Zikondwerero
Zikondwerero zimene Akhristu amachita nawo
Kodi ndi chikondwerero chiti chimene Akhristu anauzidwa kuti azichita?
Atumiki a Mulungu amasangalala kusonkhana pamodzi kuti alambire Yehova
Zikondwerero zimene Akhristu sachita nawo
N’chifukwa chiyani n’kulakwa kuchita nawo zikondwerero zokhudzana ndi chipembedzo chonyenga?
1Ak 10:21; 2Ak 6:14-18; Aef 5:10, 11
Onaninso “Kuphatikiza Chipembedzo Choona ndi Chonyenga”
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Eks 32:1-10—Aisiraeli anaputa mkwiyo wa Yehova pamene anasakaniza kulambira koona ndi konyenga
-
Nu 25:1-9—Yehova analanga anthu ake chifukwa chochita zachiwerewere komanso zikondwerero zokhudzana ndi kulambira konyenga
-
Kodi Akhristu ayenera kukondwerera Khirisimasi?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Lu 2:1-5—Yesu anabadwa pa nthawi ya kalembera. Pa nthawiyi, Aroma sakanakakamiza Ayuda opanduka kupita kwina chifukwa inali nyengo yozizira ndiponso yamvula
-
Lu 2:8, 12—Pamene Yesu ankabadwa, abusa ankagonera kunja komwe ankadyetsera ziweto zawo, choncho sizikanatheka kuchita zimenezi m’nyengo yozizira m’mwezi wa December
-
Kodi Akhristu ayenera kukondwerera masiku akubadwa?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Ge 40:20-22—Farao yemwe sankalambira Mulungu woona anakondwerera tsiku lake lobadwa ndipo patsikuli munthu anaphedwa
-
Mt 14:6-11—Herode Mfumu yoipa yomwe inkatsutsa otsatira a Khristu inkakondwerera tsiku lake lobadwa ndipo inalamula kuti Yohane M’batizi aphedwe
-
Zikondwerero zochokera m’Chilamulo cha Mose
Kodi Akhristu angagwiritse ntchito mfundo za m’Chilamulo cha Mose zomwe zikuphatikizapo zikondwerero zosiyanasiyana?
Onaninso Aga 4:4, 5, 9-11; Ahe 8:7-13; 9:1-3, 9, 10, 24
Kodi Akhristu ayenera kumvera lamulo lokhudza kusunga Sabata?
Onaninso Eks 31:16, 17
Zikondwerero zam’dziko lanu
Kodi Akhristu ayenera kuchita nawo zikondwerero zokumbukira zimene dziko lawo linachita?
Kodi Akhristu ayenera kuchita nawo miyambo yokumbukira nkhondo za mayiko?
Onaninso “Maboma—Akhristu Salowerera Zochitika za Dziko” ndi “Nkhondo”
Kodi Akhristu ayenera kuchita nawo miyambo yopereka ulemu wapadera kwa anthu otchuka?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Mac 12:21-23—Mulungu analanga Mfumu Herode Agiripa 1 chifukwa cholandira ulemu woyenera kupita kwa Mulungu yekha
-
Mac 14:11-15—Mtumwi Baranaba ndi Paulo anakana kulambiridwa
-
Chv 22:8, 9—Mngelo wa Yehova anakana kulambiridwa
-