukhululuka”
Kodi Yehova anakhazikitsa dongosolo liti pofuna kuthandiza komanso kuteteza mpingo ngati wina wachita tchimo lalikulu?
Onaninso Mac 20:28; Aga 6:1
Ngati munthu wina wachita tchimo lalikulu, kodi zingakhudze bwanji anthu ena m’banja lathu kapena mumpingo?
Onaninso De 29:18
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Yos 7:1-13, 20-26—Akani anachititsa kuti Aisiraeli onse akumane ndi mavuto chifukwa cha tchimo lalikulu limene iye anachita komanso kuyesa kulibisa
-
Yon 1:1-16—Mneneri Yona anaika pangozi moyo wa anthu omwe anali naye muchombo chifukwa sanatsatire malangizo omwe Yehova anamupatsa
-
1Ak 5:1-7—Mtumwi Paulo ananena mosabisa za tchimo lalikulu ku Korinto lomwe linkawononga mbiri ya mpingo wonse
-
N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kuti tipatsidwa chilango tikapita kwa akulu kukapempha thandizo?
N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu watikhululukira m’malo mopitiriza kudandaula za tchimo limene tinachita m’mbuyomu?
Onani “Kukhululuka”
Ngati tadziwa zoti munthu wina wachita tchimo lalikulu, n’chifukwa chiyani tiyenera kuonetsetsa kuti wochimwayo wapita kukanena kwa akulu mumpingo?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
De 13:6-9; 21:18-20—Chilamulo cha Mose chinkanena kuti munthu afunika kukanena za tchimo lalikulu ngakhale zitakhala kuti wochimwayo ndi m’bale wake kapena mnzake
-