Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Uphungu

Uphungu

Kulandira malangizo

N’chifukwa chiyani tiyenera kufufuza malangizo a m’Baibulo?

N’chifukwa chiyani ndi bwino kumvetsera malangizo m’malo modziikira kumbuyo?

Miy 12:15; 29:1

Onaninso Miy 1:23-31; 15:31

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 15:3, 9-23​—Mneneri Samueli atapereka malangizo kwa Sauli, mfumuyi inadziikira kumbuyo n’kukana malangizowo; zimenezi zinachititsa kuti Yehova amukane

    • 2Mb 25:14-16, 27​—Mfumu Amaziya anachimwa ndipo anakana malangizo othandiza ochokera kwa mneneri wa Yehova, choncho Yehova anasiya kumukonda ndi kumuteteza

N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza oyang’anira amene amatipatsa malangizo?

1At 5:12; 1Ti 5:17; Ahe 13:7, 17

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mtumwi Yohane yemwe anali wachikulire anadzudzula Diotirefe amene sankalemekeza abale amene ankatsogolera mpingo wa Chikhristu

N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera anthu achikulire?

Le 19:32; Miy 16:31

Onaninso Yob 12:12; 32:7; Tit 2:3-5

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mfumu Davide anamvera malangizo ochokera kwa Yonatani yemwe ankasiyana naye zaka 30 ndipo malangizowo anamulimbikitsa kwambiri

    • 1Mf 12:1-17​—Mfumu Rehobowamu anakana kumvera malangizo othandiza amene anthu achikulire anamupatsa ndipo anasankha kumvera malangizo ochokera kwa achinyamata anzake, pamapeto pake iye anakumana ndi mavuto aakulu

N’chiyani chikusonyeza kuti akazi okhulupirika komanso atumiki a Yehova achinyamata akhoza kupereka malangizo othandiza?

Yob 32:6, 9, 10; Miy 31:1, 10, 26; Mla 4:13

Onaninso Sl 119:100

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 25:14-35​—Abigayeli anapatsa Davide malangizo omwe anathandiza kuti Davide asaphe anthu ambiri komanso osalakwa

    • 2Sa 20:15-22​—Mayi wanzeru wamumzinda wa Abele anapereka malangizo omwe anathandiza kuti anthu onse amumzindawo asaphedwe

    • 2Mf 5:1-14​—Kamtsikana ka Chiisiraeli kanapereka malangizo omwe anathandiza kuti msilikali wamphamvu achiritsidwe ku nthenda yake ya khate

N’chifukwa chiyani sitiyenera kumvera malangizo ochokera kwa anthu amene salemekeza Yehova ndi Mawu ake?

Sl 1:1; Miy 4:14

Onaninso Lu 6:39

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mb 10:13, 14​—Mfumu Sauli anakafunsira malangizo kwa olankhula ndi mizimu m’malo mofunsira kwa Yehova ndipo anafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake

    • 2Mb 22:2-5, 9​—Mfumu Ahaziya anasankha kumvera malangizo a anthu oipa ndipo zimenezi zinachititsa kuti aphedwe

    • Yob 21:7, 14-16​—Yobu anakana kumvera malangizo olakwika a anthu amene sankalemekeza Yehova

Kupereka malangizo

N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera, kufufuza mfundo zonse komanso kumva mbali zonse zokhudzidwa tisanapereke malangizo?

Miy 18:13, 17

Onaninso Miy 25:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 1:9-16​—Mkulu wa ansembe Eli anadzudzula Hana asanamvetsere zimene akukumana nazo ndipo anachita zimenezi poganiza kuti mayi wokhulupirikayu anali ataledzera

    • Mt 16:21-23​—Mtumwi Petulo anadzudzula Yesu ndipo mosadziwa anapereka malangizo ogwirizana ndi maganizo a Satana osati a Yehova

N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera kaye kwa Yehova kuti atithandize tisanapereke malangizo?

Sl 32:8; 73:23, 24; Miy 3:5, 6

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Eks 3:13-18​—Mneneri Mose anapemphera kaye kwa Yehova kuti amuthandize kudziwa njira yabwino yoyankhira mafunso amene Aisiraeli anzake akanamufunsa

    • 1Mf 3:5-12​—Mfumu Solomo ali wachinyamata anapempha nzeru kwa Yehova m’malo modzidalira ndipo zimenezi zinachititsa kuti Yehova amudalitse

N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu popereka malangizo?

Sl 119:24, 105; Miy 19:21; 2Ti 3:16, 17

Onaninso De 17:18-20

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 4:1-11​—Poyankha mayesero a Satana, Yesu sanadalire nzeru zake koma anagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu

    • Yoh 12:49, 50​—Yesu anafotokoza kuti zimene ankaphunzitsa zinkachokera pa zimene Atate ake anamuphunzitsa ndipo chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe

N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala odekha tikamapereka malangizo komanso ngati n’zotheka, kuyamikira munthu amene tikumupatsa malangizoyo mochokera pansi pa mtima?

Aga 6:1; Akl 3:12

Onaninso Yes 9:6; 42:1-3; Mt 11:28, 29

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mb 19:2, 3​—Yehova anagwiritsa ntchito mneneri popereka malangizo kwa Mfumu Yehosafati, koma anamuyamikiranso pa zabwino zomwe anachita

    • Chv 2:1-4, 8, 9, 12-14, 18-20​—Yesu anayamikira mipingo yosiyanasiyana asanaipatse malangizo

Mkhristu wina akatidandaulira zokhudza mnzake amene wamulakwira pa nkhani zokhudza chinyengo kapena miseche, n’chifukwa chiyani ndi bwino kumulimbikitsa kuti akakambirane kaye ndi mnzakeyo pa awiri?

Ngati Mkhristu wina akuona kuti walakwiridwa, kodi tingamuthandize bwanji kukhala wachifundo, wodekha komanso wokhululuka?

Mt 18:21, 22; Mko 11:25; Lu 6:36; Aef 4:32; Akl 3:13

Onaninso Mt 6:14; 1Ak 6:1-8; 1Pe 3:8, 9

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 18:23-35​—Yesu ananena fanizo logwira mtima lofotokoza chifukwa chake timafunikira kukhululukira ena

N’chifukwa chiyani tifunika kuchita zinthu molimba mtima popereka malangizo?

Sl 141:5; Miy 17:10; 2Ak 7:8-11

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 15:23-29​—Mneneri Samueli sanalole kuopsezedwa ndi Mfumu Sauli

    • 1Mf 22:19-28​—Mneneri Mikaya sanalole kuopsezedwa kuti asatumize mauthenga ochenjeza Mfumu Ahabu, ngakhale kuti Ahabuyo ankamuzunza komanso kumuopseza

Kodi tingapereke bwanji malangizo kwa munthu wina popanda kumufooketsa mwauzimu?

Ahe 12:11-13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 22:31-34​—Ngakhale kuti Petulo ankalakwitsa zinthu zina, Yesu ankakhulupirira kuti iye angasinthe n’kupitiriza kutumikira Yehova komanso kulimbikitsa Akhristu anzake

    • Fili 21​—Mtumwi Paulo sankakayikira kuti Filimoni atsatira malangizo omwe anali ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu

Kodi tingatani kuti tizilankhula mokoma mtima tikamapereka malangizo kwa anthu amene akhumudwa kapena kufooka?

Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikupereka malangizo n’cholinga chofuna kuthandiza munthu yemwe walakwitsa?

Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikulemekeza anthu amene tikuwapatsa malangizo posatengera msinkhu, kaya ndi aamuna kapena aakazi?

N’chifukwa chiyani abusa amafunika kuchita zinthu molimba mtima ndi munthu amene akukana mobwerezabwereza kutsatira malangizo a m’Malemba?